Marko 16 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 16:1-20

Kuuka kwa Yesu

1Litapita tsiku la Sabata, Mariya Magadalena, ndi amayi ake a Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhiritsa ndi cholinga chakuti apite akadzoze thupi la Yesu. 2Mmamawa, tsiku loyamba la Sabata, dzuwa litangotuluka kumene, anali pa ulendo wopita ku manda 3ndipo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi akatikugudubuzira mwala pa khomo la manda ndani?”

4Koma atakweza maso awo, anaona kuti mwala umene unali waukulu kwambiri wagubuduzidwa kale. 5Atalowa mʼmanda, anaona mnyamata atavala mwinjiro woyera atakhala ku mbali ya kumanja, ndipo iwo anachita mantha.

6Iye anati, “Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo. 7Koma pitani, kawuzeni ophunzira ake ndi Petro kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona Iye monga momwe anakuwuzirani.’ ”

8Akunjenjemera ndi kudabwa, amayiwo anatuluka ndipo anathawa ku mandako. Sananene china chilichonse kwa aliyense, chifukwa anachita mantha.

[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe vesi 9 mpaka 20.]

Yesu Aonekera kwa Mariya Magadalena

9Yesu atauka kwa akufa mmawa pa tsiku loyamba la Sabata, anayamba kuonekera kwa Mariya Magadalena, amene anatulutsa mwa iye ziwanda zisanu ndi ziwiri. 10Iye anapita ndi kukawawuza amene anali ndi Yesu, amene ankakhuza maliro ndi kulira. 11Atamva kuti Yesu ali moyo ndikuti amuona, iwo sanakhulupirire.

Yesu Aonekera kwa Ophunzira Awiri

12Zitatha izi Yesu anaonekera mʼmaonekedwe ena kwa awiri a iwo amene anali ku dera la ku mudzi. 13Iwo anabwerera ndi kudzawawuza enawo; koma iwo sanakhulupirirebe.

Yesu Ayankhula kwa Ophunzira Khumi ndi Mmodzi

14Pambuyo pake Yesu anaonekera kwa khumi ndi mmodziwo pamene ankadya; anawadzudzula chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kukanitsitsa kwawo kuti akhulupirire amene anamuona Iye atauka.

15Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse. 16Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa. 17Tsono zizindikiro izi zidzawatsata amene adzakhulupirira: Mʼdzina langa adzatulutsa ziwanda; adzayankhula malilime atsopano; 18adzanyamula njoka ndi manja awo; ndipo pamene adzamwa mankhwala akupha, sadzawapweteka nʼpangʼonongʼono pomwe; adzasanjika manja awo pa anthu odwala ndipo odwalawo adzachira.”

Yesu Apita Kumwamba

19Ambuye Yesu atatha kuyankhulana nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu. 20Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

马可福音 16:1-20

耶稣复活

1过了安息日,抹大拉玛丽亚雅各的母亲玛丽亚撒罗米买了香料,要去抹耶稣的遗体。 2周日清早,太阳刚刚升起,她们就去坟墓那里。 3途中她们彼此议论说:“谁能替我们滚开墓口那块大石头呢?” 4她们抬头一看,那块大石头已经滚到一旁。 5她们进了坟墓,看见一位身穿洁白长袍的青年坐在右边,吓了一跳。 6那青年对她们说:“不要害怕,你们要找那位被钉十字架的拿撒勒人耶稣吗?祂已经复活了,不在这里。你们看!这是安放祂的地方。 7你们快回去,告诉祂的门徒,特别是彼得,‘祂先你们一步去了加利利,你们将在那里见到祂,正如祂以前所说的一样。’”

8她们从坟墓出来,跑走了,战战兢兢,疑惑不已,什么也没有告诉他人,因为她们很害怕。

耶稣显现

9耶稣在周日清晨复活后,首先向抹大拉玛丽亚显现,耶稣曾在她身上赶出七个鬼。 10玛丽亚赶到门徒那里,看见他们仍然在哭泣哀悼, 11就告诉他们耶稣已经复活了,还向她显现过,但他们不相信。

12此后,有两个门徒在去乡下的路上,看到耶稣以另一种形象向他们显现。 13他们回去告诉其他的门徒,但门徒还是不相信。

最后的使命

14后来,当十一位门徒在一起吃饭的时候,耶稣向他们显现,责备他们又不信又固执,因为他们不肯相信那些人在祂复活后见过祂。 15耶稣又对他们说:“你们要到世界各地去,向全人类传扬福音。 16相信并接受洗礼的人必定得救,不肯相信的人必被定罪。 17必有神迹随着信我的人,他们能奉我的名赶鬼,说新的方言, 18又能用手拿蛇,万一喝了什么毒物,也不会受害。他们把手按在病人身上,病人就可痊愈。” 19主耶稣说完这些话,就被接回天上,坐在上帝的右边。 20门徒出去到处传扬福音,主和他们一同工作,借着神迹证实他们所传的道。