2 Samueli 20 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 20:1-26

Seba Awukira Davide

1Ndipo munthu wina wokonda kuyambitsa chisokonezo, dzina lake Seba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini, anali komweko. Iye analiza lipenga ndipo anafuwula kuti,

“Ife tilibe chathu mu mfumu wa Davide,

tilibe gawo mwa mwana wa Yese!

Inu Aisraeli aliyense apite ku nyumba kwake!”

2Kotero Aisraeli onse anamuthawa Davide ndipo anatsatira Seba mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda anakhala ndi mfumu yawo njira yonse kuchokera ku Yorodani mpaka ku Yerusalemu.

3Davide atabwerera ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, iye anatenga azikazi khumi aja amene anawasiya kuti aziyangʼanira nyumba yaufumu, ndipo anawayika mʼnyumba imene anayikapo mlonda. Iye ankawadyetsa koma sanagone nawonso. Anasungidwa kwa okha mpaka tsiku la kufa kwawo ndipo anakhala ngati akazi amasiye.

4Kenaka mfumu inati kwa Amasa, “Itanitsa ankhondo a Yuda kuti abwere kwa ine pasanathe masiku atatu, ndipo iwe udzakhale nawo.” 5Motero Amasa anakayitana Ayuda, koma anachedwa, napitirira pa nthawi imene mfumu inamuyikira.

6Davide anati kwa Abisai, “Tsono Seba mwana wa Bikiri adzatipweteka kuposa momwe Abisalomu anatichitira. Tenga asilikali a mbuye wako ndipo umuthamangitse, mwina adzapeza mizinda yotetezedwa ndi kutithawa ife.” 7Kotero anthu a Yowabu, Akereti ndi Apeleti ndiponso asilikali onse amphamvu anapita motsogozedwa ndi Abisai. Iwo anayenda kuchokera ku Yerusalemu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri.

8Ali pa mwala waukulu wa ku Gibiyoni, Amasa anabwera kudzakumana nawo. Yowabu anali atavala chovala chausilikali ndipo pamwamba pa malayawo, mʼchiwuno mwake anavala lamba womangirirapo lupanga lili moyikamo mwakemo. Akuyenda linasololoka kuchoka moyikamo mwake.

9Yowabu anati kwa Amasa, “Kodi uli bwanji mʼbale wanga?” Kenaka Yowabu anamugwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja ndi kupsompsona. 10Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri.

11Mmodzi mwa ankhondo a Yowabu anakayimirira pafupi ndi mtembo wa Amasa ndipo anati, “Aliyense amene amakonda Yowabu ndi aliyense amene ali wa Davide, atsatire Yowabu!” 12Amasa anagona pakati pa msewu atasamba magazi ake, ndipo munthuyo anaona kuti asilikali onse amayima pamenepo. Atazindikira kuti aliyense amene ankafika pamene panali Amasa amayima, iye anamuchotsa mu msewu ndi kumukokera mʼmunda ndipo anamuphimba ndi nsalu. 13Amasa atachotsedwa pa msewu anthu onse anapita ndi Yowabu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri.

14Seba anadutsa mafuko onse a Israeli mpaka ku Abeli ndi Beti-Maaka ndiponso chigawo chonse cha Abeli, amene anasonkhana pamodzi ndi kumutsata iye. 15Ankhondo onse pamodzi ndi Yowabu anafika ndi kumuzungulira Seba mu Abeli-Beti-Maaka. Iwo anapanga mzere wa nkhondo mpaka ku mzinda, ndipo unayangʼanana ndi malo otetezera a kunja. Pamene amalimbana ndi khoma kuti aligwetse, 16mayi wina wanzeru anafuwula kuchokera mu mzindawo, “Tamverani! Tamverani! Muwuzeni Yowabu abwere pano kuti ndiyankhule naye.” 17Yowabu anayandikira kumene kunali mayiyo, ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndinu Yowabu?”

Iye anayankha kuti, “Ndine.”

Mayiyo anati, “Tamverani zimene mtumiki wanu akuti anene.”

Yowabu anayankha kuti, “Ndikumvetsera.”

18Iye anapitiriza kunena kuti, “Kalekale ankanena kuti, ‘Kapeze yankho lako ku Abeli,’ ndipo nkhani imathera pamenepo. 19Ife ndife anthu a mtendere ndi okhulupirika mu Israeli. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene ndi mayi mu Israeli. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kufafaniza cholowa cha Yehova?”

20Yowabu anayankha kuti, “Ayi ndisatero. Ine sindikufuna kuwufafaniza kapena kuwuwononga. 21Nkhani simeneyo ayi. Koma munthu wina wa ku dziko lamapiri la Efereimu, dzina lake Seba mwana wa Bikiri, wawukira mfumu Davide. Muperekeni munthuyo ndipo ine ndidzachoka pa mzinda uno.”

Mayiyo anati kwa Yowabu, “Mutu wake tikuponyerani pa khoma pano.”

22Ndipo mayiyo anapita kwa anthu onse ndi malangizo ake anzeru, ndipo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikiri ndipo anawuponya kwa Yowabu. Kotero iye analiza lipenga ndipo anthu ake anachoka pa mzindawo, aliyense nʼkubwerera kwawo. Ndipo Yowabu anabwerera kwa mfumu ku Yerusalemu.

