2 Mbiri 9 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 9:1-31

Mfumu Yayikazi ya ku Seba Ichezera Solomoni

1Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni, inabwera mu Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. Inafika ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri, ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake. 2Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta kwa iye komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo. 3Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru za Solomoni komanso nyumba yaufumu imene anamanga, 4chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo; atumiki opereka zakumwa ndi zovala zawo ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.

5Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu, ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona. 6Koma sindinakhulupirire zimene ankanena mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe la kuchuluka kwa nzeru zanu, pakuti zaposa zimene ndinamva. 7Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu! 8Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando wake waufumu kuti mulamulire mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu. Chifukwa cha chikondi cha Mulungu wanu pa Israeli, ndi khumbo lake kuti akusungeni mpaka muyaya, Iye wayika inu kukhala mfumu yawo kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”

9Kenaka iyo inapereka kwa mfumu makilogalamu 4,000 a golide, zonunkhira zambirimbiri ndi miyala yokongola. Nʼkale lomwe sikunaonekenso zonunkhiritsa ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapereka kwa mfumu Solomoni.

10(Anthu a Hiramu ndi anthu a Solomoni anabweretsa golide kuchokera ku Ofiri ndipo anabweretsanso mitengo ya mʼbawa ndi miyala yokongola. 11Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya mʼbawa pokonzera makwerero a Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndiponso kupangira anthu oyimba apangwe ndi azeze. Zinthu zonga zimenezi sizinaonekeponso mu Yuda).

12Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha ndipo Solomoni anayipatsa mfumuyo zoposa zimene iyo inabweretsa kwa Solomoni. Ndipo mfumuyo inabwerera ku dziko lake pamodzi ndi atumiki ake.

Ulemerero wa Mfumu Solomoni

13Kulemera kwa golide amene Solomoni amalandira pa chaka kunali makilogalamu 23,000, 14osawerengera amene ankabwera ndi anthu ochita malonda ndi osinthanitsa zinthu. Komanso mafumu onse a ku Arabiya ndi abwanamkubwa a mʼdzikomo amabweretsa golide ndi siliva kwa Solomoni.

15Mfumu Solomoni inapanga zishango zazikulu 200 zagolide wosasantha. Mʼchishango chilichonse mumalowa golide wolemera makilogalamu asanu ndi awiri. 16Iye anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide wosasantha ndipo chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu. Mfumu inayika zishangozi mʼnyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.

17Ndipo mfumu inapanganso mpando waukulu waufumu wa nyanga za njovu ndipo unakutidwa ndi golide woyengeka bwino. 18Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi ndi choyikapo mapazi cholumikizidwa ku mpandowo. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, ndi chifanizo cha mkango chitayima posanjikapo manjapo. 19Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi imodzi aja. Umodzi mbali ina ya khwerero ndi wina mbali inayo. Palibe mpando wonga uwu umene unapangidwapo mu ufumu wina uliwonse. 20Zikho zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndiponso zipangizo zonse za ku nyumba yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide oyengeka bwino. Panalibe chinthu chopangidwa ndi siliva, chifukwa siliva samayesedwa kanthu mʼnthawi ya Solomoni. 21Mfumu inali ndi sitima zambiri zapamadzi zimene zimayendetsedwa ndi antchito a Hiramu. Zimabwera kamodzi pa zaka zitatu zilizonse zitanyamula golide, siliva ndi nyanga za njovu, ndiponso anyani ndi apusi.

22Mfumu Solomoni anapambana mafumu ena onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru. 23Mafumu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuonana ndi Solomoni kuti adzamve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake. 24Chaka ndi chaka, aliyense amene amabwera, amabweretsa mphatso monga zipangizo zasiliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya komanso akavalo ndi abulu.

25Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo ndi magaleta, ndi akavalo 12,000 amene amawasunga mʼmizinda yosungira magaleta ndiponso ena anali ndi iye ku Yerusalemu. 26Iye ankalamulira mafumu onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika ku malire a dziko la Igupto. 27Mfumu inasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba mu Yerusalemu ndipo mikungudza kukhala yochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa. 28Solomoni ankayitanitsa akavalo ake kuchokera ku Igupto ndi mayiko ena onse.

Kumwalira kwa Solomoni

29Tsono ntchito zina zonse za Solomoni, kuyambira pachiyambi mpaka kumaliza, kodi sizinalembedwa mʼbuku la mbiri la mneneri Natani, ndi mʼbuku la uneneri wa Ahiya wa ku Silo ndi mʼbuku la masomphenya a mlosi Ido, lokamba za Yeroboamu mwana wa Nebati? 30Solomoni analamulira Aisraeli onse ku Yerusalemu zaka makumi anayi. 31Ndipo anamwalira nagona ndi makolo ake. Anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.

