Luka 10 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 10:1-42

Yesu Atuma Ophunzira 72

1Zitatha izi Ambuye anasankha enanso 72 ndi kuwatumiza awiriawiri patsogolo pake ku mzinda uliwonse ndi kumalo kumene Iye anatsala pangʼono kupitako. 2Iye anawawuza kuti, “Zokolola ndi zambiri, koma ogwira ntchito ndi ochepa. Pemphani Ambuye wa zokolola, kuti atumize antchito ku munda wake wa zokolola. 3Pitani! Ine ndikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. 4Musatenge chikwama kapena thumba kapena nsapato; ndipo musalonjere wina aliyense pa njira.

5“Mukamalowa mʼnyumba, poyamba nenani kuti, ‘Mtendere pa nyumba ino.’ 6Ngati mʼnyumbamo muli munthu wofuna mtendere, mtendere wanuwo udzakhala pa iyeyo; ngati mulibemo, mtendere wanuwo udzabwerera kwa inu. 7Khalani mʼnyumba yomweyo, idyani ndi kumwa chilichonse chimene akupatsani, pakuti wantchito ayenera kulandira malipiro ake. Musachoke kumene mwafikirako ndi kupita ku nyumba zina.

8“Mukamalowa mʼmudzi, ndi kulandiridwa, idyani chilichonse akukonzerani. 9Chiritsani odwala amene ali kumeneko ndipo muwawuze kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 10Koma mukalowa mʼmudzi ndipo osalandiridwa bwino, kapiteni ku misewu mʼmudzimo nʼkukanena kuti, 11‘Tikukusansirani ngakhale fumbi la mʼmudzi wanuwu limene lamamatira ku mapazi athuwa. Komabe dziwani izi: Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ 12Ine ndikuwuzani kuti adzachita chifundo polanga Sodomu pa tsikulo kusiyana ndi mudziwo.

13“Ndiwe watsoka, iwe Korazini! Ndiwe watsoka, iwe Betisaida! Kukanakhala kuti zodabwitsa zimene zinachitika mwa inu zinachitika ku Turo ndi Sidoni, iwo akanatembenuka mtima kale lomwe, atavala ziguduli ndi kudzola phulusa. 14Koma adzachita chifundo polanga Turo ndi Sidoni kusiyana ndi inu. 15Kodi iwe Kaperenawo, adzakukweza mpaka kumwamba? Ayi, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.

16“Womvera inu, akumvera Ine; wokana inu, akukana Ine. Ndipo wokana Ine; akukana Iye amene anandituma Ine.”

17Anthu 72 aja anabwerera ndi chimwemwe ndipo anati, “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera ife mʼdzina lanu.”

18Iye anayankha kuti, “Ndinaona Satana akugwa kuchokera kumwamba ngati mphenzi. 19Ine ndakupatsani ulamuliro woponda njoka ndi zinkhanira, ndi kugonjetsa mphamvu zonse za mdani; palibe chimene chidzakupwetekani. 20Komabe musakondwere chifukwa mizimu yoyipa inakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu analembedwa kumwamba.”

21Nthawi imeneyo Mzimu Woyera anadzaza Yesu ndi chimwemwe ndipo anati, “Ine ndikulemekeza Inu, Atate Ambuye a kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa mwawabisira anthu anzeru ndi ophunzira zinthu izi ndipo mwaziwulula kwa ana aangʼono. Inde, Atate, pakuti munachita zimenezi mwachifuniro chanu.

22“Atate anga anapereka zinthu zonse mʼmanja mwanga. Palibe amene amadziwa Mwana kupatula Atate yekha, ndipo palibe amene amadziwa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuwululira.”

23Kenaka anatembenukira kwa ophunzira ake nawawuza iwo okha kuti, “Ndi odala maso amene akuona zimene mukuonazi. 24Pakuti kunena zoona aneneri ambiri ndi mafumu anafunitsitsa kuona zimene mukuonazi koma sanazione, ndi kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.”

