Deuteronomo 4 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 4:1-49

Alamulidwa Kukhala Womvera

1Mverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuphunzitseni. Muwatsatire kuti mukhale ndi moyo ndi kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani. 2Musawonjezere pa zimene ndikukulamulirani ndipo musachotserepo, koma muwasunge malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.

3Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita ku Baala-Peori. Yehova Mulungu wanu anawononga aliyense amene anatsata Baala wa ku Peori pakati panu. 4Koma inu nonse amene munagwiritsitsa Yehova Mulungu wanu mukanali ndi moyo mpaka lero.

5Taonani, ndakuphunzitsani malangizo ndi malamulo monga Yehova Mulungu wanga anandilamulira kuti inuyo muwatsatire mʼdziko limene mukulowa ndi kulitengali. 6Muwasunge mosamalitsa pakuti zimenezi zidzaonetsa nzeru zanu ndi kuzindikira kwanu kwa anthu a mitundu ina, amene adzamva za malangizo onsewa nati, “Ndithudi, mtundu waukulu uwu ndi wa anthu anzeru ndi ozindikira.” 7Mtundu wina wa anthu ndi uti umene uli waukulu chomwechi, woti ukhoza kukhala ndi milungu yawo pafupi monga mmene alili Yehova Mulungu wathu ndi ife nthawi zonse pamene tipemphera kwa Iye? 8Ndipo ndi mtundu uti mwa mitundu ya anthu umene ndi waukulu chotere kuti nʼkukhala ndi malangizo ndi malamulo olungama ngati malamulo amene ndikuyika pamaso panu lero?

9Inu mungosamala ndi kudziyangʼanira kwambiri nokha kuti musayiwale zimene maso anu aona. Musalole kuti zichoke mʼmitima mwanu pa moyo wanu wonse. Zimenezi muziphunzitse kwa ana anu ndi zidzukulu zanu ngakhale mʼtsogolo. 10Kumbukirani tsiku limene munayimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebu, pamene anati kwa ine, “Sonkhanitsa anthu pamaso panga kuti amve mawu anga ndi kuti aphunzire kundilemekeza mʼmoyo wawo onse mʼdzikomo ndi kuti ana awo aziwaphunzitsa zimenezi.” 11Munabwera pafupi ndi kuyima pa tsinde pa phiri pamene phirilo limayaka moto umene umafika mpaka kumwamba. Panalinso mtambo wakuda ndi mdima wambiri. 12Kenaka Yehova anayankhula nanu kuchokera mʼmotowo. Inu munamva mawu ake okha koma simunamuone pakuti panali mawu chabe. 13Iye anakuwuzani Malamulo Khumi omwe ndi pangano lake limene anakulamulirani kuti mutsatire. Ndipo anawalemba malamulowo pa mapale awiri a miyala. 14Ndipo Yehova anandilamula nthawi imene ija kuti ndikuphunzitseni malangizo ndi malamulo amene muyenera kutsata mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani.

Mafano Aletsedwa

15Tsiku limene Yehova anayankhula nanu ku Horebu mʼmoto uja, simunaone thupi lake. Choncho mudziyangʼanire nokha mosamalitsa, 16kuti musasokonezeke ndi kudzipangira nokha fano kapena chifanizo cha mtundu uliwonse, kaya chokhala ngati mwamuna kapena ngati mkazi, 17kaya chokhala ngati nyama iliyonse ya pa dziko lapansi kapena mbalame iliyonse yowuluka mlengalenga. 18Kapena cholengedwa chilichonse choyenda pa nthaka kapena nsomba ya mʼmadzi akuya. 19Ndipo pamene muyangʼana kumwamba muona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonse zakumwambazo musakopeke kuti muzigwadire ndi kumapembedza zinthu zimene Yehova wapereka kwa anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi. 20Koma inuyo, Yehova anakutengani ndi kukutulutsani mʼngʼanjo yosungunulira zitsulo, ku Igupto kuti mukhale anthu olandira chuma chake monga mmene mulili tsopano.

21Yehova anakwiya nane chifukwa cha inu, ndipo analumbira kwathunthu kuti sindidzawoloka Yorodani ndi kulowa mʼdziko labwinolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani inu ngati cholowa chanu. 22Ine ndifera mʼdziko lino, sindiwoloka Yorodani. Koma inu mwatsala pangʼono kuwoloka ndi kukatenga dziko labwinolo. 23Samalani, musayiwale pangano limene Yehova Mulungu wanu anapangana nanu ndipo musadzipangire nokha fano la chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu waletsa. 24Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wonyeketsa ndipo ndi Mulungu wansanje.

