Hagai 2 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hagai 2:1-23

Ulemerero wa Nyumba Yatsopano ya Yehova

1Pa tsiku la 21 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Yehova anayankhula kudzera mwa mneneri Hagai kuti: 2“Yankhula kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa anthu onse otsala. Afunse kuti, 3‘Kodi alipo amene watsala pakati panu amene anaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Nanga tsopano ikuoneka motani kwa inu? Kodi sikuoneka ngati yopanda pake kwa inu? 4Iwe Zerubabeli, limba mtima tsopano,’ akutero Yehova. ‘Limba mtima, iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe. Limbani mtima, anthu nonse a mʼdziko,’ akutero Yehova, ‘ndipo gwirani ntchito. Pakuti ine ndili nanu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 5‘Izi ndi zimene ndinapangana nanu pamene munkatuluka ku Igupto. Ndipo Mzimu wanga uli pakati panu. Musachite mantha.’

6“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakapita nthawi pangʼono ndidzagwedezanso thambo ndi dziko lapansi, nyanja ndi mtunda. 7Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo chimene mitundu yonse ya anthu imachifuna chidzabwera, ndipo ndidzaza Nyumba ino ndi ulemerero,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 8‘Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanganso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. 9‘Ulemerero wa nyumba iyi udzaposa ulemerero wa nyumba yoyamba ija,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo pamalo pano ndidzakhazikitsapo mtendere,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

Madalitso kwa Anthu Oyipitsidwa

10Chaka chachiwiri cha Dariyo, pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti: 11“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Funsa ansembe za zimene lamulo likunena: 12Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo nʼkukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, mafuta kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezo zimasanduka zopatulika?’ ”

Ansembe anayankha kuti, “Ayi.”

13Pamenepo Hagai anati, “Ngati munthu amene anayipitsidwa pokhudza mtembo akhudza chimodzi cha zinthu zimenezi, kodi chinthucho chimayipitsidwa?”

Ansembe anayankha kuti, “Inde, chimayipitsidwa.”

14Pamenepo Hagai anati, “ ‘Ndi mmene zilili ndi anthu awa ndi dziko ili pamaso panga,’ akutero Yehova. ‘Chilichonse amachita ndiponso chilichonse chimene amapereka nʼchodetsedwa.

15“ ‘Tsopano muganizire zimenezi kuyambira lero mpaka mʼtsogolo. Ganizirani momwe zinthu zinalili asanayambe kumanga nyumba ya Yehova. 16Pamene munthu ankayembekezera miyeso ya tirigu makumi awiri ankangopeza khumi yokha. Munthu akapita kuti akatunge miyeso makumi asanu ya vinyo mu mtsuko, ankangopeza miyeso makumi awiri yokha. 17Ndinawononga ntchito yonse ya manja anu ndi chinsikwi, chiwawu ndi matalala, komabe inu simunatembenukire kwa Ine,’ akutero Yehova 18‘Kuyambira lero tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi mpaka mʼtsogolo, chonde ganizirani bwino tsiku limene munayika maziko a nyumba ya Yehova. Ganizirani bwino. 19Kodi mʼnkhokwe mwatsala mbewu? Mpaka lero, mpesa ndi mtengo wa mkuyu, makangadza ndi mtengo wa olivi sizinabereke zipatso.

“ ‘Kuyambira lero mpaka mʼtsogolo ndidzakudalitsani.’ ”

Zerubabeli Mphete Yolamulira ya Yehova

20Yehova anayankhula ndi Hagai kachiwiri, pa tsiku la 24 la mwezi kuti: 21“Uza Zerubabeli, bwanamkubwa wa Yuda, kuti ndidzagwedeza thambo ndi dziko lapansi. 22Ndidzagwetsa mipando yaufumu ndi kuwononga mphamvu za maufumu achilendo. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake; akavalo ndi okwerapo ake adzagwa, aliyense adzaphedwa ndi lupanga la mʼbale wake.

23“ ‘Tsiku limenelo,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndidzakutenga, iwe mtumiki wanga Zerubabeli mwana wa Sealatieli,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakusandutsa kukhala mphete yanga yolamulira, pakuti ndasankha iwe,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

哈該書 2:1-23

對新殿的應許

1七月二十一日,耶和華對先知哈該說: 2「你去告訴撒拉鐵的兒子猶大省長所羅巴伯約撒答的兒子大祭司約書亞和所有的餘民, 3『你們當中有誰見過這殿昔日的榮耀呢?現在你們看這殿如何?看上去豈不是一文不值嗎? 4所羅巴伯啊,你要剛強,這是耶和華說的。約撒答的兒子大祭司約書亞啊,你要剛強;這地方的所有百姓啊,你們要剛強。這是耶和華說的。你們要動工,因為我與你們同在。這是萬軍之耶和華說的。 5這是你們離開埃及時我對你們的應許。不要懼怕,我的靈仍住在你們當中。

6「『萬軍之耶和華說,不久,我要再次震動天、地、海洋和旱地。 7萬軍之耶和華說,我要震動萬國,萬國的珍寶都要送到這殿,我要使這殿充滿榮耀。 8萬軍之耶和華說,金子是我的,銀子也是我的。 9萬軍之耶和華說,我要使這殿比從前更加榮耀。萬軍之耶和華說,我要在這地方賜下平安。』」

指出百姓的罪

10大流士王執政第二年九月二十四日,耶和華對先知哈該說: 11「萬軍之耶和華說,『你去問祭司, 12如果有人用衣服兜著祭肉,而衣服碰到餅、湯、酒、油或其他食物,這些被衣服碰到的食物會成為聖潔之物嗎?』」祭司們答道:「不會。」 13哈該又說:「如果因碰過屍體而變得不潔淨的人接觸這些食物,這些食物會變得不潔淨嗎?」祭司答道:「會變得不潔淨。」 14於是哈該說:「耶和華說,『這百姓和這國家在我面前也是如此。他們手中的各樣工作和他們在那裡所獻的都不潔淨。』

耶和華應許賜福

15「『從今以後,你們要回想重建耶和華殿之前的光景。 16那時,有人盼望得到二十斗穀物,卻只有十斗。有人盼望得到五十桶酒,榨酒池中卻只有二十桶。 17我曾用蟲災、黴災和冰雹毀滅你們的作物,你們仍沒有歸向我。這是耶和華說的。 18九月二十四日是我的殿奠定根基的日子。你們要思想這個日子,要認真思想。 19雖然糧倉裡沒有種子,葡萄樹、無花果樹、石榴樹和橄欖樹沒結果子,但從今以後,我要賜福給你們。』」

揀選所羅巴伯

20同一天,耶和華第二次對哈該說: 21「你告訴猶大省長所羅巴伯,『我必震動天地, 22推翻君王的寶座,消滅列國的勢力,掀翻他們的戰車和駕車的人,使戰馬跌倒、騎士自相殘殺。 23萬軍之耶和華說,我的僕人撒拉鐵的兒子所羅巴伯啊,到那日,我必使你像我蓋印的戒指,因為我揀選了你。這是萬軍之耶和華說的。』」