2 Mafumu 23 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 23:1-37

Yosiya Akonzanso Pangano

1Pamenepo mfumu inayitanitsa akuluakulu onse a ku Yuda ndi Yerusalemu. 2Mfumuyo inapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu ena onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inawerenga mawu onse a mʼBuku la Chipangano limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova, anthu onse akumva. 3Mfumu inayimirira pambali pa chipilala ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo, mawu ndi malangizo ake ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukwaniritsa mawu a mʼpanganoli, olembedwa mʼbukuli. Pamenepo anthu onse anadzipereka kutsatira panganoli.

4Mfumu inalamula wansembe wamkulu Hilikiya, ansembe othandizana naye ndi alonda a pa khomo kuti achotse mʼNyumba ya Yehova ziwiya zonse zopembedzera Baala ndi Asera ndiponso mafano a zinthu zamlengalenga. Yosiya anazitentha kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Chigwa cha Kidroni ndipo phulusa lake anapita nalo ku Beteli. 5Iye anachotsa ansembe a mafano amene anayikidwa ndi mafumu a Yuda kuti azifukiza lubani ku malo opembedzera mafano a ku mizinda ya ku Yuda ndi kumalo ozungulira Yerusalemu, amene ankafukiza lubani kwa Baala, dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi zinthu zonse zamlengalenga. 6Anachotsa fano la Asera mʼNyumba ya Yehova napita nalo kunja kwa Yerusalemu, ku Chigwa cha Kidroni, nalitentha kumeneko. Anapera fanolo ndi kukataya phulusa lake pa manda a anthu wamba. 7Iye anagwetsanso tinyumba ta ochita zachiwerewere, timene tinali mʼNyumba ya Yehova, kumene akazi ankalukirako mikanjo yovala popembedza Asera.

8Yosiya anabweretsanso ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda, nawononga malo opembedzera mafano, kuyambira ku Geba mpaka ku Beeriseba, kumene ansembe ankafukizako lubani. Anagwetsa nyumba za milungu zimene zinali pa chipata cha Yoswa, bwanamkubwa wa mzindawo, kumanzere kwa chipata cha mzinda. 9Ngakhale kuti ansembe a ku malo opembedzera mafanowo sanawalole kuti atumikire pa guwa lansembe la Yehova mu Yerusalemu, koma ankadya buledi wopanda yisiti pamodzi ndi ansembe anzawo.

10Mfumu Yosiya anawononganso Tofeti, amene anali ku Chigwa cha Hinomu, kuti wina aliyense asagwiritse ntchito malowo popereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto kwa Moleki. 11Anachotsa pa chipata cholowera ku Nyumba ya Yehova akavalo amene mafumu a Yuda anawapereka ngati nsembe kwa dzuwa. Akavalo anali pafupi ndi bwalo la chipinda cha mkulu wina wotchedwa Natani-Meleki. Ndipo Yosiya anatentha magaleta opembedzera dzuwa.

12Anagwetsa maguwa amene mafumu a Yuda anawamanga pa denga pafupi ndi chipinda chapamwamba cha Ahazi, ndiponso maguwa amene Manase anamanga mʼmabwalo awiri a Nyumba ya Yehova. Yosiya anawachotsa kumeneko nawaphwanya ndi kutaya zidutswa zake mʼChigwa cha Kidroni. 13Mfumuyo inawononga malo opembedzera mafano amene ali kummawa kwa Yerusalemu cha kumpoto kwa Phiri la Chiwonongeko. Maguwawa Solomoni mfumu ya Israeli inamangira Asitoreti, fano lalikazi lonyansa la Asidoni, Kemosi, fano lonyansa la Amowabu, ndi Moleki, fano lonyansa la anthu a ku Amoni. 14Yosiya anaphwanya miyala ya chipembedzo ndiponso anadula mitengo ya fano la Asera ndipo anakwirira malowo ndi mafupa a anthu.

15Ngakhalenso guwa lansembe la ku Beteli, malo opembedzera mafano amene anapanga Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli, Yosiya anawononga guwalo ndi malo opembedzera mafanowo. Iye anatentha malo opembedzera mafanowo ndi kuwapera ndipo anatenthanso fano la Asera. 16Kenaka Yosiya anayangʼanayangʼana ndipo ataona manda amene anali pomwepo, mʼmbali mwa phiri, analamula kuti afukule mandawo ndi kutulutsa mafupa kuti awatenthe paguwapo kuti alidetse, potsatira mawu a Yehova amene munthu wa Mulungu analoseratu za zimenezi.

