Genesis 24 – CCL & PCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 24:1-67

Isake ndi Rebeka

1Tsopano Abrahamu anali atakalamba kwambiri, ndipo Yehova anamudalitsa mu zonse anachita. 2Tsiku lina Abrahamu anawuza wantchito wake wamkulu amene ankayangʼanira zonse anali nazo, kuti “Ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga. 3Ndikufuna kuti ulumbire pamaso pa Yehova, Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi, kuti sudzamupezera mwana wanga mkazi pakati pa atsikana Achikanaani a kuno kumene ndikukhala, 4koma kuti udzapita ku dziko la kwathu ndi kukamupezera mkazi mwana wanga Isake pakati pa abale anga.”

5Wantchito uja anafunsa kuti, “Nanga atakhala kuti mkaziyo sakufuna kubwera nane kuno? Kodi ine ndingadzatenge mwana wanu ndi kubwerera naye ku dziko kumene munachokera?”

6Abrahamu anati, “Uwonetsetse kuti usadzabwerere naye mwana wanga kumeneko. 7Yehova Mulungu wakumwamba amene ananditenga kwa makolo anga nanditulutsa mʼdziko lobadwira, ameneyo anayankhula nane molumbira kuti, ‘Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko ili.’ Iyeyu adzatumiza mngelo wake kuti akutsogolere kumeneko kukapezera mwana wanga mkazi. 8Ngati mkaziyo adzakana kubwerera nawe ndiye kuti udzakhala womasuka ku lumbiro langa. Koma usadzamutenge mwana wanga ndi kubwerera naye kumeneko.” 9Choncho wantchitoyo anayika dzanja lake pansi pa ntchafu ya mbuye wake Abrahamu nalumbira kwa iye kuti adzachitadi monga mwa mawu a Abrahamu.

10Tsono wantchito uja anatengapo ngamira khumi mwa ngamira za mbuye wake pamodzi ndi zinthu zabwino za mitundumitundu. Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda wa Nahori, mʼdziko la Mesopotamiya. 11Atafika, anagwaditsa pansi ngamira zija pafupi ndi chitsime chimene chinali kunja kwa mzinda uja. Awa anali madzulo ndithu, nthawi imene amayi amapita kukatunga madzi.

12Ndipo wantchito uja anapemphera nati, “Haa, Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, mulole kuti zinthu zindiyendere ine lero, ndipo muonetseni mbuye wanga Abrahamu kukoma mtima kwanu kosasinthika. 13Taonani ndayima pambali pa chitsimechi, ndipo atsikana a mu mzindawu akubwera kudzatunga madzi. 14Ine ndipempha mtsikana wina kuti, ‘Chonde tula mtsuko wako kuti ndimweko madzi.’ Tsono iye akayankha kuti ‘Imwani,’ ndipo ndidzapatsanso ngamira zanu madziwo, ameneyo akhale mkazi amene mwasankhira mtumiki wanu Isake.” Zimenezi zikachitika, ndidzadziwa kuti mwaonetsadi kukoma mtima kwanu kosasinthika kwa mbuye wanga.

15Asanatsirize kupemphera, anangoona Rebeka watulukira atasenza mtsuko wake pa phewa. Iyeyu anali mwana wa Betueli mwana wa Milika, mkazi wa Nahori mʼbale wake wa Abrahamu. 16Mtsikanayo anali wokongola kwambiri, namwali amene sanadziwe mwamuna. Iye anatsikira ku chitsime nadzaza mtsuko nakweranso ku mtunda.

17Wantchito uja anathamanga kukakumana naye nati, “Chonde patseko madzi pangʼono a mu mtsuko wakowo kuti ndimwe.”

18Mtsikanayo anati, “Imwani mbuye wanga.” Ndipo mofulumira anatsitsa mtsuko uja nawuyika mʼmanja ndi kumupatsa kuti amwe.

19Atatha kupereka madzi akumwa kwa mlendo uja, mtsikanayo anati, “Ndikatungiranso ngamira madzi kuti zimwe mpaka zitakwana.” 20Choncho anafulumira kukhuthula madzi a mu mtsuko aja momwera ziweto, nathamanga kubwerera ku chitsime kukatunga madzi ena, ndipo anatunga okwanira ngamira zake zonse. 21Modekha, munthu uja anayangʼanitsitsa kwambiri mtsikana uja kuti adziwedi ngati Yehova anamutsogolera pa ulendo wake uja kapena ayi.

