Deuteronomo 3 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Deuteronomo 3:1-29

Kugonjetsedwa kwa Ogi Mfumu ya ku Basani

1Kenaka tinakhota ndi kumayenda mokwera mtunda ndi njira yolowera ku Basani. Ndipo Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anakumana nafe ndipo anamenyana nafe ku Ederi. 2Yehova anati kwa ine, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.”

3Choncho Yehova Mulungu wathu anapereka mʼmanja mwathu Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo. Tinawakantha onsewo osasiya ndi mmodzi yemwe. 4Pa nthawi imeneyo tinatenga mizinda yake yonse. Pa mizinda 60, panalibe ndi umodzi womwe umene sitinawalande, mʼdera lonse la ufumu wa Ogi ku Basani chimene ndi chigawo cha Arigobu. 5Mizinda yonseyi inali yotetezedwa ndi malinga ataliatali wokhala ndi zitseko ndi zitsulo, komabe panali midzi ina yambiri imene inalibe malinga. 6Tinawawonongeratu monga momwe tinachitira Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Tinawononga mzinda uliwonse, amayi, amuna ndi ana omwe. 7Koma tinafunkha ziweto ndi katundu wawo yense.

8Choncho pa nthawi imeneyi tinalanda kwa mafumu awiri Aamori, dera la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku khwawa la Arinoni mpaka ku Phiri la Herimoni. 9(Asidoni amatcha Herimoni kuti Siriyoni, pamene Aamori amalitcha Seniri). 10Tinalanda mizinda yonse ya ku mapiri, ku Giliyadi, Basani mpaka ku Saleka ndi Ederi, mizinda ya mu ufumu wa Ogi wa ku Basani. 11(Ogi, mfumu ya ku Basani, anali yekhayo amene anatsala mwa mtundu wa anthu ataliatali a Chirefai. Bedi lake linali lachitsulo ndipo lalitali kuposa mamita anayi. Mulifupi mwake munali mamita awiri. Bedilo likanalipo ku Raba kwa Aamori).

Kugawana Dziko

12Dziko limene tinalanda nthawi imeneyo, ndinapatsa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi dera la kumpoto kwa Aroeri cha mʼmphepete mwa khwawa la Arinoni kuphatikizapo theka la dziko lamapiri la Giliyadi ndi mizinda yake. 13Theka la fuko la Manase ndinalipatsa dziko lonse lotsala la Giliyadi ndi Basani yense yemwe ndi dera la ufumu wa Ogi. (Chigawo chonse cha Arigobu mu Basani chinkadziwika kuti ndi dziko la Arefai. 14Yairi, mdzukulu wa Manase, anatenga chigawo chonse cha Arigobu mpaka ku malire a Agesuri ndi Amaakati. Anatcha chigawochi dzina lake, moti mpaka lero Basani amatchedwa Havoti Yairi). 15Ndipo ndinapereka Giliyadi kwa Makiri. 16Koma kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi ndinapereka chigawo chochokera ku Giliyadi kutsetsereka mpaka ku khwawa la Arinoni (pakati pa khwawalo ndiye panali malire) ndi kupitirira mpaka ku mtsinje wa Yaboki umene ndi malire Aamoni. 17Malire ake a chakumadzulo anali Yorodani ku Araba, kuchokera ku Kinereti mpaka ku Nyanja ya Araba (Nyanja ya Mchere), mʼmunsi mwa matsitso a Pisiga.

18Ndinakulamulirani nthawi imene ija kuti, “Yehova Mulungu wanu wakupatsani dziko ili kuti likhale lanu. Koma amuna amphamvu onse ali ndi zida zankhondo, awoloke kutsogolera abale anu Aisraeli. 19Koma akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri) zikhoza kumakhalabe mʼmizinda imene ndakupatsani, 20mpaka Yehova atapereka mpumulo kwa abale anu, nawonso atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa patsidya pa Yorodani, monga wachitira ndi inu. Kenaka, aliyense wa inu akhoza kudzabwerera ku dziko limene ndinakupatsani.”

Mose Aletsedwa Kuwoloka Yorodani

21Nthawi imeneyo ndinamulamula Yoswa kuti, “Waona wekha ndi maso ako zonse zimene Yehova Mulungu wako anachitira mafumu awiriwa. Yehova adzachita zomwezo ndi mafumu ena onse kumene mukupitako. 22Musawaope chifukwa Yehova Mulungu mwini adzakumenyerani nkhondo.”

