Eksodo 35 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 35:1-35

Malamulo Osunga Sabata

1Mose anasonkhanitsa gulu lonse la Aisraeli ndipo anawawuza kuti, “Zinthu zimene Yehova wakulamulirani kuti muzichite ndi izi: 2Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku la chisanu ndi chiwiri likhale la Sabata, tsiku lanu lopuma, lopatulika kwa Yehova. Aliyense amene adzagwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuphedwa. 3Pa tsiku la Sabata musakoleze moto paliponse pamene mukhala.”

Zopereka ku Malo Opatulika

4Mose ananena kwa gulu lonse la Aisraeli kuti, “Zimene Yehova wakulamulirani ndi izi: 5Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa; 6nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa; ubweya wambuzi; 7zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha, 8mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; 9miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa Efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.

10“Anthu onse aluso pakati panu abwere ndi kupanga zonse zimene Yehova walamula: 11Chihema ndi tenti yake ndiponso chophimba chake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; 12Bokosi la Chipangano pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake cha bokosilo ndi nsalu zophimba bokosilo; 13tebulo pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira pamodzi ndi zipangizo zake zonse ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; 14choyikapo nyale yowunikira pamodzi ndi zipangizo zake, nyale ndi mafuta anyalezo; 15guwa lofukizira lubani pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira, mafuta odzozera ndi lubani onunkhira; nsalu yotchinga pa khomo lolowera mʼchihema; 16guwa lansembe yopsereza pamodzi ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse, beseni losambira lamkuwa ndi miyendo yake; 17nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake, ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; 18zikhomo za tenti ya chihema ndiponso za bwalo, ndi zingwe zake; 19zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.”

20Kenaka gulu lonse la Aisraeli linachoka pamaso pa Mose, 21ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika. 22Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 23Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa. 24Onse amene anapereka chopereka cha siliva kapena mkuwa anabweretsa monga chopereka kwa Yehova. Ndipo aliyense amene anali ndi matabwa a mtengo wa mkesha kuti awagwiritse ntchito mbali ina iliyonse ya ntchitoyo, anabweretsa. 25Mayi aliyense waluso analuka ndi manja ake ndi kubweretsa chomwe analuka cha mtundu wa mtambo, chapepo kapena chofiira kapena chofewa, chosalala. 26Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi. 27Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa. 28Anabweretsanso zonunkhiritsa ndiponso mafuta owunikira a olivi ndi odzozera ndi zofukizira zonunkhira. 29Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite.

Bezaleli ndi Oholiabu

30Kenaka Mose anati kwa Aisraeli, “Taonani, Yehova wasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, 31ndipo wamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: 32Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, 33kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja. 34Ndipo Iye wapereka kwa Bezaleli pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani luso lophunzitsa ena. 35Mulungu wawapatsa maluso osiyanasiyana, maluso ogoba, olemba ndondomeko, opeta zokometsera pa nsalu zamtundu wamtambo, zapepo ndi zofiira ndiponso zofewa zosalala ndi zoluka. Onsewa ndi amisiri a ntchito zamanja ndi zokonza ndondomeko.

Священное Писание

Исход 35:1-35

Закон о субботе

1Муса собрал всё общество исраильтян и сказал им:

– Вот что Вечный повелел вам: 2заниматься делами следует шесть дней, но седьмой день – святой, это суббота покоя, день, посвящённый Вечному. Всякий, кто станет в этот день заниматься делами, будет предан смерти. 3Не зажигайте в субботний день огонь в своих жилищах.

Приношения для священного шатра

(Исх. 25:1-9; 39:32-43)

4Муса сказал обществу исраильтян:

– Вечный повелел: 5из того, что у вас есть, сделайте приношение Вечному. Пусть все, у кого щедрое сердце, сделают Вечному приношение золотом, серебром и бронзой; 6голубой, пурпурной и алой пряжей и тонким льном; козьей шерстью; 7бараньей кожей, покрашенной красным, кожей дюгоней и древесиной акации; 8оливковым маслом для светильников; благовониями для масла помазания и для возжигания; 9ониксом и другими самоцветами, чтобы украсить камнями ефод и нагрудник.

10Те из вас, кто искусен в ремёслах, пусть придут и сделают всё, что повелел Вечный: 11священный шатёр с покрытием, застёжками, брусьями, перекладинами, столбами и основаниями, 12сундук с шестами и крышкой, закрывающую завесу, 13стол с шестами и всей утварью, священный хлеб, 14светильник со всей утварью и лампадами для освещения, масло для светильника, 15жертвенник для возжигания благовоний с шестами, масло для помазания, благовония, завесу для входа в священный шатёр, 16жертвенник для всесожжений с бронзовой решёткой, шестами и утварью, умывальник с его основанием, 17завесы двора со столбами и основаниями, завесу для входа во двор, 18колья с верёвками для священного шатра и двора, 19тканые одеяния для служения в святилище: священные одеяния для священнослужителя Харуна и его сыновей, когда они совершают служение.

20Исраильтяне ушли от Мусы, 21и каждый, кто хотел и кого побуждало сердце, приходил и делал приношение Вечному на изготовление шатра встречи, на службу в нём и на священные одеяния. 22Все, кто желал, – и мужчины, и женщины – приходили и приносили разные золотые изделия: броши, серьги, перстни и подвески. Они посвящали своё золото Вечному. 23У кого были голубая, пурпурная или алая пряжа, тонкий лён, козья шерсть, баранья кожа, крашенная красным, или кожа дюгоней, те приносили их. 24Те, кто мог жертвовать серебро или бронзу, приносили их в дар Вечному, и все, у кого была древесина акации для какой-либо работы, приносили её. 25Каждая женщина-умелица сама пряла и приносила то, что напряла: голубую, пурпурную или алую пряжу или тонкий лён. 26Женщины, которые умели прясть, по велению сердца пряли козью шерсть. 27Главы родов приносили оникс и другие самоцветы, чтобы украсить ими ефод и нагрудник. 28Ещё они приносили благовония и оливковое масло для светильника, для масла помазания и для возжигания. 29Все исраильтяне и исраильтянки, кого побуждало сердце, делали Вечному добровольные приношения для той работы, которую Вечный через Мусу повелел им сделать.

Бецалил и Ахолиав

(Исх. 31:1-11)

30Муса сказал исраильтянам:

– Вечный избрал Бецалила, сына Ури, внука Хура, из рода Иуды, 31и исполнил его Духом Всевышнего, мудростью, разумением, знанием и всяким мастерством. 32Он может воплощать свои замыслы в золоте, серебре и бронзе, 33может гранить и оправлять камни, резать по дереву и заниматься всяким ремеслом. 34Вечный даровал ему и Ахолиаву, сыну Ахисамаха, из рода Дана, способность учить других. 35Он дал им умение делать любую работу ремесленников, художников, ткачей и вышивальщиков по голубой, пурпурной и алой ткани и тонкому льну. Они были искусными ремесленниками и художниками.