Luka 2 – CCL & SZ-PL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 2:1-52

Kubadwa kwa Yesu

1Mʼmasiku amenewo Kaisara Augusto anapereka lamulo kuti kalembera achitike mʼdziko lonse la Aroma. 2(Uyu ndi kalembera woyamba amene anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya). 3Ndipo aliyense anapita ku mzinda wa kwawo kukalembetsa.

4Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti ku Galileya kupita ku Yudeya, ku Betelehemu ku mudzi wa Davide, chifukwa anali wa banja ndi fuko la Davide. 5Iye anapita kumeneko kukalembetsa pamodzi ndi Mariya, amene anapalana naye ubwenzi kuti akwatirane ndipo anali woyembekezera. 6Ali kumeneko, nthawi inakwana yakuti mwana abadwe, 7ndipo anabereka mwana wake woyamba, wamwamuna. Iye anamukulunga mʼnsalu ndi kumuyika modyera ngʼombe, chifukwa kunalibe malo mʼnyumba ya alendo.

Abusa ndi Angelo

8Ndipo kunali abusa amene amakhala ku dera lomwelo, kuyangʼanira ziweto zawo usiku. 9Mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iwo ndipo ulemerero wa Ambuye unawala mowazungulira. Iwo anachita mantha. 10Koma mngeloyo anawawuza kuti, “Musachite mantha. Ine ndakubweretserani Uthenga Wabwino wachimwemwe chachikulu umene udzakhala wa anthu onse. 11Lero mʼmudzi wa Davide wakubwadwirani Mpulumutsi; Iye ndi Khristu Ambuye. 12Ichi chidzakhala chizindikiro kwa inu: mukapeza mwana wakhanda wokutidwa ndi nsalu atagona modyera ngʼombe.”

13Mwadzidzidzi gulu lalikulu la angelo linaonekera pamodzi ndi mngeloyo, kuyamika Mulungu ndi kumati,

14“Ulemerero kwa Mulungu mmwambamwamba,

ndi mtendere kwa anthu pa dziko lapansi amene Iye akondwera nawo.”

15Angelowo atabwerera kumwamba, abusawo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni ku Betelehemu tikaone zinthu zomwe zachitika, zimene Ambuye atiwuza ife.”

16Ndipo iwo anafulumira nyamuka nakapeza Mariya ndi Yosefe ndi mwana wakhanda, amene anagona modyera ngʼombe. 17Pamene anamuona Iye, iwo anafotokoza zomwe anawuzidwa za mwanayo, 18ndipo onse amene anamva zimene abusawa ananena anadabwa. 19Koma Mariya anasunga zonsezi mu mtima mwake ndi kumazilingalira. 20Abusa anabwerera, akulemekeza ndi kuyamika Mulungu chifukwa cha zonse anazimva ndi kuziona, zomwe zinali monga anawuzidwira ndi angelo aja.

Yesu Aperekedwa mʼNyumba ya Mulungu

21Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, tsiku loti amuchite mdulidwe anamutcha Yesu, dzina limene mngelo anamupatsa asanabadwe.

22Nthawi yoyeretsedwa kwawo itatha, monga mwa lamulo la Mose, Yosefe ndi Mariya anapita naye ku Yerusalemu kukamupereka kwa Ambuye. 23(Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”), 24ndi kupereka nsembe posunga zimene zinanenedwa mulamulo la Ambuye: “Njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri.”

25Ndipo taonani, mu Yerusalemu munali munthu wotchedwa Simeoni, amene anali wolungama ndi wodzipereka. Iye ankadikira chitonthozo cha Israeli, ndipo Mzimu Woyera anali pa iye. 26Mzimu Woyera anamuwululira kuti sadzafa asanaone Khristu wa Ambuye. 27Motsogozedwa ndi Mzimu Woyera, iye anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Makolo ake a Yesu atabwera naye kuti achite naye mwambo malingana ndi malamulo, 28Simeoni anamunyamula mʼmanja mwake nayamika Mulungu, nati:

29“Ambuye waulamuliro, monga munalonjeza,

tsopano lolani kuti mtumiki wanu apite mu mtendere.

30Pakuti maso anga aona chipulumutso chanu,

31chimene Inu munakonza pamaso pa anthu onse,

32kuwala kowunikira anthu a mitundu ina

ndi kwa ulemerero kwa anthu anu Aisraeli.”

