2 Mbiri 22 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 22:1-12

Ahaziya Mfumu ya Yuda

1Anthu a mu Yerusalemu anayika Ahaziya mwana wamngʼono kwambiri wa Yehoramu kukhala mfumu mʼmalo mwake, popeza gulu lankhondo limene linabwera ndi Aarabu ku misasa, linapha ana onse aakulu. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira.

2Ahaziya anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Dzina la amayi ake linali Ataliya, chidzukulu cha Omuri.

3Nayenso anayenda mʼnjira ya banja la Ahabu, pakuti amayi ake anamulimbikitsa kuchita zolakwika. 4Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe banja la Ahabu linachitira, pakuti atamwalira abambo ake, iwo anakhala alangizi ake, kumene kunali kudziwononga kwake. 5Iyeyo anatsatiranso uphungu wawo pamene anapita ndi Yehoramu, mwana wa Ahabu, mfumu ya Israeli kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yehoramu, 6kotero iye anabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene anamuvulaza ku Ramoti pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aaramu.

Ndipo Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anapita ku Yezireeli kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu chifukwa anavulazidwa.

7Mulungu anakonza kuti Ahaziya akaphedwe pa ulendo wake wokacheza. Ahaziya atafika, iye ndi Yoramu anapita kukakumana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamudzoza kuti akawononge banja la Ahabu. 8Pamene Yehu ankalanga banja la Ahabu anapeza atsogoleri a ku Yuda ndiponso ana aamuna a abale ake a Ahaziya amene amatumikira Ahaziya, ndipo anawapha. 9Kenaka anapita kukafunafuna Ahaziya, ndipo anthu ake anagwira Ahaziya pamene amabisala mu Samariya. Anabwera naye kwa Yehu ndipo anaphedwa. Iwo anamuyika mʼmanda, pakuti anati, “Iyeyu anali mwana wa Yehosafati amene anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” Kotero panalibe wamphamvu mʼbanja la Ahaziya kuti nʼkukhala mfumu.

Ataliya ndi Yowasi

10Ataliya, amayi ake a Ahaziya, ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakapha onse a banja laufumu la Yuda. 11Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, momuba ndi kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene amati aphedwe ndipo anamuyika iye ndi mlezi wake mʼchipinda chogona. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa wansembe Yehoyada, yemwe anali mlongo wake wa Ahaziya anamubisa mwanayo kuti Ataliya asamuphe. 12Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi iwo mu Nyumba ya Mulungu kwa zaka zisanu ndi chimodzi muulamuliro wa Ataliya.

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

2 Летопись 22:1-12

Охозия – царь Иудеи

(4 Цар. 8:25-29; 9:14-29)

1Жители Иерусалима сделали Охозию, младшего сына Иорама, царём вместо него, потому что люди, которые ворвались вместе с арабами в лагерь, перебили всех его старших сыновей. Так над Иудеей начал царствовать Охозия, сын Иорама.

2Охозии было двадцать два года, когда он стал царём, и правил он в Иерусалиме один год. Его мать звали Аталия, она была внучкой Омри. 3Он тоже ходил путями дома Ахава, потому что мать была ему советчицей на злые дела. 4Он делал зло в глазах Вечного по примеру дома Ахава, который стал ему, на его же погибель, советником после смерти его отца. 5Это их совету он следовал, отправляясь с царём Исроила Иорамом, сыном Ахава, воевать против Хазаила, царя Сирии, под Рамот Галаадский. Сирийцы ранили Иорама, 6и он вернулся в Изреель, чтобы оправиться от ран, нанесённых ему при Рамоте в битве с Хазаилом, царём Сирии.

Тогда иудейский царь Охозия, сын Иорама, отправился в Изреель навестить Иорама, сына Ахава, потому что тот был ранен. 7Но в воле Всевышнего было то, чтобы гибель Охозии произошла во время его прихода к Иораму. Когда Охозия пришёл, он вышел с Иорамом навстречу Иеву, сыну Нимши, которого Вечный помазал22:7 Посредством обряда помазания человек посвящался на определённое служение. Такого помазания удостаивались пророки, цари и священнослужители., чтобы истребить дом Ахава. 8Исполняя приговор дому Ахава, Иеву нашёл приближённых царя Иудеи и племянников Охозии, которые сопровождали Охозию, и перебил их. 9Затем он отправился на поиски Охозии, и его люди схватили Охозию, когда тот прятался в Сомарии. Он был приведён к Иеву и казнён. Его удостоили похорон, потому что говорили: «Он был сыном Иосафата, который всем сердцем искал Вечного». Так из дома Охозии не осталось никого, кто был бы в силах удержать царскую власть.

Попытка Аталии истребить дом Довуда

(4 Цар. 11:1-3)

10Когда Аталия, мать Охозии, увидела, что её сын мёртв, она встала и убила всю царскую семью Иудеи. 11Но Иехошева, дочь царя Иорама, взяла Иоаша, сына Охозии, выкрала его из среды царских сыновей, которых должны были убить, и спрятала его вместе с кормилицей в спальне. Так Иехошева, дочь царя Иорама и жена священнослужителя Иодая, сестра Охозии, укрыла ребёнка от Аталии, и та не смогла его убить. 12Он прятался у них в храме Всевышнего шесть лет, пока Аталия правила страной.