Marko 6 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 6:1-56

Amupeputsa Yesu ku Nazareti

1Yesu anachoka kumeneko napita ku mudzi kwawo, pamodzi ndi ophunzira ake. 2Tsiku la Sabata litafika, anayamba kuphunzitsa mʼsunagoge, ndipo ambiri amene anamumva anadabwa.

Iwo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu anazitenga kuti zimenezi? Kodi ndi nzeru yotani imene munthu ameneyu wapatsidwa, kuti Iye akuchitanso zodabwitsa! 3Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye.

4Yesu anawawuza kuti, “Mneneri amalemekezedwa kulikonse kupatula kwawo, ndi pakati pa abale ake ndi a mʼbanja mwake.” 5Sanachite zodabwitsa kumeneko, koma anangosanjika manja pa odwala ochepa ndi kuwachiritsa. 6Ndipo Iye anadabwa chifukwa chakusowa chikhulupiriro kwawo.

Yesu Atuma Ophunzira Khumi ndi Awiri

Pamenepo Yesu anayenda mudzi ndi mudzi kuphunzitsa. 7Atayitana khumi ndi awiriwo, Iye anawatuma awiriawiri ndipo anawapatsa ulamuliro pa mizimu yoyipa.

8Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama. 9Muvale nsapato koma osatenga malaya apadera. 10Pamene mulowa mʼnyumba mukakhale momwemo kufikira mutachoka mʼmudzimo. 11Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.”

12Anatuluka kupita kukalalikira kuti anthu atembenuke mtima. 13Anatulutsa ziwanda zambiri ndi kudzoza mafuta odwala ambiri ndi kuwachiritsa.

Yohane Mʼbatizi Adulidwa Mutu

14Mfumu Herode anamva zimenezi, pakuti dzina la Yesu linali litadziwika kwambiri. Ena amati, “Yohane Mʼbatizi waukitsidwa kwa akufa, ndipo nʼchifukwa chake mphamvu zochita zodabwitsa zinkagwira ntchito mwa Iye.”

15Ena anati, “Iye ndi Eliya.”

Enanso anati, “Ndi mneneri, ofanana ndi mmodzi wa aneneri akale.”

16Koma Herode atamva zimenezi anati, “Yohane, munthu amene ndinamudula mutu, waukitsidwa kuchokera kwa akufa.”

17Pakuti Herode iye mwini analamula kuti amumange Yohane ndi kumuyika mʼndende. Anachita izi chifukwa cha Herodia, mkazi wa mʼbale wake Filipo, amene iye anamukwatira. 18Pakuti Yohane ankanena kwa Herode kuti, “Sikololedwa kwa inu kuti mukwatire mkazi wa mʼbale wanu.” 19Ndipo Herodia anamusungira Yohane chidani ndipo anafuna kumupha, koma sanathe kutero, 20chifukwa Herode anaopa Yohane ndipo anamuteteza, podziwa kuti iye anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Herode akamamva Yohane, ankathedwa nzeru; komabe amakonda kumumvetsera.

21Pomaliza mpata unapezeka. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake, Herode anakonzera phwando akuluakulu ake, akulu a ankhondo ndi anthu odziwika a mu Galileya. 22Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo.

Mfumu inati kwa mtsikanayo, “Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa.” 23Ndipo analonjeza ndi lumbiriro kuti, “Chilichonse chimene upempha ndidzakupatsa, ngakhale theka la ufumu wanga.”

24Iye anatuluka nati kwa amayi ake, “Kodi ndikapemphe chiyani?”

Iye anamuyankha kuti, “Mutu wa Yohane Mʼbatizi.”

