Genesis 23 – CCL & PCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Genesis 23:1-20

Kumwalira kwa Sara

1Sara anakhala ndi moyo zaka 127. 2Anamwalirira ku Kiriyati-Araba, kumeneku ndi ku Hebroni, mʼdziko la Kanaani, ndipo Abrahamu anapita kukakhuza maliro a Sara, namulirira.

3Kenaka Abrahamu ananyamuka pamene panali mtembo wa mkazi wakepo kupita kukayankhula ndi anthu a ku Hiti. Ndipo anati, 4“Ine ndine mlendo wongoyendayenda kwanu kuno. Bwanji mundigulitse malo woti akhale manda kuti ndiyikepo thupi la mkazi wanga.”

5Anthu a ku Hiti aja anamuyankha Abrahamu kuti, 6“Tatimverani mbuye wathu, inu ndinu mwana wa mfumu wamkulu pakati pathu. Chonde ikani thupi la mkazi wanu mʼmanda aliwonse amene mungafune. Palibe mmodzi wa ife amene adzakukanizani manda ake kuti musayike mkazi wanu.”

7Tsono Abrahamu anayimirira naweramira anthu a dziko la Hiti aja 8nati, “Ngati mwaloladi kuti ndiyike mkazi wanga kuno, ndiye ndimvereni. Mundipemphere kwa Efroni mwana wa Zohari 9kuti andigulitse phanga la Makipela, limene lili kumapeto kwa munda wake. Mumupemphe kuti andigulitse pamtengo wake ndithu inu mukuona kuti akhale manda.”

10Pamenepo nʼkuti Efroni Mhiti ali pomwepo pakati pa anthuwo amene anabwera ku chipata cha mzindawo. Ndipo onse akumva anamuyankha Abrahamu 11nati, “Ayi mbuye wanga tandimverani, ine ndikukupatsani mundawo ndiponso phanga limene lili mʼmenemo. Ndikukupatsani malowa pamaso pa anthu a mtundu wanga. Chonde ikani mtembo wamkazi wanu.”

12Apo Abrahamu anaweramanso mwaulemu pamaso pa anthu a mʼdzikolo 13ndipo anthu onse akumva Abrahamu anati kwa Efroni, “Ngati kungatheke, chonde ndimvereni. Ine ndichita kugula mundawu. Landirani ndalama za mundawu kuti ine ndiyike mkazi wanga mʼmenemo.”

14Koma Efroni anamuyankha Abrahamu nati, 15“Mundimvere mbuye wanga; mundawo mtengo wake ndi masekeli asiliva okwana 400. Koma zimenezo nʼchiyani pakati pa ine ndi inu? Ikani mtembo wa mkazi wanu.”

16Abrahamu anavomera mtengo umene ananena Efroni Ahiti onse akumva ndipo anamuwerengera masekeli asiliva okwana 400 monga mwa mtengo wa ndalama umene amalonda a nthawi imeneyo ankagwiritsa ntchito.

17Choncho munda wa Efroni wa ku Makipela umene unali kufupi ndi Mamre, kuphatikiza munda, phanga linali mʼmenemo pamodzi ndi mitengo yonse ya mʼmundamo, zinaperekedwa 18kwa Abrahamu ngati chuma chake pamaso pa anthu onse a ku Hiti amene anabwera ku chipata cha mzindawo. 19Zitatha izi, Abrahamu anayika mkazi wake Sara mʼphanga la mʼmunda wa ku Makipela, kufupi ndi ku Mamre (kumene ndi ku Hebroni) mʼdziko la Kanaani. 20Choncho Ahiti anapereka munda pamodzi ndi phanga la mʼmenemo kwa Abrahamu kuti akhale manda.

Persian Contemporary Bible

پيدايش 23:1‏-20

مرگ ساره

1‏-2ساره در سن صد و بيست و هفت سالگی در حبرون واقع در سرزمين كنعان درگذشت و ابراهيم در آنجا برای او سوگواری كرد. 3سپس ابراهيم از كنار بدن بی‌جان ساره برخاسته، به مردم حيتّی گفت:

4«من در اين سرزمين غريب و مهمانم و جايی ندارم همسر خود را دفن كنم. خواهش می‌كنم قطعه زمينی به من بفروشيد تا زن خود را در آن به خاک بسپارم.»

5‏-6آنها جواب دادند: «شما سَروَر ما هستيد و می‌توانيد همسر خود را در بهترين مقبرهٔ ما دفن كنيد. هيچيک از ما مقبرهٔ خود را از شما دريغ نخواهد داشت.»

7‏-8ابراهيم در برابر آنها تعظيم نموده، گفت: «حال كه اجازه می‌دهيد همسر خود را در اينجا دفن كنم، تمنا دارم به عفرون پسر صوحار بگوييد 9غار مكفيله را كه در انتهای مزرعهٔ اوست، به من بفروشد. البته قيمت آن را تمام و كمال خواهم پرداخت و آن غار، مقبرهٔ خانوادهٔ من خواهد شد.»

10عفرون در حضور مردم حيتّی كه در دروازهٔ شهر جمع شده بودند گفت: 11«ای سَروَرم، من غار مكفيله و مزرعه را در حضور اين مردم به شما می‌بخشم. برويد و همسر خود را در آن دفن كنيد.»

12ابراهيم بار ديگر در برابر حيتّی‌ها سر تعظيم فرود آورد، 13و در حضور همه به عفرون گفت: «اجازه بده آن را از تو خريداری نمايم. من تمام بهای مزرعه را می‌پردازم و بعد همسر خود را در آن دفن می‌كنم.»

14‏-15عفرون گفت: «ای سرورم، قيمت آن چهارصد مثقال نقره است؛ ولی اين مبلغ در مقابل دوستی ما چه ارزشی دارد؟ برويد و همسر خود را در آن دفن كنيد.» 16پس ابراهيم چهارصد مثقال نقره، يعنی بهايی را كه عفرون در حضور همه پيشنهاد كرده بود، تمام و كمال به وی پرداخت.

17اين است مشخصات زمينی كه ابراهيم خريد: مزرعه عفرون واقع در مكفيله نزديک مِلک ممری با غاری كه در انتهای مزرعه قرار داشت و تمامی درختان آن. 18اين مزرعه و غاری كه در آن بود در حضور مردم حيتّی كه در دروازهٔ شهر نشسته بودند، به ملكيت ابراهيم درآمد. 19‏-20پس ابراهيم ساره را در غار مكفيله كه آن را از مردم حيتّی به عنوان مقبرهٔ خانوادگی خود خريده بود، دفن كرد.