Ezekieli 36 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 36:1-38

Kubwezeretsedwa kwa Israeli

1“Iwe mwana wa munthu, yankhula kwa mapiri a Israeli ndipo unene kuti, ‘Inu mapiri a Israeli, imvani mawu a Yehova.’ 2Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mdani wanu ankanena kuti, ‘Aa! Dziko lamapiri lakalekale lija lasanduka lathu.’ 3Choncho nenera ndipo uwawuze kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anakusakazani ndi kukuponderezani ku mbali zonse motero kuti munakhala mʼmanja mwa anthu a mitundu ina yonse ndipo anthu ankakunenani ndi kukunyozani, 4choncho, inu mapiri a Israeli, imvani zimene Ine Ambuye Yehova ndikuwuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene yakhala ikufunkhidwa komanso kunyozedwa ndi anthu a mitundu ina okuzungulirani. 5Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mu mkwiyo wanga woopsa ndinayankhula kuyimba mlandu mitundu ina yonse ya anthu makamaka a ku Edomu. Iwowa mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndi mwa nkhwidzi analanda dziko langa ndi kulisandutsa lawo ndi kutengeratu dziko la msipu kukhala lawo.’ 6Nʼchifukwa chake, lengeza ku dziko la Israeli, ndipo uwuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikuyankhula ndi mtima wokwiya kwambiri chifukwa inu munalandira chitonzo cha anthu a mitundu ina.’ 7Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikulumbira nditakweza dzanja langa kuti mitundu ya anthu idzatozedwanso.

8“Koma Inu mapiri a Israeli mudzaphukanso nthambi ndipo mudzawabalira zipatso anthu anga a Israeli, pakuti ali pafupi kubwerera kwawo. 9Taonani, Ine ndili mbali yanu ndipo ndidzakukomerani mtima. Mudzalimidwa ndi kudzalidwa. 10Ndidzachulukitsa chiwerengero cha anthu anu, nyumba yonse ya Israeli. Mʼmizinda mudzakhalanso anthu ndipo mabwinja adzamangidwanso. 11Ndidzachulukitsa chiwerengero cha amuna pamodzi ndi ziweto zomwe, ndipo adzachuluka kwambiri ndi kubereka ana ambiri. Ndidzakhazika anthu mʼdzikomo monga analili kale, ndi kukulemeretsani kuposa kale. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. 12Ndidzachititsa anthu kuyenda pa inu, ndiye kuti inu anthu anga Aisraeli. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inu mudzakhala cholowa chawo. Simudzalandanso ana awo.

13“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anthu amanena kuti, ndiwe dziko limene limadya anthu ake ‘kulanda ana a mtundu wake,’ 14nʼchifukwa chake, simudzadyanso anthu kapena kulanda ana a mtundu wako. Ine Ambuye Yehova ndikutero. 15Sindidzakulolaninso kumva mnyozo wa anthu a mitundu ina, kapena kupirira kunyogodola kwawo kapenanso kupunthwitsanso anthu a mʼdziko lako. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

16Yehova anandiyankhulanso kuti: 17“Iwe mwana wa munthu, pamene anthu a Israeli ankakhala mʼdziko lawolawo, analiyipitsa ndi makhalidwe awo ndiponso zochita zawo. Machitidwe awo pamaso panga anali onyansa pa zachipembedzo ngati msambo wa mkazi amene ali pa nthawi yake. 18Tsono ndinawalanga chifukwa cha magazi amene anakhetsa mʼdzikomo, ndiponso chifukwa anayipitsa dziko ndi mafano awo. 19Ndinawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anabalalikira mʼmayiko onse. Ndinawalanga molingana ndi makhalidwe awo ndi zochita zawo. 20Atafika kwa anthu a mitundu ina, kulikonse kumene anapitako, anayipitsa dzina langa loyera. Zinatero popeza anthu ponena za iwo ankanena kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, komatu anachotsedwa ku dziko lake.’ 21Koma Ine ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraeli analiyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapitako.

22“Nʼchifukwa chake awuze Aisraeliwo kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndidzachita zimene ndidzachitezo osati chifukwa cha inuyo Aisraelinu ayi, koma chifukwa cha dzina langa, limene mwaliyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapitako. 23Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

24“Pakuti Ine ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzakusonkhanitsani kuchoka ku mayiko onse ndi kukubwezerani ku dziko lanulanu. 25Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. 26Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. 27Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga. 28Mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. 29Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuyipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu ndipo sindidzakugwetseraninso njala. 30Ndidzachulukitsa zipatso za mʼmitengo yanu ndi zokolola za mʼmunda mwanu, kotero kuti simudzanyozedwanso pakati pa anthu a mitundu ina chifukwa cha njala. 31Pamenepo mudzakumbukira makhalidwe anu oyipa ndi ntchito zanu zoyipa. Machimo anu ndi ntchito zanu zonyansa zidzakuchititsa nokha manyazi. 32Tsono dziwani kuti Ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ayi, ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Ndiyetu chitani manyazi ndipo mugwetse nkhope zanu, inu Aisraeli chifukwa cha makhalidwe anu!