17Mfumu inafunsa kuti, “Kodi chizindikiro cha manda chimene ndikuwaonawo ndi chayani?”

Anthu a mu mzindamo anayankha kuti, “Ndi chizindikiro cha manda a munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda amene ananeneratu zimene inu mwalichita guwa lansembe la Beteli.”

18Mfumuyo inati, “Alekeni manda amenewo, munthu asachotse mafupa ake.” Choncho anawasiya mafupa akewo pamodzi ndi mafupa a mneneri wa ku Samariya uja.

19Monga momwe Yosiya anachitira ku Beteli, anachotsa ndi kuwononga nyumba za milungu zonse ndi malo opembedzera mafano amene mafumu anamanga mʼmizinda ya ku Samariya omwe anakwiyitsa Yehova. 20Yosiya anapha ansembe onse amene ankatumikira ku malo opembedzera mafano, anawaphera pa maguwa awo ndi kutentha mafupa awo. Kenaka iye anapita ku Yerusalemu.

21Mfumu inalamula anthu onse kuti, “Chitani Chikondwerero cha Paska kulemekeza Yehova Mulungu wanu, motsatira zomwe zalembedwa mʼBuku la Chipangano.” 22Paska yotere inali isanachitikepo kuyambira nthawi ya oweruza amene anatsogolera Israeli, kapenanso nthawi yonse ya mafumu a Yuda sipanachitikenso Paska ngati imeneyo. 23Koma mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, Paska imeneyi anachitira Yehova mu Yerusalemu.

24Kuwonjezera apa, Yosiya anachotsa anthu a mawula, woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, milungu ya mʼnyumba, mafano ndiponso zinthu zonse zonyansa zopezeka mu Yuda ndi Yerusalemu. Iye anachita izi pokwaniritsa lamulo lolembedwa mʼbuku limene Hilikiya analipeza mʼNyumba ya Yehova. 25Yosiyayo asanalowe ufumu, ngakhale atamwalira, panalibenso mfumu ina yofanana naye imene inatembenukira kwa Yehova monga anachitira, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu zake zonse, motsatira Malamulo onse a Mose.

26Komabe Yehova sanachotse mkwiyo wake woopsa, umene anali nawo pa Yuda chifukwa cha zonse zimene anachita Manase poputa mkwiyo wa Mulungu. 27Choncho Yehova anati, “Ndidzawachotsanso anthu a ku Yuda pamaso panga monga ndinachotsera anthu a ku Israeli ndipo ndidzawukana mzinda wa Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha, pamodzi ndi Nyumba ino imene ndinati, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo.’ ”

28Ntchito zina za Yosiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?

29Yosiya akanali mfumu, Farao wotchedwa Neko, mfumu ya Igupto, anapita ku Mtsinje wa Yufurate kukathandiza mfumu ya ku Asiriya. Mfumu Yosiya anapita kukachita naye nkhondo, koma Neko anakumana naye ndi kumupha ku Megido. 30Atumiki a Yosiyayo ananyamula mtembo wake mu galeta kuchokera ku Megido mpaka ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda akeake. Ndipo anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namudzoza, ndipo iye analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.

Yehowahazi Mfumu ya Yuda

31Yehowahazi anakhala mfumu ali ndi 23 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Hamutali, mwana wa Yeremiya wa ku Libina. 32Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe anachitira makolo ake. 33Farao Neko anamuyika mʼndende ku Ribula mʼdziko la Hamati kuti asalamulirenso mu Yerusalemu. Farao analamula Yuda kuti azikhoma msonkho wa siliva wolemera makilogalamu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogalamu 34. 34Farao Neko anayika Eliyakimu mwana wa Yosiya kuti akhale mfumu mʼmalo mwa abambo ake Yosiya, ndipo anasintha dzina lake kukhala Yehoyakimu. Koma iye anatenga Yehowahazi kupita naye ku Igupto ndipo anakafera kumeneko. 35Yehoyakimu anapereka kwa Farao Neko siliva ndi golide amene anamufuna uja. Koma kuti iye apereke zimenezi, amankhometsa msonkho mʼdziko mwakemo ndipo amalandira siliva ndi golide kuchokera kwa anthu a mʼdzikomo molingana ndi chuma cha munthu aliyense.

