2 Mbiri 2 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 2:1-18

Kukonzekera Kumanga Nyumba ya Mulungu

1Solomoni anatsimikiza zoti amange Nyumba ya Dzina la Yehova ndi nyumba yake yaufumu. 2Iye analemba ntchito anthu 70,000 onyamula katundu ndi anthu 80,000 okumba miyala ku mapiri ndiponso akapitawo 3,600 oyangʼanira anthuwo.

3Solomoni anatumiza uthenga uwu kwa Hiramu mfumu ya ku Turo:

“Munditumizire mitengo ya mkungudza monga munachitira ndi abambo anga pamene munawatumizira mitengo ya mkungudza yomangira nyumba yaufumu yokhalamo. 4Tsono ine ndikufuna kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wanga ndi kuyipereka kwa Iye kuti tiziyikamo buledi wopatulika nthawi zonse ndiponso kuperekeramo nsembe zopsereza mmawa uliwonse ndi madzulo ndi pa masabata ndi pa masiku a chikondwerero cha mwezi watsopano ndiponso pa masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova Mulungu wathu, monga mwa malamulo a Aisraeli mpaka muyaya.

5“Nyumba ya Mulungu imene ndidzamange idzakhala yayikulu, chifukwa Mulungu wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse. 6Koma ndani angathe kumumangira Iye Nyumba, pakuti mlengalenga, ngakhale kumwamba kwenikweni sikungamukwane? Tsono ine ndine yani kuti ndimangire Iyeyo Nyumba, kupatula malo chabe opserezerapo nsembe pamaso pake?

7“Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, nsalu yapepo ndi yofiira ndi yobiriwira ndiponso waluso losema, kuti adzagwire ntchito mu Yuda ndi Yerusalemu pamodzi ndi anthu aluso amene abambo anga Davide anandipatsa.

8“Munditumizirenso mitengo ya mkungudza, payini ndiponso matabwa a mʼbawa wa ku Lebanoni, pakuti ndikudziwa kuti anthu anu ali ndi luso locheka matabwa kumeneko. Antchito anga adzagwira ntchito pamodzi ndi antchito anu 9kuti andipatse matabwa ambiri, chifukwa Nyumba imene ndikumanga iyenera kukhala yayikulu ndi yokongola. 10Ine ndidzalipira antchito anu amene adzacheke matabwa matani 1,000 a tirigu wopunthapuntha, matani 2,000 a barele, malita 440,000 a vinyo, ndiponso malita 440,000 a mafuta a olivi.”

11Hiramu, mfumu ya ku Turo, anamuyankha Solomoni pomulembera kalata kuti,

“Chifukwa Yehova amakonda anthu ake, wayika iwe kukhala mfumu yawo.”

12Ndipo Hiramu anawonjezera kunena kuti,

“Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi! Iye wamupatsa Davide mwana wanzeru, wodzaza ndi luntha ndi wozindikira, amene adzamanga Nyumba ya Mulungu ndi kudzimangira yekha nyumba yaufumu.

13“Ine ndikukutumizira Hiramu Abi, munthu wa luso lalikulu, 14amene amayi ake anali wochokera ku Dani ndipo abambo ake anali a ku Turo. Iye anaphunzitsidwa kugwira ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, miyala yokongola ndi matabwa, ndiponso nsalu zofewa zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Alinso ndi luso la zosemasema ndipo atha kupanga chilichonse chimene wapatsidwa. Iye adzagwira ntchito ndi amisiri anu ndi a mbuye wanga, Davide abambo anu.

15“Tsono mbuye wanga tumizirani antchito anu tirigu ndi barele, mafuta a olivi ndi vinyo zimene mwalonjeza, 16ndipo ife tidzadula mitengo yonse imene mukuyifuna kuchokera ku Lebanoni ndipo tidzayimanga pamodzi ndi kuyiyadamitsa pa madzi mpaka ku Yopa. Ndipo inu mudzatha kuyitenga mpaka ku Yerusalemu.”