33“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limene ndidzayeretse machimo anu onse, ndidzayikamonso anthu mʼmizinda yanu, ndipo ndidzamanganso nyumba pa mabwinja. 34Dziko limene linasanduka chipululu lizidzalimidwanso. Mʼmalo moti aliyense wopitamo alione dzikolo ngati chipululu tsopano adzaliona lolimidwa. 35Iwo adzati, ‘Dziko ili, limene linali chipululu, lasanduka munda wa Edeni. Mizinda imene inali mabwinja osiyidwa ndi owonongedwa, tsopano ndi yotetezedwa ndi yokhalamo anthu. 36Ndipo anthu a mitundu ina okhala pafupi nanu amene anatsala adzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndinamanganso mizinda yowonongeka ndi kudzalanso zinthu zatsopano mʼmalo mʼmene munali chipululu. Ine Yehova ndayankhula ndipo ndidzazichitadi.’

37“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzalolanso Aisraeli kuti andipemphe zoti ndiwachitire: Ndidzachulukitsa anthu awo ngati nkhosa. 38Adzachulukadi ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu pa nthawi za chikondwerero. Choncho mizinda ya mabwinja idzadzaza ndi anthu. Zikadzatero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以西結書 36:1-38

預言賜福以色列

1「人子啊,你要向以色列的山嶺發預言說,『以色列的山嶺啊,你們要聽耶和華的話! 2主耶和華這樣說,仇敵說,哈哈,這古老的山峰歸我們了!』 3所以你要發預言,宣告主耶和華這樣說,『你們被蹂躪、掠奪,歸了列國所有,成了外族人的話柄和笑談。 4因此,以色列的山嶺、溪流、幽谷、荒地、廢墟以及那些被外族人擄掠和譏諷的城邑啊,你們要聽主耶和華的話。』 5主耶和華說,『我要在怒火中斥責列國和以東,他們幸災樂禍,滿腹憤恨,把我的土地據為己有,侵佔其中的草場。』 6所以你要對以色列說預言,告訴以色列的山岡溪谷,耶和華這樣說,『因為你們曾遭受外族人的羞辱,我為你們滿懷義憤。 7所以我誓言要讓你們四圍的外族人也受羞辱。這是主耶和華說的。

8「『以色列的山嶺啊,你們要為我的以色列子民長出枝葉,結出果子,因為他們快要回來了。 9看啊,我要幫助你們,垂顧你們,使你們被耕種。 10我要增加居住在你們那裡的以色列人,使城邑有人居住,廢墟得以重建。 11我要使你們那裡的人畜興旺,多多繁衍,我要使人們居住在你們那裡,好像以前一樣,讓你們比以前更興盛。這樣,你們就知道我是耶和華。 12我要引領我的以色列子民在你們那裡出入,使你們成為他們的產業,不再奪走他們的兒女。』 13主耶和華說,『雖然人們說你們吞吃以色列人、奪走他們的兒女。 14但你們今後必不再吞吃以色列人,不再奪走他們的兒女。這是主耶和華說的。 15我必不再使你們聽見外族人的辱罵和嘲笑,也不再使你們的國民喪失子女。這是主耶和華說的。』」

16耶和華對我說: 17「人子啊,當以色列人住在本土時,他們的惡行玷污了那裡,他們的行為在我眼中就像經期的婦女一樣污穢。 18他們殺人流血,祭拜偶像,玷污了那地方,所以我要把我的烈怒傾倒在他們身上, 19把他們驅散到列國,分散到列邦,照他們的行為報應他們。 20他們無論分散到何處,都使我的聖名受到褻瀆,因為外族人都談論他們說,『這些人是耶和華的子民,卻不得不離開耶和華的土地。』 21我顧惜我的聖名,就是以色列人在所去的列國褻瀆的聖名。

22「因此,你要告訴以色列人,主耶和華這樣說,『以色列人啊,我要行這事並非因為你們的緣故,而是因為我聖名的緣故,就是你們在所去列國褻瀆的聖名。 23我要使我偉大的名,就是你們在列國中所褻瀆的名,彰顯它的聖潔。我要當著列國的面在你們身上彰顯我的聖潔,那時他們就知道我是耶和華。這是主耶和華說的。 24我要從列邦列國招聚你們,領你們返回故土。 25我要在你們身上灑清水潔淨你們,洗淨你們所有的污穢,除掉你們心中一切的偶像。 26我要賜你們一顆新心,把新的靈放在你們裡面。我要除去你們的石心,賜給你們一顆肉心。 27我要把我的靈放在你們裡面,使你們恪守我的律例,謹遵我的典章。 28你們必安居在我賜給你們祖先的土地上。你們要做我的子民,我要做你們的上帝。 29我要拯救你們脫離各樣的污穢之事。我要使你們五穀豐登,不讓饑荒侵害你們。 30我要使樹木碩果纍纍,田間出產豐盛,免得你們因饑荒再被外族人譏笑。 31那時,你們便會想起自己邪惡的行徑,並因自己的罪惡和可憎行為而厭惡自己。 32主耶和華說,你們應當知道,我這樣做並不是為了你們。以色列人啊,你們應當為自己的行為抱愧蒙羞。』

33「主耶和華說,『在我洗淨你們一切罪惡的日子,我要使你們的城邑有人居住,廢墟得以重建。 34荒涼之地必有人耕種,路人再也看不見荒地。 35他們會說,以前的荒涼之地如今竟變得像伊甸園,被毀壞廢棄的荒涼城邑已經設防,有人居住。 36這樣,你們四周其餘的民族便知道我耶和華已重建毀壞之處,重新耕種荒廢之地。我耶和華言出必行。』

37「主耶和華說,『我要再次答應以色列人的懇求,使他們的人口增加,多如羊群。 38我要使毀壞的城邑住滿人,多如耶路撒冷在節期所獻上的羊群。這樣,他們就知道我是耶和華。』」