25Nthawi yomweyo mtsikana uja anafulumira kupita komwe kunali mfumu ndi pempho lake: “Ndikufuna kuti mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”

26Mfumu inamva chisoni chachikulu, koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo ake a pa mphwandolo, sanafune kumukaniza. 27Nthawi yomweyo iye anatumiza yemwe anali ndi ulamuliro wonyonga anthu kuti abweretse mutu wa Yohane. Munthuyo anapita, nakadula mutu wa Yohane mʼndende, 28nabweretsa mutuwo mʼmbale. Anawupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anakapereka kwa amayi ake. 29Atamva izi, ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo ndi kukawuyika mʼmanda.

Yesu Adyetsa Anthu 5,000

30Atumwi anasonkhana mozungulira Yesu namufotokozera zonse zomwe anachita ndi kuphunzitsa. 31Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.”

32Ndipo anachoka okha pa bwato napita kumalo a okhaokha. 33Koma ambiri amene anawaona akuchoka anawazindikira ndipo anathamanga wapansi kuchokera mʼmidzi yonse nakayambirira kufika. 34Yesu atafika ku mtunda ndi kuona gulu lalikulu la anthu, anamva nawo chisoni chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

35Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo. 36Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye.”

37Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.”

Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?”

38Iye anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone.”

Ataona anati kwa Iye, “Asanu ndi nsomba ziwiri.”

39Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. 40Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. 41Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. 42Onse anadya ndipo anakhuta, 43ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. 44Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.

Yesu Ayenda pa Nyanja

45Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita. 46Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera.

47Pofika madzulo, bwato linali pakati pa nyanja, ndipo Iye anali yekha pa mtunda. 48Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira, 49koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, 50pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.

Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, “Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha.” 51Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri, 52popeza sanazindikire zimene zinachitika pa malofu a buledi; pakuti mitima yawo inali yowuma.

53Atawoloka, anafika ku Genesareti nayima pa dooko. 54Atangotuluka mʼbwato, anthu anamuzindikira Yesu. 55Anathamanga uku ndi uko mʼdera lonse nakanyamula odwala pa machira kupita nawo kulikonse kumene anamva kuti kuli Iye. 56Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

馬可福音 6:1-56

拿撒勒人厭棄耶穌

1耶穌帶著門徒離開那地方,回到自己的家鄉。 2到了安息日,祂開始在會堂裡教導人,眾人聽了都很驚奇,說:「這個人從哪裡學來這些本領?祂怎麼會有這種智慧?祂怎麼能行這樣的神蹟? 3這不是那個木匠嗎?祂不是瑪麗亞的兒子嗎?祂不是雅各約西猶大西門的大哥嗎?祂的妹妹們不也住在我們這裡嗎?」他們就對祂很反感。

4耶穌對他們說:「先知到處受人尊敬,只有在本鄉、本族、本家例外。」 5耶穌不能在那裡行任何神蹟,只把手按在幾個病人身上,醫治了他們。 6他們的不信令耶穌詫異,於是祂就去周圍的村莊教導人。

差遣十二使徒

7耶穌召集了十二個使徒,差遣他們兩個兩個地出去,賜給他們制伏污鬼的權柄, 8又吩咐他們除了手杖之外,不用帶食物和背囊,腰包裡也不要帶錢, 9只穿一雙鞋子和一套衣服就夠了。 10祂說:「你們無論到哪裡,就住在那些接待你們的人家裡,一直住到離開。 11如果某地方的人不接待你們,不聽你們傳的道,你們在離開之前要跺掉腳上的塵土,作為對他們的警告!」

12使徒便出去傳道,勸人悔改, 13趕出許多鬼,為許多病人抹油,治好他們。

施洗者約翰遇害

14耶穌聲名遠播,希律王也聽說了祂的事。有人說:「施洗者約翰從死裡復活了,所以能夠行這些神蹟。」

15也有人說:「祂是先知以利亞。」

還有人說:「祂是個先知,跟古代的一位先知相似。」

16希律聽到這些議論,就說:「祂一定是被我斬了頭的約翰從死裡復活了。」 17原來希律娶了他兄弟腓力的妻子希羅底,並為她的緣故而派人逮捕了約翰,把他關押在監牢裡。 18因為約翰屢次對希律說:「你娶弟弟的妻子不合法。」