22Ngamira zija zitatha kumwa, mlendo uja anatulutsa chipini chagolide cholemera theka la sekeli ndi zibangiri zagolide ziwiri zolemera masekeli 100. 23Kenaka anafunsa namwaliyo kuti, “Chonde tandiwuza, kodi ndiwe mwana wa yani? Ndipo kodi malo alipo kwanu woti ife nʼkugona?”

24Anamuyankha kuti, “Ine ndine mwana wa Betueli, mwana amene Milika anaberekera Nahori.” 25Ndipo anapitiriza kunena kuti, “Chakudya chodyetsa nyamazi chilipo kwathu ndipo malo woti mugone aliponso.”

26Kenaka munthuyo anawerama pansi napembedza Yehova, 27nati, “Alemekezeke Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene waonetsa kukoma mtima kwake kosasintha ndi kukhulupirika kwake kwa mbuye wanga. Yehova wanditsogolera pa ulendo wanga mpaka ndafika ku nyumba kwa abale ake a mbuye wanga.”

28Mtsikana uja anathamanga nakafotokozera zimenezi anthu a kwa amayi ake. 29Tsono Rebeka anali ndi mlongo wake dzina lake Labani. 30Iyeyu atangoona chipini pa mphuno ndi zibangiri pa mikono ya mlongo wake komanso kumva zimene mlendo uja ananena kwa Rebekayo, anathamangira kwa mlendo uja, ndipo anamupeza atangoyima ndi ngamira zake pafupi ndi chitsime. 31Iye anati, “Tiyeni kwathu, ndinu munthu amene Yehova wamudalitsa. Bwanji mwangoyimirira panja pano? Ine ndakukonzerani malo ogona inu ndi ngamira zanu.”

32Choncho munthu uja analowa mʼnyumba. Labani anatsitsa katundu anali pa ngamira uja. Kenaka anazipatsa ngamira zija chakudya, ndiponso anapereka madzi wosamba mapazi kwa mlendo uja ndi anthu ena onse. 33Chakudya chitabwera mlendo uja anati, “Sindidya mpaka nditakuwuzani zimene ndadzera kuno.”

Labani anati, “Yankhulani.”

34Motero iye anati, “Ine ndine wantchito wa Abrahamu. 35Yehova wadalitsa mbuye wanga kwambiri, ndiponso walemera. Wamupatsa nkhosa ndi ngʼombe, siliva ndi golide, antchito aamuna ndi antchito aakazi, komanso ngamira ndi abulu. 36Sara, mkazi wa mbuye wanga anamubalira iye mwana wamwamuna ngakhale kuti Sarayo anali wokalamba. Tsono mbuye wanga wamupatsa mwanayo chuma chonse. 37Tsono mbuye wanga anandilumbiritsa kuti ndisunge mawu ake akuti, ‘Usadzamupezere mwana wanga mkazi kuchokera mwa atsikana a dziko lino la Kanaani, 38koma upite ku banja la abambo anga ndi kwa abale anga kuti ukamupezere mkazi mwana wanga.’ ”

39“Ndipo ine ndinati kwa mbuye wanga, ‘Nanga mkaziyo akakapanda kubwera nane pamodzi?’

40“Iye anayankha, ‘Yehova amene ndakhala ndikumumvera nthawi zonse, adzatumiza mngelo wake kuti akuperekeze ndipo adzakuthandiza mpaka ukamupezere mwana wanga mkazi kuchokera ku mtundu wanga, wa fuko langa. 41Ukadzachita zimenezi udzakhala mfulu wosamangidwa ndi lumbiro langali. Koma tsono ukadzafika kwa fuko langa, ndipo ngati sadzalola kukupatsa mbeta ya mwana wanga, aponso udzamasuka ku lumbiro langali.’ ”

42“Tsono lero lino pamene ndafika pa chitsime, ndinapempha kuti, ‘Yehova, Mulungu wa mbuye wanga, Abrahamu, ngati Inu mwandidalitsadi pa ulendowu, 43taonani ndayima pambali pa chitsime ichi; ndipo ndidzati kwa namwali amene atabwere kudzatunga kuti, chonde nditamwako madzi a mu mtsuko wakowu,’ 44ndipo ngati adzandiyankha kuti, ‘Imwani ndipo ndizimwetsanso madzi ngamira zanuzi,’ ameneyo akhale yemwe Yehova wamusankhira mwana wa mbuye wanga.”

