Genesis 32 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 32:1-32

Yakobo Akonzekera Kukumana ndi Esau

1Nayenso Yakobo analowera njira yake, ndipo angelo a Mulungu anakumana naye. 2Pamene Yakobo anawaona anati, “Ili ndi gulu la Mulungu.” Choncho anawatcha malowo Mahanaimu.

3Yakobo anatumiza amithenga ake kwa mʼbale wake Esau ku dera la Seiri, dziko la Edomu. 4Anawalangiza kuti, “Zimene mukanene ndi izi kwa mbuye wanga Esau: ‘Mtumiki wanu Yakobo akuti, Ine ndakhala ndi kukhala ndi Labani mpaka tsopano. 5Ndili ndi ngʼombe, abulu, nkhosa ndi mbuzi, antchito aamuna ndi aakazi. Tsopano ndikutumiza mawu amenewa kwa mbuye wanga, kuti mundikomere mtima.’ ”

6Pamene amithenga aja anabwerera kwa Yakobo, anati, “Tinapita kwa mʼbale wanu Esau, ndipo tsopano iye akubwera kudzakumana nanu. Ali ndi anthu 400.”

7Yakobo anali ndi mantha ndi nkhawa yayikulu kwambiri. Tsono anagawa anthu onse amene anali naye, ndiponso nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi ngamira mʼmagulu awiri. 8Mʼmaganizo ake iye ankanena kuti, “Ngati Esau atabwera ndi kuthira nkhondo gulu limodzi, gulu lina lotsalalo likhoza kupulumuka.”

9Pamenepo Yakobo anapemphera, “Haa, Mulungu wa kholo langa Abrahamu, Mulungu wa abambo anga Isake, Aa Yehova amene munati kwa ine, ‘Bwerera ku dziko la kwanu ndi kwa abale ako, ndipo ndidzakuchitira zabwino.’ 10Ine siwoyenera kulandira kukoma mtima kwanu ndi kukhulupirika kwanu kumene mwaonetsa wantchito wanu. Ndinali ndi ndodo yokha pamene ndinawoloka Yorodani uyu koma tsopano ndili ndi magulu awiri. 11Ndipulumutseni mʼdzanja la mʼbale wanga Esau, popeza ndikuopa kuti mwina akubwera kudzandithira nkhondo pamodzi ndi akazi ndi ana omwe. 12Paja Inu munandilonjeza kuti simudzalephera kundichitira zabwino ndi kuti zidzukulu zanga zidzakhala zosawerengeka ngati mchenga wa ku nyanja.”

13Iye anagona pomwepo usiku umenewo. Pambuyo pake anasankhula pa chuma chimene anali nacho zinthu izi ngati mphatso za Esau, mʼbale wake: 14Anasankhula mbuzi zazikazi 200 ndi atonde makumi awiri, nkhosa zazikazi 200 ndi nkhosa zazimuna makumi awiri, 15ngamira za mkaka 30 ndi ana awo, ngʼombe zazikazi 40 ndi zazimuna khumi, ndipo abulu aakazi makumi awiri ndi abulu aamuna khumi. 16Iye anazipereka kwa antchito ake kuti azikuse, gulu lililonse pa lokha, ndipo anati kwa antchito akewo, “Tsogolani ndipo muonetsetse kuti pali mpata pakati pa gulu ndi gulu linzake.”

17Anawuza mnyamata wa gulu loyamba kuti, “Ngati ukumana naye mʼbale wanga Esau nakufunsa kuti, ‘Ndinu antchito a yani, ndipo mukupita kuti? Nanga ziweto zonse zili patsogolo pakozi ndi za yani?’ 18Pamenepo ukayankhe kuti, ‘Zimenezi ndi za wantchito wanu, Yakobo, ndipo wazipereka kwa inu, Esau, mbuye wake ngati mphatso. Mtumiki wanuyu akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ”

19Anawuza mawu omwewo kwa wachiwiri, wachitatu ndi ena onse amene ankayenda motsogoza ziwetozo kuti, “Inunso munene zomwezo kwa Esau mukakumana naye. 20Muzikanena kuti, ‘Wantchito wanu Yakobo akubwera mʼmbuyo mwathumu.’ ” Popeza anaganiza kuti, “Ndidzamutsitsa mtima ndi mphatso ndazitsogozazi. Apo tsono ndikadzakumana naye, mwina adzandilandira bwino.” 21Choncho mphatso za Yakobo zinatsogola, koma iye mwini anagona pa msasa pomwepo usiku umenewo.

Yakobo Alimbana ndi Mulungu

22Usiku umenewo Yakobo anauka natenga akazi ake awiri, antchito ake awiri ndi ana ake aamuna khumi ndi mmodzi nawoloka pa dooko la mtsinje wa Yaboki. 23Atatha kuwawolotsa pa mtsinjewo anawolotsanso katundu wake yense. 24Tsono Yakobo anatsala yekha. Tsono munthu wina anadzalimbana naye mpaka mʼmbandakucha. 25Pamene munthuyo anaona kuti sangathe kumugonjetsa, anakhudza nyungʼunyu ya pa ntchafu ya Yakobo ndipo inaguluka polimbanapo. 26Kenaka munthuyo anati, “Ndisiye ndizipita, popeza kunja kukucha.”