King James Version

2 Chronicles 9:1-31

1And when the queen of Sheba heard of the fame of Solomon, she came to prove Solomon with hard questions at Jerusalem, with a very great company, and camels that bare spices, and gold in abundance, and precious stones: and when she was come to Solomon, she communed with him of all that was in her heart. 2And Solomon told her all her questions: and there was nothing hid from Solomon which he told her not. 3And when the queen of Sheba had seen the wisdom of Solomon, and the house that he had built, 4And the meat of his table, and the sitting of his servants, and the attendance of his ministers, and their apparel; his cupbearers also, and their apparel; and his ascent by which he went up into the house of the LORD; there was no more spirit in her.9.4 cupbearers: or, butlers 5And she said to the king, It was a true report which I heard in mine own land of thine acts, and of thy wisdom:9.5 report: Heb. word9.5 acts: or, sayings 6Howbeit I believed not their words, until I came, and mine eyes had seen it: and, behold, the one half of the greatness of thy wisdom was not told me: for thou exceedest the fame that I heard. 7Happy are thy men, and happy are these thy servants, which stand continually before thee, and hear thy wisdom. 8Blessed be the LORD thy God, which delighted in thee to set thee on his throne, to be king for the LORD thy God: because thy God loved Israel, to establish them for ever, therefore made he thee king over them, to do judgment and justice. 9And she gave the king an hundred and twenty talents of gold, and of spices great abundance, and precious stones: neither was there any such spice as the queen of Sheba gave king Solomon. 10And the servants also of Huram, and the servants of Solomon, which brought gold from Ophir, brought algum trees and precious stones.9.10 algum…: also called, almug trees 11And the king made of the algum trees terraces to the house of the LORD, and to the king’s palace, and harps and psalteries for singers: and there were none such seen before in the land of Judah.9.11 terraces: or, stairs: Heb. highways 12And king Solomon gave to the queen of Sheba all her desire, whatsoever she asked, beside that which she had brought unto the king. So she turned, and went away to her own land, she and her servants.

13¶ Now the weight of gold that came to Solomon in one year was six hundred and threescore and six talents of gold; 14Beside that which chapmen and merchants brought. And all the kings of Arabia and governors of the country brought gold and silver to Solomon.9.14 governors: or, captains

15¶ And king Solomon made two hundred targets of beaten gold: six hundred shekels of beaten gold went to one target. 16And three hundred shields made he of beaten gold: three hundred shekels of gold went to one shield. And the king put them in the house of the forest of Lebanon. 17Moreover the king made a great throne of ivory, and overlaid it with pure gold. 18And there were six steps to the throne, with a footstool of gold, which were fastened to the throne, and stays on each side of the sitting place, and two lions standing by the stays:9.18 stays: Heb. hands 19And twelve lions stood there on the one side and on the other upon the six steps. There was not the like made in any kingdom.

20¶ And all the drinking vessels of king Solomon were of gold, and all the vessels of the house of the forest of Lebanon were of pure gold: none were of silver; it was not any thing accounted of in the days of Solomon.9.20 pure: Heb. shut up9.20 none were of silver: or, there was no silver in them 21For the king’s ships went to Tarshish with the servants of Huram: every three years once came the ships of Tarshish bringing gold, and silver, ivory, and apes, and peacocks.9.21 ivory: or, elephants’ teeth 22And king Solomon passed all the kings of the earth in riches and wisdom.

23¶ And all the kings of the earth sought the presence of Solomon, to hear his wisdom, that God had put in his heart. 24And they brought every man his present, vessels of silver, and vessels of gold, and raiment, harness, and spices, horses, and mules, a rate year by year.

25¶ And Solomon had four thousand stalls for horses and chariots, and twelve thousand horsemen; whom he bestowed in the chariot cities, and with the king at Jerusalem.

26¶ And he reigned over all the kings from the river even unto the land of the Philistines, and to the border of Egypt.9.26 river: that is, Euphrates 27And the king made silver in Jerusalem as stones, and cedar trees made he as the sycomore trees that are in the low plains in abundance.9.27 made silver: Heb. gave silver 28And they brought unto Solomon horses out of Egypt, and out of all lands.

29¶ Now the rest of the acts of Solomon, first and last, are they not written in the book of Nathan the prophet, and in the prophecy of Ahijah the Shilonite, and in the visions of Iddo the seer against Jeroboam the son of Nebat?9.29 book: Heb. words 30And Solomon reigned in Jerusalem over all Israel forty years. 31And Solomon slept with his fathers, and he was buried in the city of David his father: and Rehoboam his son reigned in his stead.