45“Ndisanatsirize kupemphera, ndinangoona Rebeka akutulukira mtsuko wake uli pa phewa. Anatsetserekera ku chitsime kukatunga madzi ndipo ndinati kwa iye, ‘Chonde patseko madzi akumwa.’

46“Mofulumira, anatsitsa mtsuko wake pa phewa pake nati, ‘Imwani ndiponso ndizimwetsa madzi ngamira zanuzi.’ Kotero ine ndinamwa ndipo anamwetsanso ngamirazo.

47“Ndinamufunsa kuti, ‘Ndiwe mwana wa yani?’

“Iye anati, ‘Ndine mwana wa Betueli mwana wa Nahori, amene Milika anamuberekera.’

“Tsono ndinayika chipini pa mphuno yake ndi kumveka zibangiri mʼmikono yake, 48kenaka ndinawerama pansi ndi kupembedza Yehova. Ndipo ndinatamanda Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abrahamu, amene anandilondolera mokhulupirika njira yanga. Iye wandifikitsa kwa mʼbale wake kumene ndapezera mbeta mwana wa mbuye wanga. 49Tsono ngati mukufuna kuonetsa kukoma mtima kwanu kwa mbuye wanga, ndikuonetsa kukhulupirika kwanu, ndiwuzeni; ndipo ngati si choncho ndiwuzeninso kuti ndidziwe chochita.”

50Labani ndi Betueli anayankha nati, “Izi ndi zochokera kwa Yehova, ndipo ife sitinganenepo kanthu. 51Nayu Rebeka, mutengeni muzipita naye kuti akakhale mkazi wa mwana wa mbuye wanu, monga Yehova wanenera.”

52Wantchito wa Abrahamu uja atamva zimene anawerama pansi pamaso pa Yehova. 53Kenaka wantchitoyo anatulutsa ziwiya zagolide ndi zasiliva ndi zovala nazipereka kwa Rebeka. Anaperekanso mphatso zina za mtengowapatali kwa mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka. 54Tsono wantchito uja ndi anthu amene anali naye anadya, kumwa nagona komweko.

Kutacha mmawa wake, wantchito uja anati, “Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.”

55Koma mlongo wake ndi amayi ake a Rebeka anayankha kuti, “Muloleni mtsikanayu abakhala nafe masiku khumi kapena kupyolerapo, kenaka mukhoza kupita.”

56Koma iye anawawuza kuti, “Chonde musandichedwetse. Yehova wandithandiza kale pa ulendo wanga. Mundilole ndibwerere kwa mbuye wanga.”

57Koma iwo anati, “Bwanji timuyitane mtsikanayo ndipo timufunse ngati afuna kupita nanu panopa.” 58Choncho iwo anamuyitana Rebeka uja namufunsa kuti, “Kodi ukufuna kupita ndi munthuyu panopa?”

Iye anayankha kuti, “Ndipita.”

59Kotero anamulola Rebeka pamodzi ndi mlezi wake kuti apite ndi wantchito wa Abrahamu pamodzi ndi anthu amene anali naye. 60Ndipo iwo anadalitsa Rebeka ndi kumuwuza kuti,

“Iwe ndiwe mlongo wathu, Mulungu akudalitse iwe, ukhale

mayi wa anthu miyandamiyanda;

ndi kuti zidzukulu zako zidzalanda

mizinda ya adani awo.”

61Kenaka Rebeka ndi antchito ake ananyamuka kukakwera ngamira zawo ndipo anapita naye pamodzi munthu uja. Choncho wantchito uja anatenga Rebeka nʼkumapita.

