Eksodo 39 – CCL & KLB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 39:1-43

Zovala za Ansembe

1Anapanga zovala za ansembe, zovala potumikira ku malo wopatulika pogwiritsa ntchito nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira. Anapanganso zovala zopatulika za Aaroni monga momwe Yehova analamulira Mose.

Chovala cha Efodi

2Popanga efodi, iwo anagwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yosalala yofewa. 3Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso. 4Iwo anapanga efodi imene inali ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa, tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. 5Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose.

6Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo. 7Kenaka anayimangirira pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli monga momwe Yehova analamulira Mose.

Chovala Chapachifuwa

8Iwo anapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri. Anachipanga ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino. 9Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri. 10Kenaka anayikapo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba anayika miyala ya rubi, topazi ndi berili; 11mzere wachiwiri anayikapo miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi; 12mzere wachitatu anayikapo miyala ya opera, agate ndi ametisiti; 13mzere wachinayi anayikapo miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi anayiyika mu zoyikamo zagolide. 14Miyalayo inalipo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse unazokotedwa ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.

15Anapanga timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe. 16Anapanganso zoyikamo zake zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anamangirira mphetezo pa ngodya ziwiri za chovala chapachifuwa. 17Anamangirira timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. 18Ndipo mbali ina ya timaunyoloto anamangirira pa zoyikapo zake ziwiri zija, ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. 19Anapanganso mphete ziwiri zagolide ndipo analumikiza ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. 20Kenaka anapanga mphete zina ziwiri zagolide ndi kuzilumikiza kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi. 21Anamangirira mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi ija monga Yehova analamulira Mose.

Zovala zina za Unsembe

22Anayipangira efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo, wolukidwa ndi mmisiri waluso. 23Mkanjowo unali ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo panali chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike. 24Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, analumikiza mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yofewa yosalala ndi yopetedwa bwino yomwe inazungulira mkanjo. 25Ndipo anapanga maberu agolide wabwino kwambiri ndipo analumikiza mozungulira mpendero pakati pa makangadzawo. 26Kotero panali mphonje imodzi ndi belu limodzi kuzungulira mpendero wa mkanjo wovala potumikira monga momwe Yehova analamulira Mose.

27Kwa Aaroni ndi ana ake anawapangira minjiro ya nsalu yofewa yosalala, yolukidwa bwino ndi munthu waluso, 28nduwira ya nsalu yofewa yosalala, lamba wa nsalu yofewa yosalala, womanga mʼmutu, ndi makabudula amʼkati a nsalu yofewa yosalala olukidwa bwino. 29Anapanga lamba wolukidwa bwino wa nsalu yofewa ndi yosalala ya mtundu wa mtambo yapepo ndi yofiira. Ili linaliluso la munthu wopanga zokometsera monga Yehova analamulira Mose.

30Iwo anapanga duwa lagolide wabwino kwambiri ngati chidindo ndipo anazokotapo mawu akuti, wopatulikira Yehova. 31Kenaka analimangira ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira, monga momwe Yehova analamulira Mose.

Mose Ayendera Chihema

32Tsopano ntchito yonse ya tenti ya msonkhano inatha. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. 33Kenaka anabweretsa chihema kwa Mose. Tenti ndi zipangizo zake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; 34chophimba cha chikopa cha nkhosa yayimuna chonyikidwa mu utoto ofiira, chophimba cha chikopa cha akatumbu ndi nsalu zophimba; 35bokosi la umboni pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake; 36tebulo pamodzi ndi zipangizo zake ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; 37choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo; 38guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani onunkhira ndi nsalu yotchinga pa khomo lolowera mu tenti; 39guwa lamkuwa ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse; beseni ndi miyendo yake; 40nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zingwe zake ndi zikhomo za tenti; zipangizo zonse za chihema, tenti ya msonkhano; 41ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.

42Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose. 43Mose anayendera ntchitoyo ndipo anaona kuti anayichita monga momwe Yehova analamulira. Kotero Mose anawadalitsa.

Korean Living Bible

출애굽기 39:1-43

제사장의 예복

1그들은 여호와께서 모세에게 명령하신 대로 청색, 자색, 홍색 실로 제 사장들이 성소에서 섬길 때 입을 아름다운 옷을 만들고 또 아론이 입을 거룩한 옷 도 만들었다.

에봇

2그들은 금실과 청색, 자색, 홍색 실과 가늘게 꼰 베실로 39:2 앞치마 비슷한 제사장의 예복.에봇을 만들었는데

3금을 얇게 두들겨 오려서 실을 만들어 청색, 자색, 홍색 실과 가는 베실에 섞어 그것을 정교하게 짰다.

4그들은 또 에봇의 어깨받이를 만들어 에봇 앞판과 뒷판의 양쪽 끝에 달아 서로 연결하고

5에봇 위에 매는 허리띠는 여호와께서 모세에게 명령하신 대로 에봇을 짤 때와 같은 방법으로 금실과 청색, 자색, 홍색 실과 가늘게 꼰 베실로 정교하게 에봇에 붙여 짰다.