23Yowabu ndiye amalamulira gulu lonse la ankhondo. Benaya mwana wa Yehoyada amalamulira Akereti ndi Apeleti. 24Adoramu amayangʼanira anthu ogwira ntchito ya thangata, Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika, 25Seva anali mlembi wa mfumu. Zadoki ndi Abiatara anali ansembe 26ndipo Ira wa ku Yairi anali wansembe wa Davide.

Bibelen på hverdagsdansk

2. Samuelsbog 20:1-26

1Blandt dem fra Nordriget var der en ondsindet mand ved navn Sheba, søn af Bikri af Benjamins stamme. Midt i skænderiet stødte Sheba i hornet og råbte: „Hvad skal vi med David? Han hører jo ikke til blandt os! Kom, alle jer fra Nordriget, lad os gå hjem!” 2Da forlod de alle David og fulgte efter Sheba, mens judæerne sluttede op om kongen og ledsagede ham fra Jordanfloden op til Jerusalem.

3Da David kom hjem, lod han de ti medhustruer, som havde boet i paladset under hans eksil, flytte til et bevogtet hus et andet sted. Der blev sørget for dem, men han havde aldrig mere noget med dem at gøre. De levede afsondret til deres dødsdag, som om de var enker.

Joab slår Amasa ihjel og nedkæmper Shebas oprør

4Derefter befalede kongen Amasa at mobilisere Judas hær og være tilbage inden tre dage. 5Amasa begav sig af sted for at samle tropperne, men det tog ham mere end de tre dage, kongen havde afsat til det. 6Da sagde kongen til Abishaj:

„Jeg er bange for, at Sheba bliver en større trussel for os, end Absalom var. Tag min livvagt og sæt efter ham, så han ikke når i sikkerhed i en befæstet by.”

7Straks satte Abishaj og Joab efter Sheba sammen med elitesoldaterne og kongens livvagt. 8-10Da de kom til den store sten i Gibeon, stod de pludselig ansigt til ansigt med Amasa. Joab var iført sin kampuniform og havde en daggert spændt i sit bælte. Da han nu gik hen imod Amasa for at hilse på ham, faldt daggerten ud af skeden. Han samlede den hurtigt op med venstre hånd. „Godt at se dig,” sagde han hjerteligt til Amasa, idet han trak ham i skægget med sin højre hånd under foregivende af at ville kysse ham på kinden. Men i det samme stødte han med sin venstre hånd daggerten i maven på den intetanende Amasa, så indvoldene væltede ud på jorden. Sådan gjorde Joab det af med Amasa i et eneste stød. Joab og hans bror Abishaj lod ham ligge på jorden, for de havde travlt med at forfølge Sheba.

11En af Joabs unge officerer stillede sig ved Amasas lig og råbte til soldaterne: „Hvis I er loyale overfor David og Joab, så slut jer til os!”

12Amasa lå imidlertid i en stor blodpøl midt på vejen, og da Joabs officerer så, at soldaterne stimlede sammen om ham, trak de liget væk fra vejen og dækkede det med en kappe. 13Så snart Amasa var blevet fjernet, fulgte krigerne med Joab i jagten på Sheba.

14-15I mellemtiden drog Sheba gennem hele Nordriget, hvor det lykkedes ham at få alle sine slægtninge til at slutte op om sig. De fulgte med ham til byen Abel-Bet-Ma’aka, hvor Joab og hans hær indhentede dem og belejrede byen. Joab byggede en vold omkring byen og begyndte en systematisk nedrivning af muren.

16Men i byen var der en klog kvinde, som gik op på muren og råbte: „Hør her! Sig til Joab, at han skal komme herhen. Jeg vil tale med ham.”

17Da Joab kom derhen, spurgte hun: „Er du Joab?”

„Ja,” svarede Joab.

18Så fortsatte hun: „Fra gammel tid har man sagt: ‚Søg råd i byen Abel!’ Hos os kunne man få gode råd og hjælp til at løse konflikter. 19Men nu er du ved at ødelægge en ældgammel, fredselskende by i Israel! Vil du virkelig ødelægge det, som tilhører Herren?”

20Joab svarede: „Nej, det vil jeg bestemt ikke! Jeg er ikke ude på at ødelægge jeres by. 21Jeg er kun ude efter en mand ved navn Sheba fra Efraims bjergland, for han har gjort oprør imod kong David. Hvis I vil udlevere ham til os, skal vi gerne lade jeres by være i fred.”

„Godt,” svarede kvinden, „så smider vi hans hoved over muren ned til jer.”

22Den kloge kvinde fik så byens indbyggere overtalt til at hugge hovedet af Sheba og kaste det over muren.

Derefter stødte Joab i hornet, så hæren trak sig tilbage, og alle krigerne vendte hjem, hver til sit. Joab selv vendte tilbage til kongen i Jerusalem.

23Joab blev så igen øverstkommanderende for Israels hær. Benaja, Jojadas søn, var chef for den kongelige livvagt; 24Adoniram havde opsynet med tvangsarbejderne; Joshafat, Ahiluds søn, var historiker og rigsarkivar; 25Sheva var statssekretær; Zadok og Ebjatar var præster i templet; 26og Ira fra Jair var hofpræst.