2 Mbiri 17 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 17:1-19

Yehosafati Mfumu ya Yuda

1Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake ndipo anadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Israeli. 2Iye anayika magulu a asilikali mʼmizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, ndipo anamanga maboma mu Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Efereimu imene Asa abambo ake analanda.

3Yehova anali ndi Yehosafati chifukwa mʼzaka zoyambirira anatsatira makhalidwe a Davide abambo ake. Iye sanafunsire kwa Abaala. 4Koma anafunafuna Mulungu wa abambo ake ndipo anatsatira malamulo ake osati zochita za Israeli. 5Yehova anakhazikitsa kolimba ufumuwo mʼmanja mwake ndipo Ayuda onse anabweretsa mphatso kwa Yehosafati, kotero kuti anali ndi chuma ndi ulemu wambiri. 6Mtima wake anawupereka kutsatira Yehova, kuwonjezera apo, anachotsa malo onse achipembedzo ndi mafano a Asera mu Yuda.

7Mʼchaka chachitatu cha ufumu wake, iye anatuma akuluakulu ake Beni-Haili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya kukaphunzitsa mʼmizinda ya Yuda. 8Pamodzi ndi iwo panali Alevi ena: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobu-Adoniya ndiponso ansembe Elisama ndi Yehoramu. 9Iwo anaphunzitsa mu Yuda monse atatenga Buku la Malamulo a Yehova iwo anayenda mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndipo anaphunzitsa anthu.

10Kuopsa kwa Yehova kunali pa maufumu onse a mayiko oyandikana ndi Yuda, kotero kuti sanachite nkhondo ndi Yehosafati. 11Afilisti ena anabweretsa kwa Yehosafati mphatso ndi siliva ngati msonkho, ndipo Aarabu anabweretsa ziweto: nkhosa zazimuna 7,700 ndi mbuzi 7,700.

12Mphamvu za Yehosafati zinkakulirakulira. Iye anamanga malo otetezedwa ndi mizinda yosungiramo chuma mu Yuda 13ndipo anali ndi katundu wambiri mʼmizinda ya Yuda. Iye anayikanso asilikali odziwa bwino nkhondo mu Yerusalemu. 14Chiwerengero chawo potsata mabanja awo chinali chotere:

kuchokera ku Yuda, atsogoleri a magulu 1,000;

mtsogoleri Adina, anali ndi anthu 300,000 odziwa nkhondo;

15otsatana naye, mtsogoleri Yehohanani, anali ndi anthu 280,000;

16otsatana naye, Amasiya mwana wa Zikiri amene anadzipereka yekha kutumikira Yehova, anali ndi anthu 200,000.

17Kuchokera ku Benjamini:

Eliada, msilikali wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amene anali ndi mauta ndi zishango;

18otsatana naye, Yehozabadi, anali ndi anthu 180,000 okonzekera nkhondo.

19Awa ndi anthu amene ankatumikira mfumu osawerengera amene anawayika mʼmizinda yotetezedwa mʼdziko lonse la Yuda.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

歷代志下 17:1-19

猶大王約沙法

1亞撒的兒子約沙法繼位,他發憤圖強對抗以色列2他派兵駐守猶大所有的堅城,又把守備軍安置在猶大和他父親亞撒所征服的以法蓮各城邑。 3耶和華與約沙法同在,因為他效法他祖先大衛起初所行的,沒有尋求巴力4只尋求他父親的上帝,遵行祂的誡命,沒有效法以色列人的行為。 5因此,耶和華鞏固他的王位,所有的猶大人都向他進貢,他極有財富和尊榮。 6他專心遵行耶和華的道,剷除猶大境內的邱壇和亞舍拉神像。

7他在執政第三年委派官員便·亥伊勒俄巴底撒迦利雅拿坦業米該亞猶大各城教導民眾, 8與他們同去的還有利未示瑪雅尼探雅西巴第雅亞撒黑示米拉末約拿單亞多尼雅多比雅駝·巴多尼雅,還有祭司以利沙瑪約蘭9他們帶著耶和華的律法書,走遍猶大各城鎮教導民眾。 10猶大周圍的列國都懼怕耶和華,不敢與約沙法爭戰。 11一些非利士人向他進貢禮物和銀子,阿拉伯人也給他送來公綿羊和公山羊各七千七百隻。

12約沙法日漸強大,在猶大境內修建堡壘和儲貨城, 13猶大各城儲備大量物資。他又在耶路撒冷屯駐精兵, 14其人數按宗族記在下面。

猶大族有千夫長押拿,率領精兵三十萬; 15其次是千夫長約哈難,率領軍兵二十八萬; 16其次是自願事奉耶和華的細基利的兒子亞瑪斯雅,率領精兵二十萬。 17便雅憫族有勇士以利雅大,率領手持弓箭和盾牌的軍兵二十萬; 18其次是約薩拔,率領全副武裝的軍兵十八萬。 19以上都是服侍王的軍兵,不包括王派去駐守猶大各堅城的軍兵。