Yehoyakimu Mfumu ya Yuda

36Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Zebuda, mwana wa Pedaya wa ku Ruma. 37Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe anachitira makolo ake.

New Russian Translation

4 Царств 23:1-37

Иосия обновляет завет народа с Богом

(2 Пар. 34:3-7, 29-33)

1Тогда царь созвал всех старейшин Иудеи и Иерусалима. 2Он пошел в дом Господа с народом Иудеи, жителями Иерусалима, священниками и пророками – со всем народом, от малого до великого. Он прочитал им вслух все слова книги завета, которую нашли в доме Господа. 3Царь стоял у колонны и заключил перед Господом завет, обещая следовать Господу, и исполнять Его повеления, предписания и установления от всего сердца и от всей души, и соблюдать этим слова завета, записанные в этой книге. И весь народ также заключил завет.

4Царь приказал первосвященнику Хелкии, священникам ниже званием и привратникам убрать из храма Господа все вещи, сделанные для Баала, Ашеры и звездного воинства. Он сжег их за пределами Иерусалима на полях долины Кедрон и перенес пепел в Вефиль. 5Он сместил жрецов, которых цари Иудеи поставили возжигать благовония в святилищах на возвышенностях, в городах Иудеи и вокруг Иерусалима, и возжигавших благовония Баалу, солнцу, луне, созвездиям и звездному воинству. 6Он вынес столб Ашеры из дома Господа в долину Кедрон и сжег его там. Он стер его в порошок и развеял на общенародном кладбище. 7Еще он разрушил дома, которые находились при доме Господа, где жили храмовые блудники23:7 Храмовые блудники – имеются в виду мужчины, занимавшиеся культовой проституцией, которая была неотъемлемой частью весьма распространенных в те дни языческих культов плодородия. и где женщины ткали для Ашеры.

8Иосия вывел всех священников из городов Иудеи и осквернил святилища на возвышенностях, где священники возжигали благовония, от Гевы до Вирсавии. Он разрушил святилища на возвышенностях при воротах – при входе в ворота Иисуса, правителя города, слева от городских ворот. 9Хотя священники из святилищ на возвышенностях и не служили при жертвеннике Господа в Иерусалиме, они все же ели пресный хлеб со своими собратьями-священниками.

10Он осквернил жертвенник Тофета, что в долине Бен-Гинном, чтобы никто не мог больше приносить там сыновей и дочерей в огненную жертву Молоху23:10 Молох – аммонитский бог, в жертвы которому приносились дети. По Закону за поклонение Молоху израильтянам грозила смертная казнь (см. Лев. 18:21; 20:2-5).. 11Он убрал от входа в дом Господень коней, которых цари Иудеи посвятили солнцу. Они стояли во дворе, рядом с покоями евнуха Нафан-Мелеха, на прилегающей земле. Затем Иосия сжег посвященные солнцу колесницы.

12Он сокрушил жертвенники, которые цари Иудеи воздвигли на крыше верхней комнаты Ахаза, и жертвенники, которые Манассия построил в двух дворах дома Господа. Он убрал их оттуда, разбил на куски и выбросил мусор в долину Кедрон. 13Еще царь осквернил святилища на возвышенностях восточнее Иерусалима, к югу от горы Гибели – те, что царь Израиля Соломон построил для Астарты23:13 Астарта – богиня любви и плодородия, богиня-воительница., омерзительной богини сидонян, Кемоша23:13 Кемош – божество, в жертвы которому приносились люди., омерзительного бога Моава, и Милхома, омерзительного бога народа Аммона. 14Иосия разбил на куски священные камни, срубил столбы Ашеры и покрыл их место человеческими костями.

15Даже жертвенник в Вефиле, святилище на возвышенности, возведенное Иеровоамом, сыном Навата, который склонил к греху Израиль, – даже этот жертвенник и святилище он разрушил. Он сжег святилище на возвышенности и стер его в порошок, и столб Ашеры тоже сжег. 16После этого Иосия поглядел вокруг и, увидев могилы на склоне холма, велел вынуть из них кости и сжечь их на жертвеннике, чтобы осквернить его, по слову Господа, сказанному Божьим человеком, который предрек все это.