Fanizo la Msamariya Wachifundo

25Nthawi ina katswiri wa malamulo anayimirira kuti ayese Yesu. Iye anati, “Aphunzitsi, ndichite chiyani kuti ndikhale ndi moyo wosatha?”

26Yesu anayankha kuti, “Mwalembedwa chiyani mʼMalamulo, ndipo iwe umawerenga zotani?”

27Iye anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse ndi nzeru zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini.”

28Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”

29Koma iye anafuna kudzilungamitsa yekha, ndipo anamufunsanso Yesu kuti, “Kodi mnansi wanga ndani?”

30Yesu pomuyankha anati, “Munthu wina ankatsikira ku Yeriko kuchokera ku Yerusalemu. Pa njira anavulazidwa ndi achifwamba. Anamuvula zovala zake, namumenya ndi kuthawa, namusiya ali pafupi kufa. 31Wansembe ankapita pa njira yomweyo, ndipo ataona munthuyo, analambalala. 32Chimodzimodzinso, Mlevi wina pamene anafika pa malopo ndi kumuona, analambalalanso. 33Koma Msamariya wina, ali pa ulendo wake, anafika pamene panali munthuyo; ndipo atamuona, anamva naye chisoni. 34Anapita panali munthu wovulalayo, nathira mafuta ndi vinyo pa zilonda zake, nʼkuzimanga. Kenaka anamukweza pa bulu wake, napita naye ku nyumba ya alendo, namusamalira. 35Mmawa mwake anatenga ndalama ziwiri zasiliva nazipereka kwa woyangʼanira nyumbayo, nati, ‘Musamalireni munthuyu, ndipo pobwera ndidzakubwezerani zonse zimene mugwiritse ntchito.’

36“Kodi ukuganiza ndi ndani mwa atatuwa, amene anali mnansi wa munthu amene anavulazidwa ndi achifwambawo?”

37Katswiri wa Malamulo uja anayankha kuti, “Amene anamuchitira chifundo.”

Yesu anamuwuza kuti, “Pita, uzikachita chimodzimodzi.”

Marita ndi Mariya

38Yesu ndi ophunzira ake akuyenda, anafika pa mudzi kumene mayi wotchedwa Marita anamulandira Iye mʼnyumba mwake. 39Mayiyu anali ndi mchemwali wake wotchedwa Mariya, amene anakhala pa mapazi a Yesu kumverera zimene Iye ankanena. 40Koma Marita anatanganidwa ndi zokonzekera zonse zimene zimayenera kuchitika. Iye anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Ambuye, kodi simusamala kuti mchemwali wanga wandisiya kuti ndichite ntchito yonse ndekha? Muwuzeni andithandize!”

41Ambuye anati, “Marita, Marita, ukudandaula ndi kuvutika ndi zinthu zambiri, 42koma chofunika nʼchimodzi chokha. Mariya wasankha chinthu chabwino, ndipo palibe angamulande chimenechi.”

New International Reader’s Version

Luke 10:1-42

Jesus Sends Out the Seventy-Two

1After this the Lord appointed 72 others. He sent them out two by two ahead of him. They went to every town and place where he was about to go. 2He told them, “The harvest is huge, but the workers are few. So ask the Lord of the harvest to send out workers into his harvest field. 3Go! I am sending you out like lambs among wolves. 4Do not take a purse or bag or sandals. And don’t greet anyone on the road.

5“When you enter a house, first say, ‘May this house be blessed with peace.’ 6If someone there works to bring peace, your blessing of peace will rest on them. If not, it will return to you. 7Stay there, and eat and drink anything they give you. Workers are worthy of their pay. Do not move around from house to house.