17Solomoni anawerenga alendo onse amene anali mu Israeli, potsatira chiwerengero chimene abambo ake Davide anachita ndipo panapezeka kuti analipo anthu 153,600. 18Iye anayika anthu 70,000 kuti akhale onyamula katundu ndi anthu 80,000 kuti akhale ophwanya miyala mʼmapiri, anthu 3,600 anawayika kukhala akapitawo oyangʼanira anthu pa ntchitoyo.

Bibelen på hverdagsdansk

2. Krønikebog 2:1-17

1Til arbejdet udskrev han 80.000 mænd til at hugge stenblokke i bjergene, 70.000 mænd til at transportere stenene og 3600 arbejdsformænd.

2Salomon sendte følgende brev til kong Hiram2,2 Eller: „Huram”. Stavemåden varierer i de forskellige håndskrifter. af Tyrus: „Send mig noget cedertræ, som det du sendte til min far, da han byggede sit palads. 3Jeg skal nemlig til at bygge et tempel til ære for Herren, min Gud. Der vil jeg brænde røgelse for ham, fremlægge de hellige brød og ofre brændofre hver morgen og aften, samt på sabbatten, ved nymånefesten og de andre årlige fester som Herren, vores Gud, har fastlagt. Han har sagt, at vi altid skal holde disse fester. 4Det skal være et prægtigt tempel, som passer til en mægtig Gud, der er større end alle andre guder. 5Og dog, hvordan skulle jeg kunne bygge en bolig, som er Gud værdig, når ikke engang Himlen kan rumme hans storhed? Det eneste, jeg kan bygge for Gud, er et sted, hvor vi kan bringe ofre og tilbede ham.

6Send mig derfor en dygtig kunsthåndværker, som kan arbejde i guld, sølv, bronze og jern, som kan fremstille blåt, rødt og purpurfarvet klæde, og som er god til gravering. Han skal arbejde side om side med de kunsthåndværkere i Jerusalem og Judas land, som min far David udpegede. 7Send mig ceder-, cypres- og sandeltræ fra Libanons skove. Jeg vil sende nogle af mine folk, som kan hjælpe dine fortræffelige skovhuggere med arbejdet. 8Der er brug for en stor mængde tømmer, for jeg har i sinde at bygge et stort og prægtigt tempel. 9Til at bespise skovhuggerne vil jeg så give dig 20.000 sække hvede, 20.000 sække byg, 20.000 ankre2,9 Vi har oversat det hebraiske kor, som svarer til ca. 220 liter, med „sæk”, og det hebraiske bat, som svarer til ca. 22 liter, med „anker”. med vin og 20.000 ankre med olivenolie.”

10Kong Hiram svarede med følgende brev: „Når Herren har gjort dig til konge, må det være, fordi han elsker sit folk! 11Lovet være Herren, Israels Gud, som skabte himlen og jorden, og som har givet David en intelligent og dygtig søn til at bygge et tempel til Herren og et palads til sig selv.

12-13Jeg sender dig en dygtig kunsthåndværker ved navn Huram-Abi. Denne fremragende mand er søn af en jødisk kvinde fra Dan i Israel, men hans far er her fra Tyrus. Han er uddannet til at arbejde med guld, sølv, bronze, jern, sten, træ og linned, samt blåt, rødt og purpurfarvet klæde. Han har erfaring inden for al slags gravering og kan udføre enhver opgave, han præsenteres for. Han kan hjælpe dine kunsthåndværkere og dem, min herre David udpegede. 14Du må gerne sende den hvede, byg, olivenolie og vin, du tilbød, 15så skal vi straks i Libanons bjerge hugge alt det tømmer, du har brug for, og sende det ned langs kysten som tømmerflåder til Jafo, hvorfra du kan fragte det videre til Jerusalem.”

16Salomon foretog derefter en optælling af alle udlændinge, som boede i landet, sådan som hans far tidligere havde gjort. Det samlede antal udlændinge var 153.600, 17og Salomon gav dem som før nævnt følgende opgaver: 80.000 skulle hugge stenblokke i bjergene, 70.000 skulle transportere stenene og 3600 skulle være arbejdsformænd.