Luka 11 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 11:1-54

Yesu Aphunzitsa za ku Pemphera

1Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”

2Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti:

“ ‘Atate,

dzina lanu lilemekezedwe,

ufumu wanu ubwere.

3Mutipatse chakudya chathu chalero,

4mutikhululukire machimo athu,

monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira.

Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ”

5Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, 6chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’

7“Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’ 8Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.

9“Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. 10Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.

11“Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? 12Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? 13Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”

Yesu ndi Belezebabu

14Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa. 15Koma ena mwa iwo anati, “Iye akutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mfumu ya ziwanda.” 16Ena anamuyesa pomufunsa chizindikiro chochokera kumwamba.

17Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka. 18Ngati Satana adziwukira yekha, ufumu wake ungalimbe bwanji? Ine ndikunena izi chifukwa inu mukuti Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu. 19Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu. 20Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu.

21“Munthu wamphamvu, amene ali ndi zida, akamalondera nyumba yake, katundu wake amatetezedwa. 22Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa namugonjetsa, amalanda zida zimene munthuyo amazidalirazo ndi kugawa katundu wake.

23“Munthu amene sali mbali yanga ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ameneyo ndi womwaza.

Za Mzimu Woyipa

24“Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’ 25Ukafika umapeza mʼnyumba mosesedwa bwino ndi mokonza. 26Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa iwowo ndipo imakalowa ndi kukhala mʼmenemo. Ndipo makhalidwe otsiriza a munthuyo amakhala oyipa kuposa oyamba aja.”

Munthu Wodala

27Pamene Yesu ankanena zonsezi, mayi wina mʼgulu la anthuwo anafuwula nati, “Ndi wodala amayi amene anakubalani ndi kukulerani!”

28Koma Yesu anayankha kuti, “Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”

Chizindikiro cha Yona

29Pamene gulu la anthu limachuluka, Yesu anati, “Uno ndi mʼbado oyipa. Umafuna kuona chizindikiro chodabwitsa. Koma sadzachiona kupatula chizindikiro chija cha Yona. 30Monga Yona uja anali chizindikiro kwa anthu ku Ninive, momwemonso Mwana wa Munthu adzakhala chizindikiro kwa anthu a mʼbado uno. 31Mfumu yayikazi yakummwera idzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi anthu a mʼbado uno ndipo idzawatsutsa, chifukwa iyo inachokera kumapeto a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomoni. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Solomoni. 32Anthu a ku Ninive adzayimirira tsiku lachiweruzo pamodzi ndi mʼbado uno ndipo adzawutsutsa, pakuti anatembenuka mtima ndi ulaliki wa Yona. Ndipo tsopano pano pali wina woposa Yona.

Nyale ndi Thupi

33“Palibe amene amayatsa nyale ndi kuyiika pa malo poti sionekera, kapena pansi pa mtsuko. Mʼmalo mwake amayika pa choyikapo chake, kuti iwo amene akulowamo aone kuwunika. 34Diso lanu ndi nyale ya thupi lanu. Pamene maso anu ali bwino, thupi lanu lonse limadzaza ndi kuwunika. Koma ngati ali oyipa, thupi lanunso ndi lodzaza ndi mdima. 35Onetsetsani tsono, kuti kuwunika kuli mwa inu si mdima. 36Choncho, ngati thupi lanu lonse ndi lodzaza ndi kuwunika, ndiye kuti palibe dera lina lili mdima, lonselo lidzakhala kuwunika, monga momwe kuwunika kwa nyale kumakuwalirani.”

Tsoka la Afarisi ndi Alembi Amalamulo

37Yesu atamaliza kuyankhula, Mfarisi wina anamuyitana kuti akadye naye. Tsono Yesu analowa mʼnyumba ndi kukhala podyera. 38Mfarisiyo anadabwa atazindikira kuti Yesu anayamba kudya wosatsata mwambo wawo wakasambidwe ka mʼmanja.

39Kenaka Ambuye anamuwuza kuti, “Inu Afarisi mumatsuka kunja kwa chikho ndi mbale, koma mʼkati mwanu ndi modzaza ndi kudzikonda ndi zoyipa. 40Anthu opusa inu! Kodi amene anapanga zamʼkati sanapangenso zakunja? 41Koma popereka kwa osauka, perekani chimene chili mʼkati ndipo chilichonse chidzakhala choyera.

