1 Mbiri 10 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 10:1-14

Sauli Adzipha Yekha

1Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. 2Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa. 3Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza.

4Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe, kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere ndi kudzandizunza ine.”

Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo. 5Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa. 6Motero Sauli ndi ana ake atatu anafa, pamodzi ndi banja lake lonse anafera limodzi.

7Pamene Aisraeli onse amene anali mʼchigwa anaona kuti gulu lankhondo lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo.

8Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa pa phiri la Gilibowa. 9Iwo anamuvula zovala zake, natenga mutu wake ndi zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo. 10Iwo anayika zida zake zankhondo mʼnyumba zopembedzera milungu yawo ndipo anapachika mutu wake mʼnyumba ya Dagoni.

11Pamene anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli, 12anthu awo onse olimba mtima anapita kukatenga mitembo ya Sauli ndi ana ake ndipo anabwera nayo ku Yabesi. Anakwirira mafupa awo pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.

13Sauli anafa chifukwa anali wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova, pakuti anakafunsira nzeru kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, 14sanafunsire nzeruzo kwa Yehova. Choncho Yehova anamupha ndi kupereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese.

Bibelen på hverdagsdansk

1. Krønikebog 10:1-14

Sauls død

1.Sam. 31,1-13

1Engang angreb filistrene israelitternes lejr på Gilboahøjen. Israels hær flygtede og efterlod mange faldne rundt om på højens skråninger. 2Filistrene satte efter Saul og hans sønner, Jonatan, Abinadab og Malkishua, og det lykkedes dem at dræbe sønnerne.

3Kampen rasede omkring Saul, og det lykkedes filistrenes bueskytter at få ram på ham. Han blev såret 4og råbte til sin våbendrager: „Træk dit sværd og gennembor mig, før de ugudelige og uomskårne filistre kommer og vanærer mig.” Men våbendrageren kunne ikke få sig selv til at dræbe Saul. Derfor tog Saul sit sværd og kastede sig mod det, så sværdet gennemborede ham. 5Da våbendrageren så, at Saul var død, fulgte han sin herres eksempel og kastede sig mod sit eget sværd. 6Den dag døde både Saul og hans tre sønner, og dermed var hans slægt uddød.

7Da de israelitter, der boede i dalen, blev klar over, at hæren var flygtet, og at Saul og hans sønner var døde, flygtede de fra deres byer, og filistrene overtog byerne.

8Næste dag drog filistrene ud for at plyndre de faldne, og de fandt Sauls og hans sønners lig på Gilboahøjen. 9Så tog de Sauls våben og huggede hovedet af ham, hvorefter de sendte sejrsbudskabet hjem til alle deres afgudstempler og landsmænd. 10Sauls våben blev udstillet på afgudstemplets væg, og hans hoved blev hængt op på Dagontemplets mur.

11Men da indbyggerne i Jabesh i Gilead hørte, hvad filistrene havde gjort ved Saul, 12drog deres tapre krigere af sted for at hente Sauls og hans sønners lig. De begravede dem under egetræet i Jabesh, hvorefter de sørgede og fastede i syv dage.

Hvorfor Saul døde

13Saul døde på grund af sin utroskab mod Herren. Han adlød ikke Herrens befalinger, men søgte endog råd hos en åndemaner. 14Han søgte ikke råd hos Herren, og derfor lod Herren ham dø og overgav riget til David, Isajs søn.