23Nthawi imeneyo ndinachonderera Yehova kuti, 24“Ambuye Mulungu, mwayamba tsopano kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu. Ndi mulungu uti ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene angachite ntchito zozizwitsa zimene mumachita? 25Mundilole ndipite ndi kukaona dziko labwinolo kutsidya kwa Yorodani dziko la mapiri abwinowo ndi Lebanoni.”

26Koma chifukwa cha inu, Yehova anakwiya nane osandimvera. Yehova anati, “Basi pakwana, usayankhulenso ndi ine zimenezi. 27Pita pamwamba pa phiri la Pisiga ndipo uyangʼane kumadzulo, kumpoto, kummwera ndi kummawa. Ulione dzikolo ndi maso ako pakuti suwoloka Yorodaniyu. 28Koma langiza Yoswa ndipo umulimbikitse ndi kumupatsa mphamvu pakuti adzatsogolera anthu awa kuwoloka ndipo adzawathandiza kuti atenge dziko limene ulioneli.” 29Ndipo tinakhala mʼchigwa pafupi ndi Beti-Peori.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

申命记 3:1-29

击败巴珊王噩

1“之后,我们前往巴珊巴珊率全军在以得来迎战我们。 2耶和华对我说,‘不要怕他,因为我已把他及其众民和土地交在你手中,你要像从前对付希实本亚摩利西宏一样对付他。’

3“我们的上帝耶和华把巴珊及其众民交在我们手中,我们杀了他们,一个不留。 4我们占领了亚珥歌伯全境,即巴珊的所有城邑,共六十座。 5这些城邑围墙高耸,门闩牢固。我们还占领了许多没有城墙的乡村。 6像对付希实本西宏一样,我们将这些城邑夷为平地,城中的男女老幼一个不留, 7只留下牲畜和财物作战利品。 8于是,我们攻占了约旦河东两个亚摩利王的土地,从亚嫩谷一直到黑门山—— 9西顿人称黑门山为西连亚摩利人称之为示尼珥—— 10攻占了高原的城邑、整个基列巴珊,远至巴珊的城邑撒迦以得来11巴珊是最后一个利乏音人。他的床是铁做的,存放在亚扪人的拉巴城,长四米,宽一点八米。

分配约旦河东之地

12“我们占领了这片土地后,我把亚嫩谷边的亚罗珥以北地区和基列山区的一半及其城邑,分给吕便支派和迦得支派, 13基列山区的另一半,以及的王国巴珊全境——整个亚珥歌伯分给玛拿西半个支派。巴珊地区又被称为利乏音人之地。 14玛拿西的子孙雅珥得到亚珥歌伯全境,远至基述人和玛迦人的边界。他按自己的名字给那地方取名叫哈倭特·雅珥,沿用至今。 15我又把基列分给玛吉16把从基列亚嫩谷,以谷中央为界,远至亚扪人的边界雅博河地区分给吕便支派和迦得支派。 17我还把亚拉巴,就是以约旦河为界,从基尼烈直到东面毗斯迦山脚的亚拉巴海,即盐海地区给了他们。

18“那时我吩咐他们,‘你们的上帝耶和华已经把这些地方赐给你们,但你们所有的战士必须带着兵器过河,做同胞的先锋。 19我知道你们有许多牲畜,你们的妻子、儿女和牲畜可以留在我分给你们的城邑。 20等你们的上帝耶和华使其他以色列人和你们一样有了安身之所,占领了耶和华赐给他们的约旦河西之地后,你们才可以返回我分给你们的家园。’ 21那时我吩咐约书亚,‘你们的上帝耶和华怎样对付那两个王,你都亲眼看见了。耶和华必以同样的方式对付你将去攻占的各国。 22不要怕他们,因为你的上帝耶和华将为你争战。’

摩西不得进入迦南

23“那时,我恳求耶和华,说, 24‘主耶和华啊,你已向仆人彰显你的伟大和权能,天上地下没有神明可与你相比! 25求你让我过去看看约旦河那边的佳美之地——那美好的山区和黎巴嫩。’ 26但因你们的缘故,耶和华向我发怒,不听我的恳求,祂对我说,‘够了,不要再跟我提这件事。 27你可以上毗斯迦山顶,向东南西北眺望,但你不可过约旦河。 28你要委任约书亚,勉励他,支持他,因为他必带领以色列人过河,占领你眺望的那片土地。’ 29当时,我们驻扎在伯·毗珥对面的谷中。