1 Petro 3 – CCL & SNC

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Petro 3:1-22

Akazi ndi Amuna

1Momwemonso, akazi inu gonjerani amuna anu kuti ngati ena a iwo sakhulupirira Mawu a Mulungu, akopeke ndi makhalidwe a akazi awo ndipo sipadzafunikanso mawu 2pamene aona moyo wanu wachiyero ndi moyo woopa Mulungu. 3Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa maonekedwe akunja, monga kuluka tsitsi ndi kuvala zokometsera zagolide ndi zovala zamberewere. 4Mʼmalo mwake kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa munthu wa mʼkatimo, kukongola kosatha kwa mtima ofatsa ndi mzimu wachete, zimene ndi za mtengowapatali pamaso pa Mulungu. 5Pakuti umo ndi mmene akazi oyera mtima akale amene anali ndi chiyembekezo pa Mulungu anadzikongoletsera. Iwo ankagonjera amuna awo, 6monga Sara, amene anamvera Abrahamu namutcha iye mbuye wake. Akazi inu ndinu ana ake ngati muchita zoyenera, ndipo musaope choopsa chilichonse.

7Momwemonso amuna inu, khalani mwanzeru ndi akazi anu, ndipo muwachitire ulemu monga anzanu ofowoka ndiponso olandira nanu pamodzi mphatso ya moyo wosatha, kuti pasakhale kanthu kotsekereza mapemphero anu.

Kumva Zowawa Chifukwa cha Chilungamo

8Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa. 9Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso. 10Pakuti,

“Iye amene angakonde moyo

ndi kuona masiku abwino,

aletse lilime lake kuyankhula zoyipa,

ndiponso milomo yake kunena mabodza.

11Apewe zoyipa, ndipo azichita zabwino.

Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuwupeza.

12Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama

ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo.

Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”

13Ndani angakuchitireni zoyipa ngati muchita changu kuchita zabwino? 14Koma ngakhale mumve zowawa chifukwa cha chilungamo, ndinu odala. “Musaope anthu, musachite mantha.” 15Koma lemekezani Khristu mʼmitima mwanu ngati Ambuye wanu. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense amene akufunsani za chiyembekezo chimene muli nacho. 16Koma chitani zimenezi mofatsa ndi mwaulemu, mukhale ndi chikumbumtima chosakutsutsani, kuti anthu ena akanena zoyipa za makhalidwe anu abwino mwa Khristu, achite okha manyazi ndi chipongwe chawocho. 17Nʼkwabwino ngati ndi chifuniro cha Mulungu kumva zowawa chifukwa chochita zabwino kusiyana ndi kumva zowawa chifukwa chochita zoyipa. 18Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu. 19Ndipo ali ngati mzimu chomwecho anapita ndi kukalalikira mizimu imene inali mʼndende, 20ya anthu amene sanamvere Mulungu atadikira moleza mtima pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. Mʼchombo chija anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, ndiwo anapulumutsidwa ku madzi. 21Madziwo akufanizira ubatizo umene lero ukukupulumutsaninso, osati chifukwa chochotsa litsiro la mʼthupi koma chifukwa cha chikumbumtima choona pamaso pa Mulungu. Umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu, 22amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.

Slovo na cestu

1. Petrův 3:1-22

Rady ohledně manželství

1-2Rovněž i vy, ženy, podřizujte se svým mužům, a když se někteří z nich vzpírají Božímu slovu, můžete je beze slov získat svým čistým a bohabojným životem.

3-4Nenakloníte si je vnějšími ozdobami – šperky, okázalými účesy a nákladnými oděvy, které nejsou pro vás vhodné, ale nepomíjející krásou křesťanské osobnosti. Vaší ozdobou nechť je jemnost a mírnost, které se líbí Bohu. 5Taková vnitřní krása zdobila zbožné ženy dávných dob, které se podřizovaly svým mužům. 6Vzpomeňte na Sáru, která poslouchala svého manžela Abrahama a nazývala ho svým pánem. Jdete její cestou, jedná-te-li správně a nepodléháte nervozitě a strachu.

7Tak i vy, muži, snažte se rozumět svým manželkám, neboť jsou slabší. Ctěte je, protože jsou z Boží milosti, stejně jako vy, dědičkami věčného života. Nejednáte-li tak, nemůžete čekat, že vaše modlitby budou vyslyšeny.

Utrpení při konání dobra

8Na závěr se obracím k vám všem; buďte jednomyslní, mějte porozumění jeden pro druhého a milujte se jako Boží rodina. Mějte citlivá srdce a pokornou mysl. 9Zlo neoplácejte zlem, urážky urážkami, ale naopak prokazujte dobro. Vždyť jedině tak vám Bůh může požehnat.

10Máte za úkol dokázat, že si vážíte života, a přejete-li si žít dobře a šťastně, dávejte pozor na svůj jazyk, aby z vašich úst nevyšlo nic špatného a lstivého. 11Obraťte se zády k zlému a čiňte dobro. Šiřte kolem sebe pokoj, i když to není snadné. 12Vždyť Pán se dívá s láskou na své poslušné děti a vyhovuje jejich prosbám. Na ty pak, kteří činí zlo, hledí s přísnou tváří.

13Kdo by měl zájem vám ublížit, když budete činit dobře? 14Stane-li se však, že budete trpět pro dobrou věc, Bůh vás odmění. Nenechte se zastrašit a nebuďte malomyslní; 15usilujte o to, aby vaše srdce patřila cele Kristu. Využijte každé příležitosti ke svědectví o vaší víře, hovořte však skromně a s úctou. 16Jednejte správně, aby ti, kteří o vás mluví jako o nejhorších lidech a nadávají vám, se zastyděli, že hanobí vaše křesťanské chování.

17Pamatujte, že dopustí-li Bůh, abyste trpěli, pak je lepší trpět pro dobro než pro zlo! 18Vždyť Kristus také trpěl. Sám bez viny – zemřel za naše hříchy, aby nás přivedl k Bohu. Jeho tělo bylo vydáno na smrt, ale Boží Duch jej vzkřísil. 19-20A týž Duch svatý zmocnil Noeho, když nesl Kristovo poselství záchrany těm, kteří před potopou byli pro svou nevěru v zajetí smrti. Bůh na ně trpělivě čekal, zatímco Noe stavěl koráb. Přesto jen osm lidí bylo zachráněno.

21To je předobraz křtu, který nyní zachraňuje vás. Při křtu vyznáváme, že jsme byli zachráněni před smrtí vzkříšením Ježíše Krista. Křest vyžaduje samozřejmě daleko více než pouhé obmytí tělesné špíny. Vyjadřuje skutečnost, že se obracíme k Bohu s prosbou, aby očistil naše svědomí od hříchu. 22Nyní je onen Kristus v nebi po Boží pravici a andělé i všechny nebeské síly se před ním sklánějí a poslouchají ho.