Ezekieli 35 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 35:1-15

Za Chilango cha Edomu

1Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu, yangʼana phiri la Seiri; yankhula moliyimba mlandu ndipo 3awawuze anthu a kumeneko kuti zimene ndikuyankhula Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu anthu a ku mapiri a Seiri ndikudana nanu. Ndidzatambasula dzanja langa kulimbana nanu, ndipo ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu. 4Mizinda yanu ndidzayisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzasanduka chipululu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

5“Munali adani a Israeli nthawi zonse, ndipo munkalola kuti Aisraeli aphedwe pa nkhondo pa nthawi ya mavuto awo, pa nthawi imene chilango chawo chinafika pachimake. 6Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzakukanthani. Imfa idzakulondolani. Popeza sunadane nako kukhetsa magazi, imfa idzakulondola. 7Phiri la Seiri ndidzalisandutsa chipululu ndipo ndidzapha onse amene amapita nabwerera kumeneko. 8Ndidzaza mapiri ake ndi mitembo. Ophedwa pa nkhondo adzagwera pa zitunda zanu, zigwa zanu ndi mʼmitsinje yanu yonse. 9Ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu mpaka muyaya, ndipo mʼmizinda yanu simudzakhalanso anthu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

10“Inu munanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu, Yuda ndi Israeli, pamodzi ndi mayiko awo omwe idzakhala yathu.’ Munanena chomwechi ngakhale kuti Ine Yehova ndinali momwemo. 11Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzachita nanu monga munachita ndi anthu a ku Yuda ndi Israeli poonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu pa iwo. Ndikadzakulangani mudzandidziwadi pakati panupo. 12Ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndinamva mawu anu onse onyoza amene munanena molimbana ndi mapiri a Israeli. Inu munati, ‘Mapiri a Israeli asanduka bwinja, ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwawononge.’ 13Mawu anu amene munayankhula monyada kundinyoza Ine ndinawamva. 14Ine Ambuye Yehova ndikuti: Dziko lonse lapansi lidzasangalala pamene ndidzakusandutsani bwinja. 15Monga momwe inu munasangalala pamene anthu anga Aisraeli anagwa, Inenso ndidzakuchitani chimodzimodzi. Udzasanduka bwinja, iwe Phiri la Seiri, iwe ndi dziko lonse la Edomu. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Bibelen på hverdagsdansk

Ezekiels Bog 35:1-15

Dom over Edom

1Herren sagde til mig: 2„Du menneske, ret blikket mod Seirs bjerg og profetér imod Edoms folk:

3Jeg er imod jer, Seirs stolte bjerge. Jeg løfter min hånd for at straffe jer og gøre jeres land til en ødemark. 4Jeg jævner jeres byer med jorden og lægger hele landet øde, så I kan forstå, at jeg er Herren.

5I har altid hadet mit folk, Israel. I overfaldt dem og sablede dem ned, dengang jeg var nødt til at straffe dem. 6Så sandt jeg lever, siger Herren: I elsker at se blod, og I skal få blod at se, for nu kommer turen til jer. 7Jeg gør Seirs bjerge til ødemark og udrydder folket, som færdes der. 8Jeg sørger for, at bjergsider, dale og vandløb bliver fyldt med lig. 9Landet bliver en ødemark for evigt, og ingen skal bo i byerne igen. Da skal I indse, at jeg er Herren.

10I rykkede ud mod Israel og Juda for at erobre dem, selvom I vidste, at jeg var deres Gud. 11Så sandt jeg lever, vil jeg straffe jer på grund af jeres vrede, had og jalousi, og I skal erkende, at det er mig, Herren, som griber ind og dømmer jer. 12Da skal I indse, at jeg hørte hvert eneste hånende ord, I udtalte imod Israels bjerge, da I mente, at de lå øde hen, og at I derfor havde ret til at besætte dem. 13I hånede mig med de mange ord, I udtalte imod mig. Men jeg hørte det alt sammen.

14Gud Herren siger: Hele verden vil fryde sig over jeres undergang. 15I frydede jer over Israels sørgelige skæbne. Nu er det min tur til at fryde mig over jeres, for I vil blive udryddet, alle I folk i Seirs bjerge og i hele Edom. Da skal I indse, at jeg er Herren.