Ezekieli 6 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 6:1-14

Uneneri Wotsutsa Mapiri a Israeli

1Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, 2“Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku mapiri a Israeli; yankhula nawo modzudzula 3kuti, ‘Inu mapiri a ku Israeli, imvani mawu a Ambuye Yehova. Iye akuwuza mapiri, magomo, mitsinje ndi zigwa kuti: Ine ndizakuthirani nkhondo ndipo ndidzawononga nyumba zanu mʼmene mukupembedzeramo mafano. 4Maguwa anu ansembe adzagumulidwa ndipo maguwa anu ofukizira lubani adzaphwanyidwa; ndipo ndidzapha anthu anu pamaso pa mafano anu. 5Ine ndidzagoneka mitembo ya Aisraeli pamaso pa mafano awo, ndipo ndidzamwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu ansembe. 6Konse kumene mumakhala, mizinda yanu idzasanduka bwinja. Nyumba zanu zopembedzera mafano zidzagumulidwa kotero kuti maguwa anu adzawonongedwa ndi kusakazidwa, mafano anu adzaphwanyidwa ndi kuwonongedwa. Maguwa anu ofukizirapo lubani adzagwetsedwa pansi ndipo zonse zimene munapanga zidzatheratu. 7Anthu anu adzaphedwa pakati panu, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’

8“Komabe ndidzasiya ena pangʼono opulumuka ku nkhondo. Iwowa ndidzawamwazira ku mayiko ena pakati pa anthu a mitundu ina. 9Pamenepo opulumuka mwa inu adzandikumbukira ku mayiko kumene anatengedwa ukapolo. Ndidzawamvetsa chisoni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo ndi kundipandukira kuja ndiponso chifukwa kuti anayika mtima wawo pa mafano. Choncho adzachita okha manyazi chifukwa cha zoyipa zimene ankachita ndi miyambo yonyansa imene ankatsata. 10Ndipo iwo adzadziwa kuti ndine Yehova ndi kuti sindinkawaopseza chabe pamene ndinanena kuti ndidzawawononga.

11“Ambuye Yehova akuti: Womba mʼmanja mwako ndipo uponde mapazi ako pansi mwamphamvu ndipo ufuwule kuti, ‘Mayo!’ chifukwa cha zonyansa ndi zoyipa zonse zimene Aisraeli achita, pakuti adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri. 12Amene ali kutali adzafa ndi mliri, ndipo amene ali pafupi adzafa pa nkhondo, ndipo amene adzapulumuke ndi kusaphedwa adzafa ndi njala. Kotero ndidzakwaniritsa ukali wanga pa iwo. 13Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene anthu awo adzagona atafa pakati pa mafano awo mozungulira maguwa awo ansembe, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse watambalala ndi wa thundu uliwonse wamasamba ambiri, kumalo kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano awo onse. 14Choncho ndidzawalanga ndi mkono wanga ndi kusandutsa dziko kukhala bwinja. Dziko lonse kumene akukhala kuyambira ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula ndidzalisandutsa bwinja. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

New International Version – UK

Ezekiel 6:1-14

Doom for the mountains of Israel

1The word of the Lord came to me: 2‘Son of man, set your face against the mountains of Israel; prophesy against them 3and say: “You mountains of Israel, hear the word of the Sovereign Lord. This is what the Sovereign Lord says to the mountains and hills, to the ravines and valleys: I am about to bring a sword against you, and I will destroy your high places. 4Your altars will be demolished and your incense altars will be smashed; and I will slay your people in front of your idols. 5I will lay the dead bodies of the Israelites in front of their idols, and I will scatter your bones around your altars. 6Wherever you live, the towns will be laid waste and the high places demolished, so that your altars will be laid waste and devastated, your idols smashed and ruined, your incense altars broken down, and what you have made wiped out. 7Your people will fall slain among you, and you will know that I am the Lord.

8‘ “But I will spare some, for some of you will escape the sword when you are scattered among the lands and nations. 9Then in the nations where they have been carried captive, those who escape will remember me – how I have been grieved by their adulterous hearts, which have turned away from me, and by their eyes, which have lusted after their idols. They will loathe themselves for the evil they have done and for all their detestable practices. 10And they will know that I am the Lord; I did not threaten in vain to bring this calamity on them.

11‘ “This is what the Sovereign Lord says: strike your hands together and stamp your feet and cry out ‘Alas!’ because of all the wicked and detestable practices of the people of Israel, for they will fall by the sword, famine and plague. 12One who is far away will die of the plague, and one who is near will fall by the sword, and any one who survives and is spared will die of famine. So will I pour out my wrath on them. 13And they will know that I am the Lord, when their people lie slain among their idols around their altars, on every high hill and on all the mountaintops, under every spreading tree and every leafy oak – places where they offered fragrant incense to all their idols. 14And I will stretch out my hand against them and make the land a desolate waste from the desert to Diblah6:14 Most Hebrew manuscripts; a few Hebrew manuscripts Riblah – wherever they live. Then they will know that I am the Lord.” ’