33Abambo ndi amayi a Mwanayo anadabwa chifukwa cha zimene zinanenedwa za Iye. 34Kenaka Simeoni anawadalitsa ndipo anati kwa Mariya amayi ake: “Mwana uyu wakonzedwa kukhala kugwa ndi kudzuka kwa ambiri mu Israeli, ndi kukhala chizindikiro chimene adzayankhula motsutsana nacho, 35kotero kuti malingaliro a mitima ya ambiri adzawululidwa. Ndipo lupanga lidzabaya moyo wakonso.”

36Panalinso mneneri wamkazi, dzina lake Ana, mwana wa Fanuelo, wa fuko la Aseri. Anali wokalamba kwambiri; anakhala ndi mwamuna wake zaka zisanu ndi ziwiri atakwatiwa, 37ndipo kenaka anakhala wamasiye mpaka pamene anali ndi zaka 84. Iye sanachoke mʼNyumba ya Mulungu koma ankapembedza usiku ndi usana, kusala kudya ndi kupemphera. 38Pa nthawiyo pamene ankapita kwa iwo, iye anayamika Mulungu ndi kuyankhula za Mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.

39Yosefe ndi Mariya atachita zonse zimene zinkafunikira ndi lamulo la Ambuye, anabwerera ku Galileya ku mudzi wa Nazareti. 40Ndipo Mwanayo anakula nakhala wamphamvu; Iye anadzazidwa ndi nzeru, ndipo chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Yesu mʼNyumba ya Mulungu

41Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska. 42Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo. 43Phwando litatha, pamene makolo ake ankabwerera kwawo, mnyamata Yesu anatsalira ku Yerusalemu, koma iwo sanadziwe zimenezi. 44Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo. 45Atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu kukamufuna. 46Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso. 47Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake. 48Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, “Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe.”

49Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?” 50Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza.

51Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo.

52Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.

Słowo Życia

Łukasza 2:1-52

Narodzenie Jezusa

1Tymczasem August, rzymski cezar, wydał dekret o powszechnym spisie ludności w swoim państwie. 2Był to pierwszy taki spis od chwili, gdy Kwiryniusz został gubernatorem Syrii. 3Wszyscy udawali się więc do swoich rodzinnych miejscowości, aby dać się tam zapisać. 4Józef musiał wyruszyć z Nazaretu w Galilei do Betlejem w Judei, rodzinnego miasta króla Dawida. Pochodził bowiem z jego rodu. 5Wybrał się więc w drogę wraz z Marią, swoją narzeczoną, która była już w zaawansowanej ciąży. 6Gdy tam dotarli, nadszedł czas porodu 7i Maria urodziła swojego pierwszego Syna. Owinęła Go w pieluszki i położyła w stajennym żłobie, gdyż nie było już dla nich miejsca w tamtejszym zajeździe.

Pasterze i aniołowie

8Tej właśnie nocy, na pobliskich łąkach pasterze pilnowali owiec. 9Nagle stanął pośród nich anioł, a wokół zajaśniała chwała Pana. Bardzo się przestraszyli, 10lecz anioł rzekł:

—Nie bójcie się! Przynoszę wam radosną nowinę, która dotyczy wszystkich ludzi. 11Dzisiaj w Betlejem narodził się Zbawiciel, długo oczekiwany Mesjasz i Pan! 12Oto jak Go rozpoznacie: Ujrzycie Niemowlę owinięte w pieluszki, leżące w żłobie.

13W tym momencie pojawiło się całe mnóstwo aniołów, którzy wielbili Boga:

14—Chwała Bogu w niebie,

a na ziemi pokój tym, których On kocha!

15Gdy aniołowie powrócili do nieba, pasterze powiedzieli:

—Chodźmy do Betlejem i zobaczmy ten cud, o którym usłyszeliśmy.

16Pobiegli do miasteczka i odnaleźli Marię z Józefem. Zobaczyli też leżące w żłobie Niemowlę. 17A wszystkim napotkanym ludziom opowiadali o tym, co przeżyli i co anioł mówił o Dziecku. 18Słuchający ich nie mogli wyjść z podziwu, 19a Maria zachowywała to wszystko w swoim sercu i wiele o tym rozmyślała. 20Pasterze zaś powrócili do swoich stad, wielbiąc Boga za to, że usłyszeli i zobaczyli dokładnie to, co im zapowiedział anioł.

Ofiarowanie Jezusa w świątyni

21Po ośmiu dniach, podczas ceremonii obrzezania, nadano Dziecku imię Jezus, zgodnie z tym, co nakazał anioł, zanim jeszcze się poczęło.