25Mukadzakhala nthawi yayitali mʼdzikomo ndi kubereka ana ndi kukhala ndi zidzukulu ndipo mukadzasokonekera ndi kupanga fano la mtundu uliwonse, nʼkumachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kumukwiyitsa, 26ine ndi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni lero zokutsutsani kuti mudzawonongedwa msanga ndipo mudzachotsedwa mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani. Simudzakhalitsa kumeneko koma mudzawonongedwa ndithu. 27Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu ena. Ochepa okha pakati panu ndi amene adzapulumuke pakati pa anthu a mitundu ina kumene Yehova adzakupirikitsireniko. 28Kumeneko mudzapembedza milungu ya mitengo ndi miyala yopangidwa ndi anthu, imene singaone kapena kumva kapena kudya kapena kununkhiza. 29Mukanali komweko, ngati mudzamufunafuna Yehova Mulungu wanu mudzamupeza koma ngati mutamufunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 30Mukadzakhala pa chipsinjo ndipo zonsezi zikadzakuchitikirani, ndi pamene pambuyo pake mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera Iye. 31Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo, Iye sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuyiwala pangano lake ndi makolo anu, limene analitsimikiza mwa lumbiro.

Yehova Ndiye Mulungu

32Tsopano tafunsani za masiku a mʼmbuyomu, zakale inu musanabadwe, kuyambira tsiku limene Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani kuyambira kumapeto mpaka mapeto anzake a thambo. Kodi chinachitikako china chachikulu ngati ichi, kapena chinayamba chamvekako chokhala ngati ichi? 33Kodi uliponso mtundu wina wa anthu umene unamva mawu a Mulungu akuyankhula kuchokera mʼmoto nʼkukhala ndi moyo monga mwachitira inumu? 34Kodi alipo mulungu amene anayeserapo kudzitengera mtundu wa anthu kuwachotsa mu mtundu unzake mwa mayesero, zizindikiro zozizwitsa, nkhondo, komanso mwa mphamvu zake zopanda malire, kapena mwa zochita zazikulu ndi zochititsa mantha, monga zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Igupto inu mukupenya?

35Iye anakuonetsani zonsezi kuti inu muzindikire kuti Yehova ndiye Mulungu, palibenso wina wofanana naye. 36Kuchokera kumwamba, Iye anafuna kuti inu mumve mawu ake ndi kuti mukhale osunga mwambo. Pa dziko lapansi anakuonetsani moto waukulu, ndipo inu munamva mawu ake kuchokera mʼmotomo. 37Popeza anakonda makolo anu ndi kusankha adzukulu awo, a pambuyo pawo, anakutulutsani kuchoka ku Igupto ali pakati panu ndi mphamvu yake, 38kuti akupirikitsireni mayiko akuluakulu ndi amphamvu kuposa inu, ndi kukubweretsani inu ku dziko lawo kuti likhale lanu, monga liliri lero.

39Vomerezani lero ndipo dziwani mu mtima mwanu kuti Yehova ndiye Mulungu kumwamba ndi pa dziko lapansi. Palibenso wina. 40Sungani malangizo ake ndi malamulo ake amene ndikukupatsani lero lino, kuti zikuyendereni bwino inu ndi ana anu kutsogoloko, ndi kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kwa nthawi zonse.

Mizinda Yothawirako

41Kenaka Mose anapatula mizinda itatu cha kummawa kwa Yorodani, 42kumene aliyense amene wapha munthu akhoza kuthawirako ngati wopha munthuyo sanaphe mnzakeyo mwadala ndi maganizo oyipa. Iye akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi napulumutsa moyo wake. 43Mizindayo inali iyi: ku fuko la Rubeni, unali mzinda wa Bezeri ku mapiri a ku chipululu; ku fuko la Gadi, unali Ramoti ku Giliyadi; ndipo ku fuko la Manase, unali Golani ku Basani.

Kufotokozera za Malamulo

44Awa ndi malamulo amene Mose anapereka kwa Aisraeli. 45Izi ndi ndondomeko, malangizo ndi malamulo amene Mose anawapatsa iwo pamene anatuluka ku Igupto. 46Anali ku chigwa cha kufupi ndi Beti-Peori mbali ya kummawa kwa Yorodani, mʼdziko la Sihoni mfumu ya Aamori amene ankalamulira ku Hesiboni ndipo anagonjetsedwa ndi Mose ndi Aisraeli pamene ankachokera ku Igupto. 47Iye anamulanda dziko lake ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani. Awa anali mafumu awiri Aamori a kummawa kwa Yorodani. 48Dziko ili linayambira ku Aroeri cha kumphepete kwa khwawa la Arinoni ku phiri la Siyoni (limeneli ndi phiri la Herimoni), 49ndi kuphatikizapo dziko lonse la Araba cha kummawa kwa Yorodani mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, kumunsi kwa Phiri la Pisiga.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

申命記 4:1-49

當守律法

1以色列人啊,要聆聽我傳授給你們的律法,要切實遵行,以便你們可以存活,並進入你們祖先的上帝耶和華賜給你們的那片土地。 2我吩咐你們的,你們不可做任何增減,這是你們的上帝耶和華的命令,你們要遵守。 3你們親眼看見耶和華在巴力·毗珥事件中的作為,你們的上帝耶和華毀滅了你們中間所有拜巴力·毗珥的人, 4但你們這些信靠你們的上帝耶和華的人至今還活著。 5看啊,遵照我的上帝耶和華的吩咐,我把律例和典章傳授給你們,好讓你們在將要佔領的土地上遵守。 6你們要謹遵這些律例和典章,因為這樣就會讓外族人看見你們的智慧和聰明。他們聽見這些律法後,必說,『這偉大的民族真有智慧和聰明!』 7我們的上帝耶和華與我們如此親近,隨時垂聽我們的呼求,有哪個偉大民族的神明能與之相比? 8有哪個偉大的民族擁有我今天所傳授給你們的如此公義的律例和典章?

