約翰一書 4 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

約翰一書 4:1-21

靈的分辨

1親愛的弟兄姊妹,不要什麼靈都信,總要試驗那些靈是否出於上帝,因為世上已經出現了許多假先知! 2任何靈若承認耶穌基督曾降世為人,就是從上帝來的,你們可以憑這一點認出上帝的靈。 3任何靈若不承認耶穌,就不是從上帝來的,而是敵基督者的靈。以前你們聽說敵基督者要來,現在他已經在世上了。

4孩子們,你們屬於上帝,你們已經勝過了那些假先知,因為在你們裡面的聖靈比在世上運行的邪靈更有能力。 5他們屬於世界,所以他們談論的都是世俗的事,世人也聽從他們。 6我們屬於上帝,認識上帝的人聽從我們,不屬於上帝的人不聽從我們。這樣,我們就可以分辨真理的靈和錯謬的靈。

上帝是愛

7親愛的弟兄姊妹,我們應當彼此相愛,因為愛是從上帝來的。凡有愛心的人都是從上帝生的,並且認識上帝。 8沒有愛心的人不認識上帝,因為上帝就是愛。 9上帝差遣祂獨一的兒子到世上來,是為了叫我們靠著祂得到生命。這就顯明了上帝對我們的愛。 10不是我們愛上帝,而是上帝愛我們,並且差遣祂兒子為我們的罪作了贖罪祭,這就是愛。

11親愛的弟兄姊妹,上帝既然這樣愛我們,我們也應該彼此相愛。 12從來沒有人見過上帝,如果我們彼此相愛,上帝就住在我們裡面,祂的愛就在我們裡面得到成全。

13上帝將祂的靈賜給了我們,所以我們知道自己住在祂裡面,祂也住在我們裡面。 14我們看見過,現在做見證:父差遣了祂的兒子成為世人的救主。 15無論是誰,他若承認耶穌是上帝的兒子,上帝必住在他裡面,他也住在上帝裡面。 16我們已經認識並且相信了上帝對我們的愛。

上帝就是愛,住在愛中的,就是住在上帝裡面,上帝也住在他裡面。 17這樣,愛在我們裡面得到成全,使我們在審判的日子可以坦然無懼,因為我們在這世上以基督為榜樣。 18愛裡沒有恐懼,純全的愛能驅除恐懼,因為恐懼意味著怕受懲罰。人若心裡恐懼,就表示他尚未明白那純全的愛。

19我們愛,因為上帝先愛了我們。 20若有人說「我愛上帝」,卻恨自己的弟兄姊妹,這人就是說謊話,因為人若不愛看得見的弟兄姊妹,又怎能愛看不見的上帝呢? 21愛上帝的人也應該愛弟兄姊妹,這是上帝給我們的命令。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Yohane 4:1-21

Kuyesa Mizimu

1Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi. 2Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu, 3koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi.

4Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi. 5Aneneri onyengawa ndi ochokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake amayankhula za dziko lapansi, ndipo dziko lapansi limawamvera. 6Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.

Mulungu ndiye Chikondi

7Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu. 8Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi. 9Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo. 10Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. 11Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake. 12Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.

13Ife tikudziwa kuti timakhala mwa Iye ndipo Iyeyo amakhala mwa ife chifukwa anatipatsa Mzimu wake. 14Ndipo taona ndipo tikuchitira umboni, kuti Atate anatuma Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi. 15Ngati aliyense avomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye ndipo iyeyo amakhala mwa Mulungu. 16Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife.

Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye. 17Chikondi chafika pachimake penipeni pakati pathu, kotero kuti pa tsiku lachiweruzo tidzakhala olimba mtima chifukwa mʼdziko lapansi moyo wathu uli ngati wa Khristu. 18Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro.

19Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda. 20Ngati wina anena kuti, “Ine ndimakonda Mulungu,” koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone. 21Ndipo Iye anatipatsa lamulo lakuti: Aliyense amene amakonda Mulungu ayenera kukondanso mʼbale wake.