Ezekieli 5 – CCL & NIVUK

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 5:1-17

Chizindikiro cha Chiweruzo

1Tsiku lina Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga lupanga lakuthwa ndipo uligwiritse ntchito ngati lumo lometera. Umete tsitsi ndi ndevu zako. Kenaka utenge sikelo ndipo ugawe tsitsilo patatu. 2Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiwiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda muzungulire mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga. 3Koma utengeko tsitsi pangʼono, ulimange mu mpindiro wa mkanjo wako. 4Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto ndi kulitentha. Moto udzayambira pamenepo mpaka ku nyumba yonse ya Israeli.”

5Ambuye Yehova akunena kuti, “Uyu ndi Yerusalemu amene ndamuyika pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mayiko onse amuzungulira. 6Koma anthu a Yerusalemu aphwanya malamulo anga pochita zoyipa kuposa anthu a mitundu ina. Iwo anandipandukira kupambana anthu ena amene awazungulira. Iwo anakana malamulo anga ndipo sanasunge malangizo anga.

7“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Popeza mwakhala osamvera kupambana anthu a mitundu ina amene akuzungulirani, popeza simunatsate malamulo anga kapena kusunga malangizo anga, mʼmalo mwake mwakhala mukutsata makhalidwe a anthu a mitundu ina amene akuzungulirani.

8“Tsono Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndikutsutsana nawe, Yerusalemu, choncho Ine ndidzakulangani. Ine ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuona. 9Chifukwa cha ntchito zanu zonyansa ndidzakulangani ndi chilango chimene sindinakulangeni nacho nʼkale lomwe ndipo sindidzakulangani ndi chofanana nacho mʼtsogolomo. 10Tsono pakati panu makolo adzadya ana awo, ndipo ana adzadya makolo awo. Ndidzakulanga ndipo otsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse zinayi. 11Ndithu, pali Ine, akutero Ambuye Yehova Wamoyo, pakuti mwayipitsa Nyumba yanga ndi mafano ano oyipa ndi miyambo yanu yonyansa, Inenso ndidzakulangani. Sindidzakulekererani kapena kukumverani chisoni. 12Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu ako chidzafa ndi mliri, kapena chidzawonongeka ndi njala; chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda, ndipo chigawo china ndidzachibalalitsira ku mphepo zonse zinayi pochita kuchithamangitsa.

13“Ndi mmene udzachitire mkwiyo wanga. Ndikadzatsiriza kuwalanga, pamenepo mtima wanga udzakhala pansi. Adzadziwa kuti Ine Yehova ndinawayankhula mwa nsanje ndikadzawalanga.

14“Ndidzakusandutsa iwe bwinja ndi chinthu chonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina amene akuzungulira, ndi kwa onse odutsapo 15Udzakhala chinthu chonyozeka ndi chonyogodoledwa. Udzakhala chenjezo ndi chinthu choopsa kwa anthu a mitundu ina amene akuzungulira ndikadzakulanga mokwiya ndi mwaukali ndi kugamula mlandu wako mokwiya. Ine Yehova ndayankhula. 16Pamene ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza ndidzatero nʼcholinga choti ndikuwonongeni. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe mowirikiza pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku. 17Ndidzatumiza njala ndi zirombo za kuthengo, ndipo zidzakulanda ana ako. Mliri ndi kuphana zidzakhala pakati pako, ndipo ndidzakubweretsera nkhondo. Ine Yehova ndayankhula.”

New International Version – UK

Ezekiel 5:1-17

God’s razor of judgment

1‘Now, son of man, take a sharp sword and use it as a barber’s razor to shave your head and your beard. Then take a set of scales and divide up the hair. 2When the days of your siege come to an end, burn a third of the hair inside the city. Take a third and strike it with the sword all around the city. And scatter a third to the wind. For I will pursue them with drawn sword. 3But take a few hairs and tuck them away in the folds of your garment. 4Again, take a few of these and throw them into the fire and burn them up. A fire will spread from there to all Israel.

5‘This is what the Sovereign Lord says: this is Jerusalem, which I have set in the centre of the nations, with countries all around her. 6Yet in her wickedness she has rebelled against my laws and decrees more than the nations and countries around her. She has rejected my laws and has not followed my decrees.

7‘Therefore this is what the Sovereign Lord says: you have been more unruly than the nations around you and have not followed my decrees or kept my laws. You have not even5:7 Most Hebrew manuscripts; some Hebrew manuscripts and Syriac You have conformed to the standards of the nations around you.

8‘Therefore this is what the Sovereign Lord says: I myself am against you, Jerusalem, and I will inflict punishment on you in the sight of the nations. 9Because of all your detestable idols, I will do to you what I have never done before and will never do again. 10Therefore in your midst parents will eat their children, and children will eat their parents. I will inflict punishment on you and will scatter all your survivors to the winds. 11Therefore as surely as I live, declares the Sovereign Lord, because you have defiled my sanctuary with all your vile images and detestable practices, I myself will shave you; I will not look on you with pity or spare you. 12A third of your people will die of the plague or perish by famine inside you; a third will fall by the sword outside your walls; and a third I will scatter to the winds and pursue with drawn sword.

13‘Then my anger will cease and my wrath against them will subside, and I will be avenged. And when I have spent my wrath on them, they will know that I the Lord have spoken in my zeal.

14‘I will make you a ruin and a reproach among the nations around you, in the sight of all who pass by. 15You will be a reproach and a taunt, a warning and an object of horror to the nations around you when I inflict punishment on you in anger and in wrath and with stinging rebuke. I the Lord have spoken. 16When I shoot at you with my deadly and destructive arrows of famine, I will shoot to destroy you. I will bring more and more famine upon you and cut off your supply of food. 17I will send famine and wild beasts against you, and they will leave you childless. Plague and bloodshed will sweep through you, and I will bring the sword against you. I the Lord have spoken.’