路加福音 17 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

路加福音 17:1-37

論罪、信心和本分

1耶穌教導門徒說:「引人犯罪的事是免不了的,但引人犯罪的人有禍了。 2誰使一個卑微的弟兄失足犯罪,他的下場比把大磨石拴在他脖子上扔到海裡還要慘。 3你們要小心謹慎!你的弟兄若犯了罪,要責備他。他若悔改,要饒恕他。 4就算他一天得罪你七次,每次都對你說,『我悔改』,你都要饒恕他。」

5使徒對主說:「請你加添我們的信心。」

6主說:「如果你們的信心像一粒芥菜種那麼大,便可對這棵桑樹說,『連根拔起,栽在大海裡!』它必服從你們。

7「你們誰會對種田或放羊回來的奴僕說,『請趕快坐下來吃飯』? 8不都是吩咐他『給我準備晚飯,束上腰帶伺候我用餐,等我吃完,你才可以吃』嗎? 9奴僕照著吩咐去做,主人會謝他嗎? 10同樣,你們照著吩咐把事情辦妥後,也該這樣說,『我們是無用的奴僕,所做的不過是分內的事。』」

十個痲瘋病人

11耶穌繼續前往耶路撒冷,途經撒瑪利亞加利利的交界處。 12祂進入一個村莊時,十個痲瘋病人迎面而來。他們遠遠地站著, 13高聲呼喊道:「耶穌,老師啊,求你可憐我們吧!」

14耶穌看見他們,就說:「去讓祭司察看你們的身體。」

他們去的時候,就潔淨了。 15其中一個發現自己痊癒了,就跑回來,高聲讚美上帝, 16又俯伏在耶穌的腳前連連稱謝。這人是撒瑪利亞人。

17耶穌說:「被醫好的不是有十個人嗎?其他九個呢? 18回來讚美稱頌上帝的只有這個外族人嗎?」 19於是祂對那人說:「起來回去吧!你的信心救了你。」

上帝國的降臨

20法利賽人問耶穌:「上帝的國什麼時候降臨?」

耶穌回答說:「上帝國的降臨並沒有看得見的徵兆。 21所以沒有人能說,『上帝的國在這裡』,或說,『在那裡』,因為上帝的國就在你們心裡17·21 在你們心裡」或作「在你們當中」。。」

22祂又對門徒說:「時候將到,你們將渴望見到人子降臨的日子,可是你們卻見不到。 23有人將對你們說,『看啊,祂在這裡!』或說,『看啊,祂在那裡!』你們不要出去,也不要追隨他們。 24因為人子降臨的時候必如劃過長空的閃電,從天這邊一直照亮到天那邊。 25但祂必須先受苦,被這個世代棄絕。

26「人子降臨時的情形將像挪亞的時代, 27人們吃喝嫁娶,一直到挪亞進入方舟那天,洪水來了,毀滅了他們; 28又像羅得的時代,人們吃喝、做買賣、耕地、蓋房。 29羅得離開所多瑪那天,烈火和硫磺從天而降,把他們全毀滅了。

30「人子顯現之日的情形也是如此。 31那天,在自己屋頂上的,不要下來收拾行李;在田裡工作的,也不要回家。 32你們要記住羅得妻子的事。 33想保全生命的,必喪失生命;喪失生命的,必保全生命。 34我告訴你們,那天晚上,兩個人睡在一張床上,一個將被接去,一個將被撇下; 35兩個女人一起推磨,一個將被接去,一個將被撇下; 36兩個人在田間,一個將被接去,一個將被撇下。17·36 有古卷無36節。

37門徒問:「主啊,在哪裡有這事呢?」

耶穌回答說:「屍體在哪裡,禿鷹就會聚集在哪裡。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Luka 17:1-37

Za Uchimo, Chikhulupiriro ndi Ntchito

1Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zinthu zimene zimachimwitsa sizingalephere kubwera, koma tsoka kwa munthu wozibweretsayo. 2Kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala wamphero mʼkhosi mwake kusiyana kuti achimwitse mmodzi mwa ana aangʼonowa. 3Nʼchifukwa chake dziyangʼanireni nokha.

“Ngati mʼbale wanu achimwa, mudzudzuleni, ndipo ngati alapa, mukhululukireni. 4Ngati iye akulakwira kasanu ndi kawiri pa tsiku, ndipo ngati nʼkubweranso kwa iwe kasanu ndi kawiri nati, ‘Ndalapa,’ umukhululukire.”

5Atumwiwo anati kwa Ambuye, “Kulitsani chikhulupiriro chathu!”

6Yesu anayankha kuti, “Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani.