8“When you enter a town and are welcomed, eat what is given to you. 9Heal the sick people who are there. Tell them, ‘God’s kingdom has come near to you.’ 10But what if you enter a town and are not welcomed? Then go into its streets and say, 11‘We wipe from our feet even the dust of your town. We do it to warn you. But here is what you can be sure of. God’s kingdom has come near.’ 12I tell you this. On judgment day it will be easier for Sodom than for that town.

13“How terrible it will be for you, Chorazin! How terrible for you, Bethsaida! Suppose the miracles done in you had been done in Tyre and Sidon. They would have turned away from their sins long ago. They would have put on the rough clothing people wear when they’re sad. They would have sat down in ashes. 14On judgment day it will be easier for Tyre and Sidon than for you. 15And what about you, Capernaum? Will you be lifted up to the heavens? No! You will go down to the place of the dead.

16“Whoever listens to you listens to me. Whoever does not accept you does not accept me. But whoever does not accept me does not accept the one who sent me.”

17The 72 returned with joy. They said, “Lord, even the demons obey us when we speak in your name.”

18Jesus replied, “I saw Satan fall like lightning from heaven. 19I have given you authority to walk all over snakes and scorpions. You will be able to destroy all the power of the enemy. Nothing will harm you. 20But do not be glad when the evil spirits obey you. Instead, be glad that your names are written in heaven.”

21At that time Jesus was full of joy through the Holy Spirit. He said, “I praise you, Father. You are Lord of heaven and earth. You have hidden these things from wise and educated people. But you have shown them to little children. Yes, Father. This is what you wanted to do.

22“My Father has given all things to me. The Father is the only one who knows who the Son is. And the only ones who know the Father are the Son and those to whom the Son chooses to make the Father known.”

23Then Jesus turned to his disciples. He said to them in private, “Blessed are the eyes that see what you see. 24I tell you, many prophets and kings wanted to see what you see. But they didn’t see it. They wanted to hear what you hear. But they didn’t hear it.”

The Story of the Good Samaritan

25One day an authority on the law stood up to test Jesus. “Teacher,” he asked, “what must I do to receive eternal life?”

26“What is written in the Law?” Jesus replied. “How do you understand it?”

27He answered, “ ‘Love the Lord your God with all your heart and with all your soul. Love him with all your strength and with all your mind.’ (Deuteronomy 6:5) And, ‘Love your neighbor as you love yourself.’ ” (Leviticus 19:18)

28“You have answered correctly,” Jesus replied. “Do that, and you will live.”

29But the man wanted to make himself look good. So he asked Jesus, “And who is my neighbor?”

30Jesus replied, “A man was going down from Jerusalem to Jericho. Robbers attacked him. They stripped off his clothes and beat him. Then they went away, leaving him almost dead. 31A priest happened to be going down that same road. When he saw the man, he passed by on the other side. 32A Levite also came by. When he saw the man, he passed by on the other side too. 33But a Samaritan came to the place where the man was. When he saw the man, he felt sorry for him. 34He went to him, poured olive oil and wine on his wounds and bandaged them. Then he put the man on his own donkey. He brought him to an inn and took care of him. 35The next day he took out two silver coins. He gave them to the owner of the inn. ‘Take care of him,’ he said. ‘When I return, I will pay you back for any extra expense you may have.’

36“Which of the three do you think was a neighbor to the man who was attacked by robbers?”

37The authority on the law replied, “The one who felt sorry for him.”

Jesus told him, “Go and do as he did.”

Jesus at the Home of Martha and Mary

38Jesus and his disciples went on their way. Jesus came to a village where a woman named Martha lived. She welcomed him into her home. 39She had a sister named Mary. Mary sat at the Lord’s feet listening to what he said. 40But Martha was busy with all the things that had to be done. She came to Jesus and said, “Lord, my sister has left me to do the work by myself. Don’t you care? Tell her to help me!”

41“Martha, Martha,” the Lord answered. “You are worried and upset about many things. 42But few things are needed. Really, only one thing is needed. Mary has chosen what is better. And it will not be taken away from her.”