Genesis 36 – CCL & PCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 36:1-43

Zidzukulu za Esau

1Nazi zidzukulu za Esau amene ankatchedwanso Edomu:

2Esau anakwatira akazi atatu a ku Kanaani. Iwowa ndiwo Ada mwana wa Eloni Mhiti; Oholibama mwana wa Ana amene anali mwana wa Zibeoni Mhivi 3ndi Basemati mwana wa Ismaeli, amenenso anali mlongo wa Nabayoti.

4Ada anaberekera Esau, Elifazi; Basemati anabereka Reueli; 5ndipo Oholibama anabereka Yeusi, Yolamu ndi Kora. Amenewa anali ana a Esau amene anabadwira ku Kanaani.

6Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi ndi ena onse a pa banja pake. Anatenganso ziweto zake ndi ziweto zake zonse pamodzi ndi katundu wake yense amene anamupata ku Kanaani, ndipo anachoka ku dziko la Kanaani kupatukana ndi mʼbale wake Yakobo. 7Iwo anatero chifukwa dziko limene ankakhalamo silikanakwanira awiriwo. Iwowa anali ndi ziweto zochuluka motero kuti sakanatha kukhala pamodzi. 8Choncho Esau (amene ndi Edomu) anakakhazikika ku dziko la mapiri ku Seiri.

9Nazi zidzukulu za Esau, kholo la Aedomu amene ankakhala ku Seiri.

10Awa ndi mayina a ana aamuna a Esau:

Elifazi, mwana wa Ada, mkazi wa Esau, ndi Reueli, mwana wamwamuna wa Basemati, mkazi wa Esau.

11Awa ndi mayina a ana a Elifazi:

Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.

12Timna anali mzikazi wa Elifazi, mwana wa Esau. Iyeyo anaberekera Elifazi mwana dzina lake Amaleki. Amenewa ndiwo zidzukulu za Ada, mkazi wa Esau.

13Awa ndi ana a Reueli:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Amenewa ndi ana a Basemati, mkazi wa Esau.

14Ana aamuna a Oholibama, mkazi wa Esau, mwana wa Ana ndi mdzukulu wa Zebeoni ndi awa:

Yeusi, Yolamu ndi Kora.

15Nawa mafumu a zidzukulu za Esau:

Mwa ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau panali mafumu awa:

Temani, Omari, Zefo, ndi Kenazi, 16Kora, Gatamu, ndi Amaleki. Awa anali mafumu mwa ana a Elifazi ku Edomu ndipo onsewa anali zidzukulu za Ada.

17Mwa ana a Reueli, mwana wa Esau munali mafumu awa:

Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Awa anali mafumu mwa ana a Reueli ku Edomu. Iwowa anali zidzukulu za Basemati mkazi wa Esau.

18Mwa ana a Oholibama, mkazi wa Esau munali mafumu awa:

Yeusi, Yolamu, ndi Kora. Amenewa anali mafumu mwa ana a mkazi wa Esau, Oholibama, mwana wa Ana.

19Amenewa ndiwo zidzukulu za Esau (amene ndi Edomu) ndiponso mafumu awo.

20Awa ndi ana a Seiri Mhori, amene ankakhala mʼdzikomo:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 21Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo ana a Seiri a ku Edomu ndipo analinso mafumu a Ahori.

22Ana aamuna a Lotani anali awa:

Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.

23Ana aamuna a Sobala anali awa:

Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.

24Ana aamuna a Zibeoni anali awa:

Ayiwa ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi amoto mʼchipululu pamene ankadyetsa abulu abambo wake Zibeoni.

25Ana a Ana anali:

Disoni ndi Oholibama mwana wake wamkazi.

26Ana aamuna a Disoni anali awa:

Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani.

27Ana aamuna a Ezeri anali awa:

Bilihani, Zaavani ndi Akani.

28Ana aamuna a Disani anali awa:

Uzi ndi Arani.

29Mafumu a Ahori anali awa:

Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, 30Disoni, Ezeri ndi Disani. Amenewa ndiwo mafumu a Ahori, monga mwa mafuko awo, mʼdziko la Seiri.

Mafumu a ku Edomu

31Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:

32Bela mwana wa Beori anakhala mfumu ya ku Edomu. Mzinda wake ankawutcha Dinihaba.

33Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.

34Atafa Yobabu, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa mʼmalo mwake ngati mfumu.

35Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.

36Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka, analowa ufumu mʼmalo mwake.

37Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje, analowa ufumu mʼmalo mwake.

38Sauli atamwalira, Baala-Hanani, mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.

39Pamene Baala-Hanani mwana wa Akibori anamwalira, Hadari analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli, mwana wamkazi wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.

40Mayina a mafumu ochokera mwa zidzukulu za Esau malingana ndi mafuko awo ndi malo a fuko lililonse anali awa:

Timna, Aliva, Yeteti, 41Oholibama, Ela, Pinoni, 42Kenazi, Temani, Mibezari, 43Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu molingana ndi malo awo okhala mʼdzikomo.