Koma Yakobo anayankha, “Sindikulolani kupita pokhapokha mutandidalitsa.”

27Munthu uja anamufunsa Yakobo kuti, “Kodi dzina lako ndiwe yani?”

Iye anayankha, “Ndine Yakobo.”

28Pamenepo munthuyo anati, “Dzina lako silidzakhalanso Yakobo koma Israeli, chifukwa walimbana ndi Mulungu ndi anthu ndipo wapambana.”

29Yakobo anati, “Chonde, uzeni dzina lanu.”

Koma munthuyo anati, “Chifukwa chiyani ukundifunsa dzina?” Kenaka anamudalitsa pomwepo.

30Choncho Yakobo anawatcha malowo Penueli, popeza anati, “Ndinaonana ndi Mulungu maso ndi maso koma sindinafe.”

31Dzuwa linamutulukira Yakobo pamene amachoka pa Penueli. Tsono ankayenda chotsimphina chifukwa cha nyungʼunyu yake ija. 32Nʼchifukwa chake mpaka lero Aisraeli sadya nyama ya pa nyungʼunyu chifukwa Yakobo anakhudzidwa pa nyungʼunyu.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

創世記 32:1-32

雅各預備見以掃

1雅各繼續前行,遇見了上帝的天使。 2雅各看見他們,就說:「這是上帝的軍隊!」於是稱那地方為瑪哈念32·2 瑪哈念」意思是「兩營軍隊」。

3雅各先派人到西珥,就是以東,去見他哥哥以掃4並吩咐他們:「你們要這樣對我主以掃說,『你僕人雅各一直寄居在拉班家裡, 5現在他帶了牛羊、驢和僕婢回來見你,派我們來報信,希望得到你的恩待。』」

6報信的人回到雅各那裡,說:「我們到了你哥哥以掃那裡,他正帶著四百人前來見你。」 7雅各聽了非常害怕,便把隨從、牛群、羊群和駱駝分成兩隊, 8心想:「如果以掃來攻擊一隊,另一隊還可以逃生。」

9他禱告說:「耶和華,我祖父亞伯拉罕和我父親以撒的上帝啊!你吩咐我回到家鄉和親族那裡,答應厚待我。 10我不配蒙你以慈愛和信實相待,我先前過約旦河的時候,手上只有一根杖,現在卻有兩隊人丁家畜。 11求你救我脫離我哥哥以掃的手,我怕他會來殺我和我的妻兒。 12然而,你曾說,『我必厚待你,使你的後代多如海沙,不可勝數。』」

13那天晚上,雅各就在那裡過夜,又挑選牲畜送給哥哥以掃作禮物: 14母山羊二百隻、公山羊二十隻、母綿羊二百隻、公綿羊二十隻、 15哺乳的駱駝三十頭及其小駱駝、母牛四十頭、公牛十頭、母驢二十頭、驢駒十頭。 16雅各把牲畜每類分成一群,交給僕人看管,對他們說:「你們走在前頭,每群牲畜之間要保持一段距離!」 17又吩咐走在最前面的僕人說:「我哥哥以掃遇到你的時候,如果問你是誰家的人?要到哪裡去?前頭這些牲畜是誰的? 18你就說,『是僕人雅各要送給他主人以掃的禮物,他自己就跟在後面。』」 19雅各又吩咐看管第二群、第三群及其餘牲畜的僕人遇見以掃時也要這樣回答, 20並且一定要說:「你僕人雅各就在後面。」雅各想先用禮物去化解以掃的怨恨,或許見面時以掃會善待他。 21於是,他派人先把禮物送過去,自己則留在營裡過夜。

雅各遇見上帝

22那天晚上,雅各起來帶著兩個妻子、兩個婢女和十一個兒子渡過雅博渡口。 23雅各把他們連同一切所有都送過河以後, 24自己獨自留下。這時,有一個人來和他摔跤,直到黎明。 25那人見勝不過雅各,就在他的大腿窩摸了一下,他大腿的關節就脫了臼。 26那人說:「天亮了,讓我走吧!」但雅各說:「你不祝福我,我就不讓你走。」 27那人問道:「你叫什麼名字?」他說:「我叫雅各。」 28那人說:「你以後不要再叫雅各了,你要叫以色列,因為你跟上帝和人角力都得勝了。」

29雅各說:「請你告訴我你的名字。」那人說:「你為什麼問我的名字?」他就在那裡給雅各祝福。 30雅各稱那地方為毗努伊勒,因為他說:「我當面見過上帝,竟能活命。」 31雅各經過毗努伊勒的時候,太陽出來了,那時他的大腿瘸了。 32以色列人至今都不吃大腿窩的筋,因為那人摸過雅各大腿窩的筋。