42“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumapereka kwa Mulungu chakhumi cha timbewu tonunkhira, ndi timbewu tokometsera chakudya ndi mbewu zina zonse za mʼmunda, koma mumakana chilungamo ndi chikondi cha Mulungu. Mumayenera kuchita zomalizirazi osalekanso kuchita zoyambazi.

43“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malonje mʼmalo a pa msika.

44“Tsoka kwa inu Afarisi, chifukwa muli ngati manda osawaka, amene anthu amangoyendapo, osawadziwa.”

45Mmodzi mwa akatswiri a Malamulo anamuyankha Iye nati, “Aphunzitsi, pamene mukunena zinthu izi, mukutinyoza ifenso?”

46Yesu anayankha kuti, “Tsoka kwa inunso akatswiri a Malamulo chifukwa mumawalemetsa anthu ndi mtolo umene iwo sangathe kunyamula, ndipo inu eni ake simutenga chala chanu kuti muwathandize.

47“Tsoka kwa inu, chifukwa mumawaka manda a aneneri, komatu ndi makolo anu amene anawapha. 48Tsono potero mumachitira umboni za zimene makolo anu anachita. Anapha aneneri, ndipo inu mumawaka manda awo. 49Chifukwa cha ichi, Mulungu mu nzeru zake anati, ‘Ine ndidzawatumizira aneneri ndi atumwi, ena mwa iwo adzawapha ndipo ena adzawazunza.’ 50Choncho mʼbado uwu udzasenza magazi a aneneri onse amene anakhetsedwa kuyambira pachiyambi cha dziko, 51kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi.

52“Tsoka kwa inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mwachotsa kiyi wachidziwitso inu eni akenu musanalowemo, ndipo mwatsekerezanso iwo amene amalowa.”

53Pamene Yesu anachokamo, Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo anayamba kumamutsutsa koopsa ndi kumupanikiza ndi mafunso, 54pofuna kumukola muchina chilichonse chimene Iye angayankhule.

New International Reader’s Version

Luke 11:1-54

Jesus Teaches About Prayer

1One day Jesus was praying in a certain place. When he finished, one of his disciples spoke to him. “Lord,” he said, “teach us to pray, just as John taught his disciples.”

2Jesus said to them, “When you pray, this is what you should say.

“ ‘Father,

may your name be honored.

May your kingdom come.

3Give us each day our daily bread.

4Forgive us our sins,

as we also forgive everyone who sins against us.

Keep us from falling into sin when we are tempted.’ ”

5Then Jesus said to them, “Suppose you have a friend. You go to him at midnight and say, ‘Friend, lend me three loaves of bread. 6A friend of mine on a journey has come to stay with me. I have no food to give him.’ 7And suppose the one inside answers, ‘Don’t bother me. The door is already locked. My children and I are in bed. I can’t get up and give you anything.’ 8I tell you, that person will not get up. And he won’t give you bread just because he is your friend. But because you keep bothering him, he will surely get up. He will give you as much as you need.

9“So here is what I say to you. Ask, and it will be given to you. Search, and you will find. Knock, and the door will be opened to you. 10Everyone who asks will receive. The one who searches will find. And the door will be opened to the one who knocks.

11“Fathers, suppose your son asks for a fish. Which of you will give him a snake instead? 12Or suppose he asks for an egg. Which of you will give him a scorpion? 13Even though you are evil, you know how to give good gifts to your children. How much more will your Father who is in heaven give the Holy Spirit to those who ask him!”

Jesus and Beelzebul

14Jesus was driving out a demon. The man who had the demon could not speak. When the demon left, the man began to speak. The crowd was amazed. 15But some of them said, “Jesus is driving out demons by the power of Beelzebul, the prince of demons.” 16Others tested Jesus by asking for a sign from heaven.

17Jesus knew what they were thinking. So he said to them, “Any kingdom that fights against itself will be destroyed. A family that is divided against itself will fall. 18If Satan fights against himself, how can his kingdom stand? I say this because of what you claim. You say I drive out demons by the power of Beelzebul. 19Suppose I do drive out demons with Beelzebul’s help. With whose help do your followers drive them out? So then, they will be your judges. 20But suppose I drive out demons with the help of God’s powerful finger. Then God’s kingdom has come upon you.