Umenewu ndi mndandanda wa mʼbado wa Esau, kholo la Aedomu.

Persian Contemporary Bible

پيدايش 36:1-43

نسل عيسو

(اول تواريخ 1‏:34‏-42)

1اسامی زنان و فرزندان عيسو كه او را ادوم نيز می‌گفتند از اين قرار است:

2‏-3عيسو با سه دختر كنعانی ازدواج كرد: عاده (دختر ايلون حيتّی)، اهوليبامه (دختر عنا، نوه صبعون حّوی) و بسمه (دختر اسماعيل و خواهر نبايوت.)

4عاده، اليفاز را برای عيسو زاييد و بسمه رعوئيل را. 5اهوليبامه، يعوش و يعلام و قورح را زاييد. همهٔ پسران عيسو در سرزمين كنعان متولد شدند.

6‏-8عيسو، زنان و پسران و دختران و همهٔ اهل بيت و تمامی حيوانات و دارايی خود را كه در سرزمين كنعان به دست آورده بود، برداشت و از نزد برادرش يعقوب به كوه سعير رفت، زيرا هر دو گله‌ها و رمه‌های فراوان داشتند و زمين آنقدر بزرگ نبود كه در يكجا با هم زندگی كنند.

9‏-12اسامی ادومی‌ها يعنی نوادگان عيسو، كه از زنان او عاده و بسمه در كوهستان سعير متولد شدند، از اين قرار است:

فرزندان اليفاز پسر عاده: تيمان، اومار، صفوا، جعتام، قناز و عماليق (كه مادرش تمناع كنيز اليفاز بود). 13عيسو نوه‌های ديگری هم داشت كه فرزندان رعوئيل پسر بسمه بودند؛ اسامی آنها از اين قرار است: نحت، زارح، شمه و مزه.

14اهوليبامه، زن عيسو (دختر عنا و نوهٔ صبعون) سه پسر برای عيسو زاييد به نامهای يعوش، يعلام و قورح.

15‏-16نوه‌های عيسو سران اين قبايل شدند: تيمان، اومار، صفوا، قناز، قورح، جعتام و عماليق. قبايل نامبرده فرزندان اليفاز پسر ارشد عيسو و همسرش عاده بودند.

17سران اين قبايل فرزندان رعوئيل پسر عيسو از همسرش بسمه بودند: نحت، زارح، شمه و مزه.

18‏-19سران اين قبايل پسران عيسو از همسرش اهوليبامه بودند: يعوش، يعلام و قورح.

20‏-21قبايلی كه از نسل سعير حوری، يكی از خانواده‌های ساكن سرزمين سعير، به وجود آمدند عبارتند از: لوطان، شوبال، صبعون، عنا، ديشون، ايصر و ديشان.

22‏-28حوری و هومام فرزندان لوطان بودند. لوطان خواهری داشت به نام تمناع. فرزندان شوبال: علوان، مناحت، عيبال، شفو و اونام. فرزندان صبعون: ايّه و عنا (عنا همان پسری بود كه موقع چرانيدن الاغهای پدرش چشمه‌های آب گرم را در صحرا يافت). فرزندان عنا: ديشون و اهوليبامه. فرزندان ديشون: حمدان، اشبان، يتران و كران. فرزندان ايصر: بلهان، زعوان و عقان. فرزندان ديشان: عوص و اران.

29‏-30اسامی سران قبايل حوری كه در سرزمين سعير بودند عبارتند از: لوطان، شوبال، صبعون، عنا، ديشون، ايصر و ديشان.

پادشاهان ادوم

(اول تواريخ 1‏:43‏-54)

31‏-39پيش از اين كه در اسرائيل پادشاهی روی كار آيد، در سرزمين ادوم اين پادشاهان يكی پس از ديگری به سلطنت رسيدند:

بالع، پسر بعور اهل دينهابه واقع در ادوم.

يوباب، پسر زارح از شهر بصره.

حوشام، از سرزمين تيمانی‌ها.

حداد، پسر بداد. او لشكر مديانی‌ها را در سرزمين موآب شكست داد. نام شهر او عويت بود.

سمله، از اهالی مسريقه.

شائول، اهل رحوبوت كه در كنار رودخانه‌ای واقع بود.

بعل حانان، پسر عكبور.

حداد، از اهالی فاعو كه نام زنش مهيطب‌ئيل دختر مطرد و نوهٔ ميذهب بود.

40‏-43اين قبايل از عيسو به وجود آمدند: تمناع، علوه، يتيت، اهوليبامه، ايله، فينون، قناز، تيمان، مبصار، مجدی‌ئيل و عيرام. همهٔ اينها ادومی بودند و هر يک نام خود را بر ناحيه‌ای كه در آن ساكن بودند نهادند.