62Pa nthawiyi nʼkuti Isake atafika kuchokera ku chitsime cha Wamoyo Wondipenya (Beeri-lahai-roi), popeza tsopano ankakhala ku Negevi. 63Tsiku lina chakumadzulo, Isake anatuluka kukayendayenda ku munda, ndipo atakweza maso anaona ngamira zikubwera. 64Rebeka nayenso anatukula maso naona Isake. Ndipo anatsika pa ngamira yake 65nafunsa wantchito uja kuti, “Kodi munthu uyo ndi ndani akuyenda mʼmundamo kubwera kudzakumana nafe?”

Wantchitoyo anayankha, “Ndiye mbuye wanga.” Choncho Rebeka anatenga nsalu ndi kufunda kumaso.

66Tsono wantchito uja anawuza Isake zonse zimene anazichita. 67Isake analowa naye Rebeka mu tenti ya amayi ake Sara, ndipo anakhala mkazi wake. Isake anamukonda kwambiri Rebeka mkazi wake motero kuti zimenezi zinamutonthoza imfa ya amayi ake.

Persian Contemporary Bible

پيدايش 24:1-67

اسحاق و ربكا

1ابراهيم اكنون مردی بود بسيار سالخورده و خداوند او را از هر لحاظ بركت داده بود. 2‏-3روزی ابراهيم به ناظر خانهٔ خود كه رئيس نوكرانش بود، گفت: «دستت را زير ران من بگذار و به خداوند، خدای آسمان و زمين قسم بخور كه نگذاری پسرم با يكی از دختران كنعانی اينجا ازدواج كند. 4به زادگاهم نزد خويشاوندانم برو و در آنجا برای اسحاق همسری انتخاب كن.»

5ناظر پرسيد: «اگر هيچ دختری حاضر نشد زادگاه خود را ترک كند و به اين ديار بيايد، آن وقت چه؟ در آن صورت آيا اسحاق را به آنجا ببرم؟»

6ابراهيم در جواب گفت: «نه، چنين مكن! 7خداوند، خدای قادر متعال، به من فرمود كه ولايت و خانه پدری‌ام را ترک كنم و وعده داد كه اين سرزمين را به من و به فرزندانم به مِلكيت خواهد بخشيد. پس خودِ خداوند فرشتهٔ خود را پيش روی تو خواهد فرستاد و ترتيبی خواهد داد كه در آنجا همسری برای پسرم اسحاق بيابی و همراه خود بياوری. 8اما اگر آن دختر نخواست بيايد، تو از اين قسم آزاد هستی. ولی به هيچ وجه نبايد پسرم را به آنجا ببری.»

9پس ناظر دستش را زير ران سَرور خود ابراهيم گذاشت و قسم خورد كه مطابق دستور او عمل كند.

10او با ده شتر از شتران ابراهيم و مقداری هدايا از اموالِ او به سوی شمالِ بين‌النهرين، به شهری كه ناحور در آن زندگی می‌كرد، رهسپار شد. 11وقتی به مقصد رسيد، شترها را در خارج شهر، در كنار چاه آبی خوابانيد. نزديک غروب كه زنان برای كشيدن آب به سر چاه می‌آمدند، 12او چنين دعا كرد: «ای خداوند، خدای سَروَر من ابراهيم، التماس می‌كنم نسبت به سرورم لطف فرموده، مرا ياری دهی تا خواستهٔ او را برآورم. 13اينک من در كنار اين چاه ايستاده‌ام و دختران شهر برای بردن آب می‌آيند. 14من به يكی از آنان خواهم گفت: ”سبوی خود را پايين بياور تا آب بنوشم.“ اگر آن دختر بگويد: ”بنوش و من شترانت را نيز سيراب خواهم كرد،“ آنگاه خواهم دانست كه او همان دختری است كه تو برای اسحاق در نظر گرفته‌ای و سرورم را مورد لطف خويش قرار داده‌ای.»