21“When a strong man is completely armed and guards his house, what he owns is safe. 22But when someone stronger attacks, he is overpowered. The attacker takes away the armor the man had trusted in. Then he divides up what he has stolen.

23“Whoever is not with me is against me. And whoever does not gather with me scatters.

24“What happens when an evil spirit comes out of a person? It goes through dry areas looking for a place to rest. But it doesn’t find it. Then it says, ‘I will return to the house I left.’ 25When it arrives there, it finds the house swept clean and put in order. 26Then the evil spirit goes and takes seven other spirits more evil than itself. They go in and live there. That person is worse off than before.”

27As Jesus was saying these things, a woman in the crowd called out. She shouted, “Blessed is the mother who gave you birth and nursed you.”

28He replied, “Instead, blessed are those who hear God’s word and obey it.”

The Sign of Jonah

29As the crowds grew larger, Jesus spoke to them. “The people of today are evil,” he said. “They ask for a sign from God. But none will be given except the sign of Jonah. 30He was a sign from God to the people of Nineveh. In the same way, the Son of Man will be a sign from God to the people of today. 31The Queen of the South will stand up on judgment day with the people now living. And she will prove that they are guilty. She came from very far away to listen to Solomon’s wisdom. And now something more important than Solomon is here. 32The men of Nineveh will stand up on judgment day with the people now living. And the Ninevites will prove that those people are guilty. The men of Nineveh turned away from their sins when Jonah preached to them. And now something more important than Jonah is here.

The Eye Is the Lamp of the Body

33“No one lights a lamp and hides it. No one puts it under a bowl. Instead, they put a lamp on its stand. Then those who come in can see the light. 34Your eye is like a lamp for your body. Suppose your eyes are healthy. Then your whole body also is full of light. But suppose your eyes can’t see well. Then your body also is full of darkness. 35So make sure that the light inside you is not darkness. 36Suppose your whole body is full of light. And suppose no part of it is dark. Then your body will be full of light. It will be just as when a lamp shines its light on you.”

Six Warnings

37Jesus finished speaking. Then a Pharisee invited him to eat with him. So Jesus went in and took his place at the table. 38But the Pharisee was surprised. He noticed that Jesus did not wash before the meal.

39Then the Lord spoke to him. “You Pharisees clean the outside of the cup and dish,” he said. “But inside you are full of greed and evil. 40You foolish people! Didn’t the one who made the outside make the inside also? 41Give freely to poor people to show what is inside you. Then everything will be clean for you.

42“How terrible it will be for you Pharisees! You give God a tenth of your garden plants, such as mint and rue. But you have forgotten to be fair and to love God. You should have practiced the last things without failing to do the first.

43“How terrible for you Pharisees! You love the most important seats in the synagogues. You love having people greet you with respect in the market.

44“How terrible for you! You are like graves that are not marked. People walk over them without knowing it.”

45An authority on the law spoke to Jesus. He said, “Teacher, when you say things like that, you say bad things about us too.”

46Jesus replied, “How terrible for you authorities on the law! You put such heavy loads on people that they can hardly carry them. But you yourselves will not lift one finger to help them.

47“How terrible for you! You build tombs for the prophets. It was your people of long ago who killed them. 48So you show that you agree with what your people did long ago. They killed the prophets, and now you build the prophets’ tombs. 49So God in his wisdom said, ‘I will send prophets and apostles to them. They will kill some. And they will try to hurt others.’ 50So the people of today will be punished. They will pay for all the prophets’ blood spilled since the world began. 51I mean from the blood of Abel to the blood of Zechariah. He was killed between the altar and the temple. Yes, I tell you, the people of today will be punished for all these things.

52“How terrible for you authorities on the law! You have taken away the key to the door of knowledge. You yourselves have not entered. And you have stood in the way of those who were entering.”

53When Jesus went outside, the Pharisees and the teachers of the law strongly opposed him. They threw a lot of questions at him. 54They set traps for him. They wanted to catch him in something he might say.