17Царь спросил:

– Чей это могильный камень я вижу?

Жители города сказали:

– Это могила Божьего человека, который приходил из Иудеи и предсказал все то, что ты сделал с жертвенником Вефиля23:17 См. 3 Цар. 13..

18– Пусть он покоится, – сказал он. – Пусть никто не тревожит его кости.

И они пощадили его кости и кости пророка, который приходил из Самарии.

19Еще Иосия уничтожил все святилища на возвышенностях, которые были в городах Самарии, – их возвели цари Израиля, вызывая Господень гнев. Он сделал с ними то же, что в Вефиле. 20Иосия заколол всех жрецов этих23:20 Букв.: «возвышенностей». святилищ на жертвенниках и сжег на них человеческие кости. После этого он вернулся в Иерусалим.

Возобновление Пасхи

(2 Пар. 35:1, 18-19)

21Царь повелел народу:

– Празднуйте Пасху Господу, вашему Богу, как написано в книге завета.

22Со дней судей, которые возглавляли Израиль, во все дни царей Израиля и царей Иудеи такой Пасхи, как эта, не бывало. 23Но на восемнадцатом году правления царя Иосии эта Пасха Господу отмечалась в Иерусалиме.

О царствовании царя Иосии

24Еще Иосия уничтожил вызывателей умерших, и чародеев, домашних божков, идолов, и все прочие мерзости, которые нашлись в Иудее и в Иерусалиме. Он сделал это, чтобы исполнить требования Закона, написанного в книге, которую священник Хелкия нашел в доме Господа. 25Ни до Иосии, ни после него не было царя, подобного ему, который обратился бы к Господу, как сделал это он, всем сердцем, всей душой и всеми силами, по всему Закону Моисея.

26И все-таки Господь не отвратился от великой ярости Своего гнева, вспыхнувшего на Иудею из-за всего, что сделал, вызывая Его гнев, Манассия. 27Господь сказал:

– Я удалю от Себя и Иудею, как удалил Израиль, и отвергну этот город, Иерусалим, который Я избрал, и дом, о котором Я сказал: «Здесь будет Мое имя».

Смерть Иосии

(2 Пар. 35:20–36:1)

28Что же до прочих событий правления Иосии и всего, что он сделал, то разве не записаны они в «Книге летописей царей Иудеи»?

29Во время правления Иосии фараон Нехо23:29 Нехо II, правивший Египтом с 610 по 595 гг. до н. э., пошел на помощь Ашшурубаллиту II, последнему царю Ассирии, воевавшему с Вавилоном., царь Египта, пошел к реке Евфрату на помощь царю Ассирии. Царь Иосия выступил, чтобы сразиться с ним, но Нехо, встретившись с ним в Мегиддо, убил его. 30Слуги Иосии привезли его тело в колеснице из Мегиддо в Иерусалим и похоронили его в его гробнице. А народ страны взял сына Иосии Иоахаза, и помазал его царем вместо его отца.

Иоахаз – царь Иудеи

(2 Пар. 36:2-4)

31Иоахазу было двадцать три года, когда он стал царем, и правил он в Иерусалиме три месяца. Его мать звали Хамуталь, дочь Иеремии; она была родом из Ливны. 32Он делал зло в глазах Господа, во всем уподобляясь своим отцам.

33Фараон Нехо заковал его в кандалы в городе Ривле, в земле Хамата, чтобы он не правил больше в Иерусалиме, и обложил Иудею данью в сто талантов23:33 Около 3 400 кг. серебра и один талант23:33 Около 34 кг. золота. 34Фараон Нехо сделал Элиакима, сына Иосии, царем вместо его отца Иосии и переименовал его в Иоакима. А Иоахаза он увел в Египет, где тот и умер. 35Иоаким выплатил фараону Нехо серебро и золото, которое тот потребовал. Для этого он обложил страну налогом и взыскал с народа страны серебро и золото, оценив имущество каждого.

Иоаким – царь Иудеи

(2 Пар. 36:5-8)

36Иоакиму было двадцать пять лет, когда он стал царем, и правил он в Иерусалиме одиннадцать лет. Его мать звали Зевудда, она была дочерью Педаи, родом из Румы. 37Он делал зло в глазах Господа, во всем уподобляясь своим отцам.