6그리고 그들은 호마노를 깎아 금테에 물리고 인장 반지를 새기듯이 그 위에 야곱의 열두 아들의 이름을 새겨

7여호와께서 모세에게 명령하신 대로 그것을 양쪽 어깨받이에 달아 이스라엘 열두 지파의 상징으로 삼았다.

가슴패

8그들은 또 에봇과 마찬가지로 금실과 청색, 자색, 홍색 실과 가늘게 꼰 베실로 가슴패를 정교하게 짰다.

9그것은 가로 세로가 각각 한 뼘으로 네모가 반듯하고 두 겹으로 되어 있었다.

10그런 다음 그들은 그 가슴패 위에 네 줄의 보석을 물렸다. 첫째 줄에는 홍옥, 황옥, 녹주석;

11둘째 줄에는 홍수정, 청옥, 금강석;

12셋째 줄에는 호박, 백마노, 자수정;

13넷째 줄에는 감람석, 호마노, 벽옥이었다. 이것들은 다 금테에 물렸으며

14이 열두 보석 위에는 이스라엘 열두 지파를 상징하는 야곱의 아들들의 이름이 하나씩 새겨져 있었다.

15그리고 그들은 순금을 노끈처럼 땋아 금사슬을 만들고

16또 금테 둘과 금고리 둘을 만들어 그 고리를 가슴패 위쪽 양끝에 달고

17땋은 그 두 금사슬을 가슴패 윗고리에 연결하였으며

18사슬의 다른 두 끝은 에봇 앞쪽의 두 어깨받이 금테에 매달았다.

19그런 다음 그들은 금고리 두 개를 더 만들어 그 고리가 잘 보이지 않도록 가슴패 양쪽 아래 끝 안쪽에 달았으며

20또 다른 금고리 두 개를 더 만들어 에봇의 양쪽 옆구리 부분인 허리띠 바로 위에 달고

21여호와께서 모세에게 명령하신 대로 청색 끈으로 가슴패 고리를 에봇 고리에 매어 가슴패가 움직이지 않고 허리띠 위쪽 에봇에 부착되어 있도록 하였다.

제사장의 다른 예복

22그들은 에봇 속에 받쳐 입는 겉옷을 전부 청색 실로 짜서 만들었다.

23그 옷은 머리가 들어갈 수 있도록 구멍을 만들고 찢어지지 않게 구멍 둘레를 갑옷 깃처럼 짰다.

24그리고 청색, 자색, 홍색 실과 가는 베실로 그 옷자락의 가장자리에 석류를 만들어 달고

25순금으로 방울을 만들어 그 가장자리로 돌아가며 석류 사이사이에 달아

26여호와께서 모세에게 명령하신 대로 방울과 석류가 하나씩 번갈아 달리게 하였다.

27그들은 또 아론과 그의 아들들을 위하여 고운 모시로 긴 속옷과

28두건과 관과 속바지를 만들고

29가는 베실과 청색, 자색, 홍색 실로 수를 놓아 띠를 만들었는데 이 모든 것은 여호와께서 모세에게 명령하신 대로 만든 것이었다.

30그리고 그들은 순금으로 거룩한 패를 만들어 그 위에 인장 반지를 새기듯이 ‘여호와께 성결’ 이라 새기고

31여호와께서 모세에게 명령하신 대로 그 패를 청색 끈으로 관 앞면에 매었다.

성막의 모든 일이 완성됨

32이렇게 해서 성막의 모든 일이 완성되었다. 이스라엘 백성들은 모든 것을 여호와께서 모세에게 명령하신 그대로 만들어

33모세에게 가져왔다. 그들이 가져온 것은 막과 그 모든 기구, 갈고리, 널빤지, 가로대, 성막 기둥과 그 받침,

34붉게 물들인 숫양의 가죽 덮개, 바닷소의 가죽 덮개, 법궤를 가리는 휘장,

35십계명이 든 법궤와 그 운반채, 법궤의 뚜껑인 39:35 또는 ‘시은좌’속죄소,

36상과 그 모든 기구와 차림빵,

37순금 등대와 그 등잔과 그 모든 기구와 기름,

38향단, 거룩한 의식에 쓸 기름, 향기로운 향, 성막 출입구 휘장,

39놋제단과 놋그물, 그 제단의 운반채와 모든 기구, 넓적한 물통과 그 받침,

40뜰의 포장, 뜰 기둥과 그 밑받침, 뜰의 출입구 막, 뜰의 포장에 쓸 말뚝과 줄, 성막에서 쓰이는 모든 기구,

41그리고 아론과 그의 아들들이 성소에서 제사장 일을 볼 때 입을 거룩한 옷이었다.

42여호와께서 모세에게 명령하신 대로 이스라엘 백성은 모든 일을 완성하였다.

43모세가 그 모든 것을 점검해 보니 그들이 여호와께서 명령하신 그대로 만들었다. 그래서 모세는 그들에게 축복하였다.