7“Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu anali ndi wantchito wolima kapena woweta nkhosa, kodi angawuze wantchitoyo atabwera ku munda kuti, ‘Tsopano bwera kuno khala pansi kuti udye?’ 8Kodi sangamuwuze kuti, ‘Konzere chakudya cha madzulo, iweyo ukonzeke ndipo undidikirire pamene ndikudya ndi kumwa; kenaka ukhoza kudya ndi kumwa?’ 9Kodi iye angathokoze wantchitoyo chifukwa chochita chimene anawuzidwa kuchita? 10Chimodzimodzi inunso, mukachita zonse zimene munawuzidwa, muzinena kuti, ‘Ndife antchito osayenera; tangogwira ntchito yathu basi.’ ”

Yesu Achiritsa Akhate Khumi

11Tsopano Yesu anayenda mʼmalire a pakati pa Samariya ndi Galileya pa ulendo wake wa ku Yerusalemu. 12Akulowa mʼmudzi wina, amuna khumi amene anali ndi khate anakumana naye. Iwo anayima patali 13ndipo anafuwula ndi mawu okweza kuti, “Yesu, Ambuye, tichitireni chifundo!”

14Iye atawaona, anati, “Pitani kadzionetseni nokha kwa ansembe.” Ndipo pamene iwo ankapita, anachiritsidwa.

15Mmodzi wa iwo, ataona kuti wachiritsidwa, anabwerera, nayamika Mulungu ndi mawu okweza. 16Anagwetsa nkhope yake nagwa pa mapazi a Yesu ndi kumuthokoza. Ndipo iye anali Msamariya.

17Yesu anafunsa kuti, “Kodi amene anachiritsidwa sanalipo khumi? Nanga asanu ndi anayi ena ali kuti? 18Kodi palibe mmodzi mwa iwo amene anabwerera kudzalemekeza Mulungu kupatula mlendoyu?” 19Pamenepo anati kwa iye, “Imirira ndipo pita; chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe.”

Za Ufumu wa Mulungu

20Ndipo Afarisi atamufunsa Iye kuti, ufumu wa Mulungu udzabwera liti, Yesu anayankha kuti, “Mulungu sakhazikitsa ufumu wake mooneka ndi maso, 21kapenanso kuti anthu adzati, ‘Uwu uli apa,’ kapena ‘Uwo uli apo,’ Pakuti taonani ufumu wa Mulungu uli pakati panu.”

22Kenaka Iye anati kwa ophunzira ake, “Masiku akubwera pamene inu mudzalakalaka mutaona tsiku limodzi la masiku a Mwana wa Munthu, koma simudzaliona. 23Anthu adzakuwuzani kuti, ‘Uyo ali apoyo!’ kapena ‘Uyu ali apa!’ Musawathamangire iwo. 24Pakuti monga mphenzi ingʼanima ndi kuwala kuchokera mbali ina ya thambo kufikira inzake, koteronso adzakhala ali Mwana wa Munthu pa tsiku lake. 25Koma poyamba ayenera kuzunzika mu zambiri ndi kukanidwa ndi mʼbado uno.

26“Monga mmene zinkachitikira nthawi ya Nowa, momwemonso zidzachitikanso nthawi ya Mwana wa Munthu. 27Anthu ankadya, kumwa, kukwatira ndi kukwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchombo. Pomwepo chigumula chinafika ndi kuwawononga onsewo.

28“Zinalinso chimodzimodzi nthawi ya Loti. Anthu ankadya ndi kumwa, kugula ndi kugulitsa, kudzala ndi kumanga. 29Koma tsiku limene Loti anachoka ku Sodomu, moto ndi sulufule zinavumbwa kuchokera kumwamba ndi kuwawononga onsewo.

30“Zidzakhalanso choncho Mwana wa Munthu akadzaonekera. 31Tsiku limenelo munthu amene ali pa denga la nyumba yake, ndi katundu wake ali mʼnyumbamo, asadzatsike kukatenga. Chimodzimodzinso, munthu amene adzakhale ali ku munda asadzabwerere kukatenga chilichonse. 32Kumbukirani mkazi wa Loti! 33Aliyense amene ayesetsa kusunga moyo wake adzawutaya, ndipo aliyense amene ataya moyo wake adzawusunga. 34Ine ndikukuwuzani inu, usiku umenewo anthu awiri adzagona pa mphasa imodzi; wina adzatengedwa ndipo wina adzasiyidwa. 35Amayi awiri adzakhala pamodzi akusinja; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa. 36Amuna awiri adzakhala akulima mʼmunda; wina adzatengedwa ndi wina adzasiyidwa.”

37Iwo anafunsa kuti, “Ambuye, kodi zimenezi zidzachitikira kuti?”

Iye anayankha kuti, “Kumene kuli mtembo, nʼkumene makwangwala amasonkhanako.”