15‏-16در حالی كه ناظر هنوز مشغول راز و نياز با خداوند بود، دختر زيبايی به نام رِبِكا كه سبويی بر دوش داشت، سر رسيد و آن را از آب چاه پُر كرد. (ربكا دختر بتوئيل و نوهٔ ناحور و مِلكه بود و ناحور برادر ابراهيم بود.) 17ناظر نزد او شتافت و از وی آب خواست. 18دختر گفت: «سَروَرم، بنوش!» و فوری سبوی خود را پايين آورد و او نوشيد. 19سپس افزود: «شترانت را نيز سيراب خواهم كرد.» 20آنگاه آب را در آبشخور ريخت و دوباره به طرف چاه دويد و برای تمام شترها آب كشيد. 21ناظر چشم بر او دوخته، چيزی نمی‌گفت تا ببيند آيا خداوند او را در اين سفر كامياب خواهد ساخت يا نه.

22پس از آنكه ربكا شترها را سيراب نمود، ناظر يک حلقهٔ طلا به وزن نيم مثقال و يک جفت النگوی طلا به وزن ده مثقال به او داده، گفت: 23«به من بگو دختر كه هستی؟ آيا در منزل پدرت جايی برای ما هست تا شب را به سر ببريم؟»

24او در جواب گفت: «من دختر بتوئيل و نوهٔ ناحور و مِلكه هستم. 25بلی، ما برای شما و شترهايتان جا و خوراک كافی داريم.»

26آنگاه آن مرد خداوند را سجده كرده، گفت: 27«ای خداوند، خدای سَروَرم ابراهيم، از تو سپاسگزارم كه نسبت به او امين و مهربان بوده‌ای و مرا در اين سفر هدايت نموده، به نزد بستگان سرورم آوردی.»

28پس آن دختر دوان‌دوان رفته، به اهل خانهٔ خود خبر داد. 29‏-30وقتی كه برادرش لابان حلقه و النگوها را بر دست خواهرش ديد و از جريان امر مطلع شد، نزد ناظر ابراهيم كه هنوز كنار چاه پيش شترهايش ايستاده بود، شتافت و به او گفت: 31«ای كه بركت خداوند بر توست، چرا اينجا ايستاده‌ای؟ به منزل ما بيا. ما برای تو و شترهايت جا آماده كرده‌ايم.»

32پس آن مرد با لابان به منزل رفت و لابان بار شترها را باز كرده، به آنها كاه و علف داد. سپس برای خادم ابراهيم و افرادش آب آورد تا پاهای خود را بشويند. 33وقتی غذا را آوردند، خادم ابراهيم گفت: «تا مقصود خود را از آمدن به اينجا نگويم لب به غذا نخواهم زد.»

لابان گفت: «بسيار خوب، بگو.»

34ناظر گفت: «من خادم ابراهيم هستم. 35خداوند او را بسيار بركت داده است و او مردی بزرگ و معروف می‌باشد. خداوند به او گله‌ها و رمه‌ها، طلا و نقرهٔ بسيار، غلامان و كنيزان، و شترها و الاغهای فراوانی داده است. 36ساره همسر سرورم در سن پيری پسری زاييد، و سرورم تمام دارايی خود را به پسرش بخشيده است. 37سرورم مرا قسم داده كه از دختران كنعانی برای پسرش زن نگيرم، 38بلكه به اينجا نزد قبيله و خاندان پدری‌اش آمده، زنی برای او انتخاب كنم. 39من به سرورم گفتم: ”شايد نتوانم دختری پيدا كنم كه حاضر باشد به اينجا بيايد؟“ 40او به من گفت: ”خداوندی كه از او پيروی می‌كنم، فرشتهٔ خود را همراه تو خواهد فرستاد تا در اين سفر كامياب شوی و دختری از قبيله و خاندان پدری‌ام پيدا كنی. 41تو وظيفه داری به آنجا رفته، پرس و جو كنی. اگر آنها از فرستادن دختر خودداری كردند، آن وقت تو از سوگندی كه خورده‌ای آزاد خواهی بود.“