22Gdy zakończył się okres poporodowego oczyszczenia, ustalony w Prawie Mojżesza, rodzice zanieśli Jezusa do Jerozolimy, aby Go poświęcić Panu. 23W Prawie napisano bowiem: „Każdego pierwszego syna poświęcicie Panu”. 24Złożyli też ofiarę oczyszczenia, którą według Prawa mogła być para synogarlic lub dwa młode gołębie.

25A mieszkał wtedy w Jerozolimie niejaki Symeon. Był to człowiek prawy, bardzo pobożny i posłuszny Duchowi Świętemu. Nieustannie oczekiwał nadejścia upragnionego przez Żydów Mesjasza. 26Duch Święty objawił mu, że nie umrze, dopóki Go nie ujrzy. 27Tego właśnie dnia Symeon, kierowany przez Ducha, przyszedł do świątyni. Gdy więc rodzice przynieśli Jezusa, by zgodnie z Prawem poświęcić Go Panu, 28spotkali Symeona. On zaś wziął Dziecko na ręce i uwielbił Boga, mówiąc:

29—Teraz, Wszechmocny Panie,

mogę spokojnie umrzeć.

30Zobaczyłem bowiem Zbawiciela,

31którego dałeś wszystkim ludom.

32On jest światłem dla narodów

i chwałą Twojego ludu, Izraela!

33Słysząc te słowa o Jezusie, Józef i Maria zdumieli się. 34Symeon zaś pobłogosławił ich i rzekł do Marii:

—Ten Chłopiec stanie się przyczyną kontrowersji w Izraelu: jedni Go odrzucą, ściągając na siebie zgubę, a inni z radością Go przyjmą. 35W ten sposób wyjdą na jaw najskrytsze ludzkie myśli. Twoją zaś duszę przeniknie miecz cierpienia.

36Tego dnia była również w świątyni prorokini Anna, córka Fanuela, z rodu Asera. Została ona wdową po siedmiu latach małżeństwa, 37a obecnie miała już osiemdziesiąt cztery lata—była więc w podeszłym wieku. Przez cały czas nie opuszczała jednak świątyni—dniem i nocą służyła bowiem Bogu, modląc się i powstrzymując się od posiłków. 38Gdy spotkała Marię z małym Jezusem, zaczęła wychwalać Boga. Potem zaś wszystkim mieszkańcom Jerozolimy, którzy oczekiwali przyjścia Zbawiciela, mówiła, że Mesjasz już się narodził.

39Po spełnieniu wszystkich wymogów Bożego Prawa, rodzice Jezusa powrócili do rodzinnego Nazaretu w Galilei. 40Z upływem czasu Chłopiec dorastał, nabierał sił i stawał się coraz mądrzejszy, a Bóg nieustannie mu błogosławił.

Dwunastoletni Jezus w świątyni

41Jego rodzice każdego roku udawali się do Jerozolimy na święto Paschy. 42Gdy Jezus ukończył dwanaście lat, zabrali Go ze sobą. 43Po skończonych uroczystościach wszyscy udali się w drogę powrotną, ale Jezus został w Jerozolimie. Początkowo rodzice tego nie zauważyli. 44Szukali Go wśród krewnych i przyjaciół, bo sądzili, że idzie gdzieś w tłumie. 45Gdy Go nie znaleźli, wrócili do Jerozolimy, by tam kontynuować poszukiwania. 46Dopiero po trzech dniach odnaleźli Jezusa. Siedział w świątyni, w gronie nauczycieli Prawa Mojżesza. Słuchał ich i zadawał im pytania, 47a wszystkich obecnych zadziwiał swoimi wypowiedziami i mądrością. 48Rodzice byli zaskoczeni tym widokiem.

—Synu—powiedziała matka—dlaczego tak postąpiłeś? Szukaliśmy Cię z ojcem i bardzo się niepokoiliśmy.

49—Dlaczego Mnie szukaliście?—zapytał. —Nie wiedzieliście, że powinienem zajmować się sprawami mojego Ojca?

50Ale oni nie zrozumieli, co chciał przez to powiedzieć. 51Wrócił razem z nimi do Nazaretu i był im posłuszny, a Jego matka wszystko to zachowywała w swoim sercu. 52Jezus zaś rósł i nabierał mądrości, ciesząc się przychylnością Boga i ludzi.