Eksodo 6 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 6:1-30

1Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.”

2Mulungu anatinso kwa Mose, “Ine ndine Yehova. 3Ndinaonekera kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo monga Mulungu Wamphamvuzonse, koma sindinawadziwitse dzina langa kuti ndine Yehova. 4Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuwalonjeza kuti ndidzawapatsa dziko la Kanaani kumene anakhalako kale ngati alendo. 5Ndamvanso kubuwula kwa Aisraeli, amene Aigupto awayesa akapolo ndipo ndakumbukira pangano langa.”

6“Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo. 7Ndidzakutengani kukhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼgoli la Aigupto. 8Ndipo ndidzakufikitsani ku dziko limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo. Ndidzakupatsani dziko limenelo kuti likhale lanu. Ine ndine Yehova.’ ”

9Mose anawafotokozera Aisraeli zimenezi, koma iwo sanamumvere chifukwa cha kukhumudwa ndi goli lankhanza.

10Kenaka Yehova anati kwa Mose, 11“Pita ukawuze Farao mfumu ya Igupto kuti awalole Aisraeli atuluke mʼdziko lake.”

12Koma Mose ananena kwa Yehova kuti, “Ngati Aisraeli sanandimvere, Farao akandimvera chifukwa chiyani, pajatu sinditha kuyankhula bwino?”

Mibado ya Mose ndi Aaroni

13Ndipo Yehova analamula Mose ndi Aaroni kuti awuze Aisraeli ndi Farao mfumu ya Igupto kuti Aisraeli ayenera kutuluka mʼdziko la Igupto.

14Atsogoleri a mafuko awo anali awa:

Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni.

15Ana a Simeoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Saulo mwana wa kwa mkazi wa Chikanaani. Awa anali mafuko a Simeoni.

16Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137.

17Ana a Geresoni, mwa mafuko awo, anali Libini ndi Simei.

18Ana a Kohati anali Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Kohati anakhala ndi moyo zaka 133.

19Ana a Merari anali Mali ndi Musi.

Awa anali mafuko a Levi monga mwa mibado yawo.

20Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137.

21Ana a Izihari anali Kora, Nefegi ndi Zikiri.

22Ana a Uzieli anali Misaeli, Elizafani ndi Sitiri.

23Aaroni anakwatira Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wa Nasoni ndipo Iye anabereka Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara.

24Ana a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu. Awa ndiwo mafuko a Kora.

25Eliezara mwana wa Aaroni anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Putieli, ndipo anabereka Finehasi.

Awa anali atsogoleri a mabanja a Levi, monga mwa mafuko awo.

26Aaroni ndi Mose ndi aja amene Yehova anawawuza kuti, “Tulutsani Aisraeli mu Igupto mʼmagulu awo.” 27Mose ndi Aaroni ndiwo amene anayankhula ndi Farao mfumu ya Igupto kuti atulutse Aisraeli mu Igupto.

Aaroni Ayankhula Mʼmalo mwa Mose

28Tsopano pamene Yehova anayankhula kwa Mose mu Igupto, 29anati, “Ine ndine Yehova. Umuwuze Farao mfumu ya Igupto zonse zimene Ine ndikuwuze iwe.”

30Koma Mose anati kwa Yehova, “Farao akandimvera bwanji, pakuti ine sinditha kuyankhula bwino?”

Священное Писание

Исход 6:1-30

1Тогда Вечный сказал Мусе:

– Теперь ты увидишь, что Я сделаю с фараоном: под Моей могучей рукой он отпустит исраильтян, под Моей могучей рукой он даже прогонит их из своей страны.

2Всевышний сказал Мусе:

– Я – Вечный. 3Я являлся Ибрахиму, Исхаку и Якубу как Бог Всемогущий, но под именем Вечный они Меня не знали. 4Я заключил с ними соглашение, чтобы дать им землю Ханаана, где они жили как чужеземцы. 5Теперь Я услышал стон исраильтян, которых египтяне сделали своими рабами, и вспомнил про это соглашение. 6Итак, скажи исраильтянам: «Я – Вечный, и Я выведу вас из-под египетского гнёта. Я освобожу вас из рабства и спасу вас простёртой рукой и великими судами. 7Я сделаю вас Своим народом и буду вашим Богом. Тогда вы узнаете, что Я – Вечный, ваш Бог, Который вывел вас из-под египетского гнёта. 8Я приведу вас в землю, которую клялся с поднятой рукой отдать Ибрахиму, Исхаку и Якубу. Я отдам её вам во владение. Я – Вечный».

9Муса передал это исраильтянам, но они не послушали его, потому что их дух был сломлен жестокой неволей. 10Тогда Вечный сказал Мусе:

11– Пойди, скажи фараону, царю Египта, чтобы он отпустил исраильтян из своей страны.

12Но Муса сказал Вечному:

– Если даже исраильтяне не слушают меня, как послушает фараон, ведь я так косноязычен?

Родословие Мусы и Харуна

13Вечный говорил с Мусой и Харуном об исраильтянах и фараоне, царе Египта, и повелел им вывести исраильтян из Египта.

14Вот главы их кланов:

Сыновьями Рувима, первенца Исраила, были Ханох и Фаллу, Хецрон и Харми. Это кланы Рувима.

15Сыновьями Шимона были Иемуил, Иамин, Охад, Иахин, Цохар и Шаул, сын хананеянки. Это кланы Шимона.

16Вот имена сыновей Леви по их родословиям: Гершон, Кааф и Мерари. Леви прожил сто тридцать семь лет.

17Сыновьями Гершона, по кланам, были Ливни и Шимей.

18Сыновьями Каафа были Амрам, Ицхар, Хеврон и Узиил. Кааф прожил сто тридцать три года.

19Сыновьями Мерари были Махли и Муши.

Это кланы Леви по их родословиям.

20Амрам был женат на Иохеведе, сестре своего отца, которая родила ему Харуна и Мусу. Амрам прожил сто тридцать семь лет.

21Сыновьями Ицхара были Корах, Нефег и Зихри.

22Сыновьями Узиила были Мисаил, Элцафан и Ситри.

23Харун женился на Элишеве, дочери Аминадава и сестре Нахшона. Она родила ему Надава и Авиуда, Элеазара и Итамара.

24Сыновьями Кораха были Асир, Элкана и Авиасаф. Это кланы Кораха.

25Элеазар, сын Харуна, женился на одной из дочерей Путиила, и она родила ему Пинхаса.

Это главы левитских кланов, по кланам.

26Муса и Харун – это те, кому Вечный сказал: «Выведите исраильтян из Египта по их воинствам».

27Это они говорили с фараоном, царём Египта, чтобы вывести исраильтян из Египта, те самые Муса и Харун.

Харун говорит за Мусу

28Когда Вечный говорил с Мусой в Египте, 29Он сказал ему:

– Я – Вечный. Передай фараону, царю Египта, всё, что Я говорю тебе.

30Но Муса сказал Вечному:

– Я так косноязычен, как же фараон послушает меня?