42«امروز كه به سر چاه رسيدم چنين دعا كردم: ای خداوند، خدای سَروَرم ابراهيم، التماس می‌كنم مرا در اين سفر كامياب سازی. 43اينک در كنار اين چاه می‌ايستم و به يكی از دخترانی كه از شهر برای بردن آب می‌آيند خواهم گفت: ”از سبوی خود قدری آب به من بده تا بنوشم.“ 44اگر آن دختر جواب بدهد: ”بنوش و من شترانت را نيز سيراب خواهم كرد،“ آنگاه خواهم دانست كه او همان دختری است كه تو برای اسحاق پسر سرورم در نظر گرفته‌ای. 45هنوز دعايم تمام نشده بود كه ديدم ربكا با سبويی بر دوش سر رسيد و به سر چاه رفته، آب كشيد و سبو را از آب پُر كرد. به او گفتم: ”كمی آب به من بده تا بنوشم.“ 46او فوراً سبو را پايين آورد تا بنوشم و گفت: ”شترانت را نيز سيراب خواهم كرد“ و چنين نيز كرد.

47«آنگاه از او پرسيدم: تو دختر كه هستی؟

«او به من گفت: ”دختر بتوئيل و نوه ناحور و مِلكه هستم.“

«من هم حلقه را در بينی او و النگوها را به دستش كردم. 48سپس سجده كرده خداوند، خدای سَروَرم ابراهيم را پرستش نمودم، چون مرا به راه راست هدايت فرمود تا دختری از خانواده برادر سرور خود برای پسرش پيدا كنم. 49اكنون به من جواب بدهيد؛ آيا چنين لطفی در حق سرور من خواهيد كرد و آنچه درست است به جا خواهيد آورد؟ به من جواب بدهيد تا تكليف خود را بدانم.»

50لابان و بتوئيل به او گفتند: «خداوند تو را به اينجا هدايت كرده است، پس ما چه می‌توانيم بگوييم؟ 51اينک ربكا را برداشته برو تا چنانكه خداوند اراده فرموده است، همسر پسر سرورت بشود.»

52به محض شنيدن اين سخن، خادمِ ابراهيم در حضور خداوند به خاک افتاد و او را سجده نمود. 53سپس لباس و طلا و نقره و جواهرات به ربكا داد و هدايای گرانبهايی نيز به مادر و برادرانش پيشكش كرد. 54پس از آن او و همراهانش شام خوردند و شب را در منزل بتوئيل به سر بردند. خادم ابراهيم صبح زود برخاسته، به آنها گفت: «حال اجازه دهيد برويم.»

55ولی مادر و برادر ربكا گفتند: «ربكا بايد اقلاً ده روز ديگر پيش ما بماند و بعد از آن برود.»

56اما او گفت: «خواهش می‌كنم مرا معطل نكنيد. خداوند مرا در اين سفر كامياب گردانيده است. بگذاريد بروم و اين خبر خوش را به سرورم برسانم.»

57ايشان گفتند: «بسيار خوب. ما از دختر می‌پرسيم تا ببينيم نظر خودش چيست.» 58پس ربكا را صدا كرده، از او پرسيدند: «آيا مايلی همراه اين مرد بروی؟» وی جواب داد: «بلی، می‌روم.»

59آنگاه با او خداحافظی كرده، دايه‌اش را همراه وی فرستادند. 60هنگام حركت، ربكا را بركت داده، چنين گفتند: «خواهر، اميدواريم مادرِ فرزندان بسياری شوی! اميدواريم نسل تو بر تمام دشمنانت چيره شوند.»

61پس ربكا و كنيزانش بر شتران سوار شده، همراه خادمِ ابراهيم رفتند.

62در اين هنگام اسحاق كه در سرزمين نِگِب سكونت داشت، به بئرلحی رُئی بازگشته بود. 63يک روز عصر هنگامی كه در صحرا قدم می‌زد و غرق انديشه بود، سر خود را بلند كرده، ديد كه اينک شتران می‌آيند. 64ربكا با ديدن اسحاق به شتاب از شتر پياده شد 65و از خادم پرسيد: «آن مردی كه از صحرا به استقبال ما می‌آيد كيست؟»

وی پاسخ داد: «اسحاق، پسر سَروَر من است.» با شنيدن اين سخن، ربكا با روبندِ خود صورتش را پوشانيد.

66آنگاه خادم تمام داستان سفر خود را برای اسحاق شرح داد. 67اسحاق ربكا را به داخل خيمهٔ مادر خود آورد و او را به زنی گرفته به او دل بست و از غم مرگ مادرش تسلی يافت.