Marko 13 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Marko 13:1-37

Zizindikiro za Kutha kwa Masiku Yomaliza

1Iye atachoka mʼNyumba ya Mulungu, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Aphunzitsi taonani! Miyala ikuluikulu! Nyumba zikongolerenji!”

2Yesu anayankha kuti, “Kodi mukuziona nyumba zikuluzikuluzi? Palibe mwala ndi umodzi pano umene udzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”

3Yesu atakhala pansi pa phiri la Olivi moyangʼanana ndi Nyumba ya Mulungu, Petro, Yakobo, Yohane ndi Andreya anamufunsa Iye pambali kuti, 4“Tatiwuzani, izi zidzachitika liti? Nanga chizindikiro chakuti zatsala pangʼono kukwaniritsidwa chidzakhala chiyani?”

5Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani kuti wina asakunyengeni. 6Anthu ambiri adzabwera mʼdzina langa, nadzati, ‘Ine ndi Iyeyo,’ ndipo adzanamiza anthu ambiri. 7Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi. 8Mtundu udzawukira mtundu unzake, ndi ufumu kuwukira ufumu unzake. Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana, ndi njala. Izi ndi chiyambi chabe cha zowawa monga mayi pobereka.

9“Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine. 10Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. 11Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.

12“Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 13Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

14“Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri. 15Aliyense amene ali pa denga la nyumba yake asatsike kapena kulowa mʼnyumba kukatenga kanthu kalikonse. 16Aliyense amene ali ku munda asabwerere kukatenga mkanjo wake. 17Kudzakhala koopsa mʼmasiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! 18Pempherani kuti zimenezi zisadzachitike nthawi yozizira, 19chifukwa masiku amenewo adzakhala owawitsa osafanana ndi ena kuyambira pachiyambi, pamene Mulungu analenga dziko, kufikira lero ndipo sadzafanananso ndi ena. 20Ambuye akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwiratu, amene anawasankha, Iye anawafupikitsa. 21Pa nthawi imeneyo, ngati wina adzati kwa inu, ‘Taonani, Khristu ali kuno, kapena, Taonani, uyo ali apoyo!’ musakhulupirire. 22Pakuti akhristu onama ndi aneneri onama adzaonekera ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa kuti anyenge osankhidwiratu ngati kutakhala kotheka kutero. 23Choncho khalani tcheru; ndakuwuzani zonse nthawi isanafike.

24“Koma masiku amenewo, masautsowo atatha,

“ ‘dzuwa lidzada,

ndipo mwezi sudzawala;

25nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo,

ndipo mayiko mumlengalenga adzagwedezeka!’

26“Nthawi imeneyo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero. 27Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.

28“Tsopano phunzirani phunziro ili kuchokera ku mtengo wamkuyu. Pamene msonga za nthambi zake zikhala za nthete ndipo masamba ake ayamba kuphukira, mumadziwa kuti dzinja layandikira. 29Momwenso pamene muona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti wayandikira, ali pa khomo. 30Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika. 31Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”

Tsiku ndi Ora Sizikudziwika

32“Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha. 33Khalani maso! Khalani tcheru! Simudziwa pamene nthawi imeneyo idzafike. 34Zili ngati munthu amene akuchokapo. Amasiyira nyumba yake antchito ake, aliyense ndi ntchito yake; ndi kumuwuza wa pa khomo kuti azikhala maso.

35“Inunso muyenera kukhala maso chifukwa simukudziwa nthawi imene mwini nyumba adzabwere, kaya madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena tambala akulira, kapena mʼbandakucha. 36Ngati atabwera mwadzidzidzi, asadzakupezeni inu muli mtulo. 37Zimene ndikunena kwa inu, ndikunena kwa aliyense: ‘Khalani tcheru!’ ”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

马可福音 13:1-37

预言圣殿被毁

1耶稣走出圣殿的时候,有一个门徒对祂说:“老师,你看!这是多么大的石头,多么宏伟的建筑啊!”

2耶稣说:“你看见这宏伟的建筑了吗?将来它要被完全拆毁,找不到两块叠在一起的石头。”

3耶稣面向圣殿坐在橄榄山上,彼得雅各约翰安得烈私下来问祂: 4“请告诉我们,这些事什么时候会发生?有什么预兆?”

5耶稣对他们说:“你们要小心,免得被人迷惑。 6将有很多人冒我的名来,说,‘我是基督’,欺骗许多人。

7“你们听见战争爆发、战讯频传时,不要惊慌,因为这些事必然发生,只是末日还没有到。

8“民族将与民族互斗,国家将与国家相争,各处将有地震和饥荒。这些只是灾难13:8 灾难”希腊文是“生产之痛”。的开始。

9“你们要小心,因为你们将被送上法庭,将在会堂里受鞭打,又将为了我的缘故在官长和君王面前做见证。 10不过,福音一定要先传遍天下。 11你们被拘捕,受审讯的时候,不用预先考虑怎样辩解,到时候赐给你们什么话,你们就说什么话,因为那时候说话的不是你们自己,而是圣灵。

12“那时,人必把自己的弟兄置于死地,父亲必把儿子置于死地,儿女必反叛父母,置他们于死地。 13你们将为我的名而被众人憎恨,但坚忍到底的必定得救。

大灾难

14“当你们看见‘那带来毁灭的可憎之物’站在不当站的地方时(读者须会意),住在犹太地区的人要逃到山上去; 15在屋顶上的人不要下来,不要进房屋收拾行李; 16在田间的人不要回家取外衣。 17那时,孕妇和哺育婴儿的母亲们可就遭殃了! 18你们要祈求上帝使这些事不要在冬天发生, 19因为那是上帝创造天地以来空前绝后的大灾难。 20如果主不缩短灾期,恐怕没有人能活命,但为了祂所拣选的子民,祂已经缩短灾期。 21那时,如果有人对你们说,‘看啊!基督在这里’,或说,‘基督在那里’,你们不要相信。 22因为假基督和假先知将出现,行各种神迹奇事,如果可能,甚至会迷惑上帝拣选的子民。 23你们要小心,我已经把一切预先告诉你们了。

人子降临

24“大灾难过后,

太阳昏暗,

月亮无光,

25星宿陨落,

天体震动。

26那时,世人必看到人子驾着云、带着极大的能力和荣耀降临。 27祂必差遣天使从四面八方、天涯海角招聚祂拣选的人。

28“你们可以从无花果树学个道理。当无花果树发芽长叶的时候,你们就知道夏天快来了。 29同样,当你们看见这些事情发生时,就知道人子快来了,就在门口。 30我实在告诉你们,这个世代还没有过去,这一切都要发生。 31天地都要过去,我的话却永远长存。

32“但没有人知道那日子和时辰何时来到,连天上的天使和人子都不知道,只有天父知道。 33你们要小心,警醒祷告,因为你们不知道那日子何时来到。

34“这就好像一个人在出远门之前,把家中的事交给仆人,让他们各做各的工作,又吩咐守门的人要警醒。 35所以你们要警醒,因为你们不知道主人什么时候回来,可能是黄昏,可能是夜半,也可能是黎明或早上。 36别让他突然回来时看到你们在睡觉。 37我劝你们也劝所有的人,要警醒!”