19希羅底約翰懷恨在心,想要殺掉他,只是不能得逞。 20因為希律知道約翰是個公義聖潔的人,所以敬畏他,並對他加以保護。儘管約翰所講的道理令他困惑不安,他仍然喜歡聽。

21機會終於來了。希律在自己的生日那天設宴招待文武百官和加利利的顯要。 22希羅底的女兒進來跳舞,甚得希律和客人的歡心。王對她說:「你想要什麼,只管說。」 23王還對她起誓說:「無論你要什麼,哪怕是我的半壁江山,我都會給你。」

24她便出去問她母親:「我應該要什麼呢?」

她母親說:「要施洗者約翰的頭!」

25她馬上回去對王說:「願王立刻把施洗者約翰的頭放在盤子裡送給我。」

26王聽了這個請求,感到十分為難,但因為在賓客面前起了誓言,就不好拒絕。 27他立刻命令衛兵進監牢砍了約翰的頭, 28放在盤子裡送給這女子,她又轉送給她母親。 29約翰的門徒聽到這個消息,就來把約翰的屍體領回去,安葬在墳墓裡。

耶穌使五千人吃飽

30使徒們聚集在耶穌身邊,向祂報告事工和傳道的經過。 31耶穌對他們說:「你們私下跟我到僻靜的地方去歇一會兒吧。」因為當時來來往往找他們的人實在太多,他們連吃飯的時間都沒有。

32他們乘船悄悄地到了一處僻靜的地方。 33可是有許多人看見他們離開,認出了他們,便從各城鎮步行趕往那裡,比他們先到達。 34耶穌一下船,看見這一大群人好像沒有牧人的羊,心裡憐憫他們,於是教導了他們許多道理。

35天色晚了,門徒過來對耶穌說:「時候已經不早了,這裡又是荒郊野外, 36請遣散眾人,好讓他們到周圍的村莊去自己買些吃的。」

37耶穌說:「你們給他們吃的吧。」

門徒說:「我們哪來這麼多錢買東西給他們吃啊?」

38耶穌說:「看看你們有多少餅。」

他們察看後,說:「有五個餅和兩條魚。」

39耶穌吩咐門徒叫大家分組坐在草地上。 40於是眾人坐下,有的五十人一組,有的一百人一組。 41耶穌拿起那五個餅、兩條魚,舉目望著天祝謝後,掰開遞給門徒,讓他們分給眾人。祂又照樣把那兩條魚分給眾人。 42大家都吃了,並且吃飽了。 43門徒把剩下的碎餅、碎魚收拾起來,裝滿了十二個籃子。 44當時吃餅的男人有五千。

耶穌在湖面上行走

45隨後,耶穌催門徒上船,叫他們先渡到湖對岸的伯賽大,祂則遣散眾人。 46祂辭別了眾人後,就上山去禱告。 47到了晚上,門徒的船在湖中心,耶穌獨自留在岸上。 48大約凌晨三點鐘,祂看見門徒在逆風中搖櫓,非常吃力,就從水面上朝門徒走去,想要從他們旁邊經過。 49門徒看見有人在湖面上走,以為是幽靈,嚇得驚叫起來。 50全船的人看見祂,都嚇壞了,耶穌立刻對他們說:「放心吧,是我,不要怕!」

51耶穌上了船,來到他們那裡,風便停了。門徒心裡十分驚奇, 52因為他們仍然不明白耶穌分餅那件事的意義,心裡還是愚頑。 53他們渡到湖對岸,來到革尼撒勒,在那裡靠岸, 54剛一下船,眾人立刻認出了耶穌。 55他們跑遍那一帶地方,用墊子把生病的人抬來,聽到耶穌在哪裡,就把病人抬到哪裡。 56耶穌不論到哪一個城市、鄉鎮和村莊,人們總是把病人抬到街市上,求耶穌讓他們摸一摸祂衣裳的穗邊,所有摸過的病人都好了。