1 Yohane 3 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yohane 3:1-24

1Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye. 2Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. 3Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.

4Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo. 5Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo. 6Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa.

7Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama, monga Khristu ali wolungama. 8Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi. 9Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu. 10Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.

Kukondana Wina ndi Mnzake

11Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake. 12Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama. 13Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu. 14Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. 15Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.

16Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu. 17Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? 18Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi. 19Pamenepo tidzadziwa kuti tili pa choonadi ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu, 20nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa. Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse.

21Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu. 22Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa. 23Ndipo lamulo lake ndi ili: kukhulupirira dzina la Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga Iye anatilamulira. 24Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.

New Serbian Translation

1. Јованова 3:1-24

Деца Божија

1Погледајте колику нам је љубав Отац даровао: толику да се зовемо Божијом децом, као што и јесмо. Свет не зна ко смо ми, јер није упознао њега. 2Вољени моји, сад смо деца Божија, а шта ћемо постати то нам још није откривено. Међутим, знамо да ћемо када се он појави бити њему слични, јер ћемо га видети онаквог какав заиста јесте. 3И свако ко полаже ову наду у њега, чисти себе као што је он сам чист.

4Свако ко чини грех крши Закон, јер грех је безакоње. 5Ви знате да се Христос појавио да уклони грехе и да је он без греха. 6Нико ко остаје у њему не живи у греху, а ко живи у греху није га ни видео ни упознао.

7Дечице, не дајте да вас ко заведе. Свако ко чини правду, праведан је, као што је сам Христос праведан. 8Ко живи у греху, од ђавола је, јер ђаво греши од почетка. Син Божији је дошао због овога: да уништи дела ђаволска. 9Нико ко је од Бога рођен не живи у греху, зато што његово семе пребива у њему. Он не може да живи у греху, јер је рођен од Бога. 10По овоме се препознају Божија деца и ђавоља деца: ко год не чини правду и не воли свога брата, не припада Богу.

Волите један другога

11Ово је, наиме, порука коју сте чули од почетка: „Волите једни друге!“ 12Не будите као Кајин који је припадао Зломе, па је убио свога брата. И зашто га је убио? Зато што су његова дела била зла, а дела његовог брата праведна. 13Не чудите се, браћо, ако вас свет мрзи. 14Ми знамо да смо прешли из смрти у живот по томе што волимо браћу. Ко не воли, и даље је у смрти. 15Свако ко мрзи свог брата, јесте братоубица, а ви знате да ни један убица нема вечни живот у себи.

16Љубав смо познали по томе што је Христос положио свој живот за нас. Тако смо и ми дужни да положимо своје животе за браћу. 17Ако неко живи у благостању и види свога брата како оскудева, па остане равнодушан према њему, може ли у себи имати љубав према Богу? 18Дечице, немојмо волети само речју и језиком, већ делом и истином.

19По томе ћемо знати да припадамо истини, па ћемо умирити нашу савест пред Богом, 20ако нас савест у било чему осуђује. Јер, Бог је већи од наше савести и он зна све. 21Вољени моји, ако нас савест не осуђује, тада имамо поуздање пред Богом, 22па што год затражимо од њега то и добијамо, јер се његових заповести држимо и чинимо оно што је њему угодно. 23Ово је његова заповест: да верујемо у његовога Сина Исуса Христа и да волимо један другога онако како нам је заповедио. 24Ко држи његове заповести остаје у Богу, и Бог остаје у њему. А по овоме знамо да је он у нама: по Духу којег нам је даровао.