9「要謹慎、小心,不可忘記親眼所見的事,要一生銘記在心,並且告訴子子孫孫。 10那天,你們在何烈山站在你們的上帝耶和華面前,耶和華對我說,『把民眾招聚起來,讓他們聽我的教誨,學習一生敬畏我,並傳授給自己的兒女。』 11你們來到山腳下,站在那裡,山上烈焰沖天、烏雲密佈、極其幽暗。 12耶和華在火焰中對你們說話,你們只聽見祂的聲音,卻看不見祂的形像。 13祂向你們宣告祂的約,就是祂吩咐你們遵守的十誡,並寫在兩塊石版上。 14那時,耶和華吩咐我把律例和典章傳授給你們,好讓你們在將要佔領的土地上遵守。

不可拜偶像

15「你們要格外小心,耶和華在何烈山的火焰中對你們說話時,你們沒有看見任何形像, 16所以不可墮落,去為自己製造任何形狀的神像——男人、女人、 17飛禽走獸、 18爬蟲或魚類。 19當你們舉目觀看你們的上帝耶和華賜給天下萬民的日、月、星辰等天上萬象時,不要受誘惑去跪拜、供奉它們。 20耶和華拯救你們脫離埃及那座熔鐵爐,讓你們做祂自己的子民,正如今日的情形。 21因你們的緣故,耶和華向我發怒,起誓不讓我過約旦河、進入祂賜給你們作產業的那片佳美之地。 22我將死在約旦河這邊,過不了約旦河。但你們必過去得到那片佳美之地。 23你們要謹慎,不可忘記你們的上帝耶和華與你們所立的約,不可違背你們上帝耶和華的禁令,去製造任何形狀的神像。 24因為你們的上帝耶和華是烈火,是痛恨不貞的上帝。

25「將來,即使你們在那裡安頓已久、子孫滿堂,也不可墮落、製造任何形狀的神像,不可做你們的上帝耶和華視為邪惡的事,惹祂發怒。 26否則,今天我叫天地作證,你們必很快從約旦河對面將要佔領的土地上滅亡,你們必被徹底消滅,不得在那裡長久居住。 27耶和華必把你們驅散到列邦,使你們在列邦中的人數所剩無幾。 28你們必在那裡供奉人用木石造的不會看、不會聽、不會吃、不會聞的神像。 29但你們若在那裡尋求你們的上帝耶和華,全心全意地尋求祂,就必尋見。 30日後,當你們遭遇這些事,受盡苦難的時候,必歸向你們的上帝耶和華,聽從祂。 31因為你們的上帝耶和華充滿憐憫,祂不會拋棄你們,滅絕你們,也不會忘記祂與你們祖先所立的誓約。

獨一的上帝

32「你們可以查考歷史,自上帝創造世人以來,這樣的奇事,天地之間何曾有過?誰曾聽聞? 33有哪個民族像你們一樣,聽見了上帝在火中說話,還活了下來? 34有哪個神明像你們的上帝耶和華那樣在埃及當著你們的面降災禍、行神蹟奇事、興起戰爭、伸出臂膀、施展大能的手、以偉大而可畏的作為拯救一族脫離異邦? 35耶和華行這樣的事,是要叫你們知道祂是上帝,除祂以外,別無他神。 36祂讓你們聽見祂從天上來的聲音,好教導你們,又在地上讓你們看見祂的烈火,並聽見祂在烈火中說的話。 37因為祂愛你們的祖先,所以揀選你們,親自用大能把你們從埃及領出來, 38趕走比你們強大的民族,領你們進入他們的土地,把他們的土地賜給你們作產業,正如今日的情形。 39所以,今天你們要知道並謹記,耶和華是天上地下的上帝,此外別無他神。 40我今天將祂的律例和誡命傳授給你們,你們要遵守,以便你們及子孫都蒙福,在你們上帝耶和華所賜的土地上得享長壽。」

設立避難城

41那時,摩西約旦河東劃出三座城作避難城, 42供素無冤仇卻誤殺他人者逃往避難。 43三座城分別是曠野高原的比悉——供呂便人避難,基列拉末——供迦得人避難,巴珊哥蘭——供瑪拿西人避難。

重申律法

44以下是摩西頒佈給以色列人的律法, 45即在離開埃及後傳授給他們的法度、律例和典章。 46當時他們在約旦河以東伯·毗珥對面的山谷,那裡原屬於希實本亞摩利西宏摩西以色列人離開埃及後消滅了西宏47佔領了他的土地,還佔領了巴珊的土地。西宏約旦河東亞摩利人的兩個王, 48其國土從亞嫩谷邊的亞羅珥一直到西雲山,即黑門山, 49包括約旦河東的整個亞拉巴,遠至毗斯迦山腳的亞拉巴海。