利未記 7 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

利未記 7:1-38

祭司獻贖過祭的條例

1「以下是獻贖過祭的條例。

「贖過祭是至聖的。 2要在殺燔祭牲的地方宰贖過祭祭牲,祭牲的血要灑在祭壇周圍。 3要獻上祭牲的所有脂肪,包括肥尾巴、遮蓋內臟的脂肪、 4兩個腎臟和腎臟上靠近腰部的脂肪以及肝葉。 5祭司要在壇上焚燒這一切,作為獻給耶和華的火祭。這是贖過祭。 6祭司家的任何男子都可以吃剩下的祭肉,但要在聖潔之處吃,因為這是至聖之物。 7祭物要歸主持祭禮的祭司,這一條例也適用於贖罪祭。 8燔祭牲的皮要歸主持祭禮的祭司。 9至於素祭,不論是用爐烤的,還是用平底鍋或煎鍋做的,都要歸主持祭禮的祭司。 10但調油的或乾的素祭要歸亞倫的子孫,由他們均分。

獻平安祭的條例

11「以下是向耶和華獻平安祭的條例。

12「如果有人為感謝耶和華而獻平安祭,除了獻祭牲以外,要一同獻上調油的無酵餅、塗油的無酵薄餅及調油的細麵餅, 13也要一同獻上有酵餅。 14他要從每種餅中各取一個,作為舉祭獻給耶和華。舉祭歸灑平安祭祭牲血的祭司。 15至於祭牲的肉,要在獻祭的當天吃完,不可留到次日早晨。 16如果是自願獻的或為了還願而獻的祭物,要在當天吃祭肉,剩下的可以留到第二天吃。 17但到第三天,必須燒掉剩下的祭肉。 18如果第三天仍然吃,所獻的祭便不蒙悅納,毫無價值,是不潔淨的。吃的人要自擔罪責。

19「祭肉如果接觸到任何不潔之物,就不可以吃,要燒掉。潔淨的人都可以吃平安祭的祭肉。 20如果有人不潔淨,卻吃獻給耶和華的平安祭祭肉,要將他從民中剷除。 21如果有人接觸到人或獸的不潔之物,或任何不潔的可憎之物,又吃獻給耶和華的平安祭祭肉,要將他從民中剷除。」

22耶和華對摩西說: 23「你把以下條例告訴以色列人。

「你們不可吃牛、綿羊或山羊的脂肪。 24自然死亡或被野獸咬死的動物的脂肪也不可吃,但可以作其他用途。 25無論誰吃了獻給耶和華的火祭祭牲的脂肪,都要將他從民中剷除。 26你們無論住在哪裡,都不可吃鳥和獸的血。 27凡吃血的,要將他從民中剷除。」

28耶和華對摩西說: 29「你把以下條例告訴以色列人。

「凡向耶和華獻平安祭的,都要從平安祭中取出一份獻給耶和華作禮物。 30他要親手將這獻給耶和華的火祭帶來,將祭牲的脂肪和胸肉帶來,在耶和華面前將胸肉搖一搖,當作搖祭獻上。 31祭司要把脂肪放在壇上焚燒,胸肉歸亞倫及其子孫。 32你們要把祭牲的右腿獻為舉祭,歸給祭司。 33要把右腿歸給亞倫子孫中獻平安祭的血和脂肪的那位祭司。 34因為耶和華已經從以色列人獻的平安祭中,把作搖祭的胸肉和作舉祭的腿肉賜給祭司亞倫及其子孫。他們在以色列人中要永遠享有這一份。 35亞倫及其子孫受膏為祭司事奉耶和華開始,在獻給耶和華的火祭中,這是他們應得之份。 36祭司受膏之日,耶和華就命令以色列人把這部分祭肉分給他們,這是他們世世代代應得之份。」

37以上是獻燔祭、素祭、贖罪祭、贖過祭、平安祭和授聖職時所獻之祭的條例。 38這些條例是耶和華在西奈山上吩咐摩西的。同一天,摩西命令以色列人在西奈曠野向耶和華獻祭。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Levitiko 7:1-38

Nsembe Yopepesera Kupalamula

1“ ‘Malamulo a nsembe yopepesera kupalamula imene ndi nsembe yopatulika kwambiri ndi awa: 2Nsembe yopepesera machimo iziphedwa pamalo pomwe amaphera nsembe yopsereza ndipo awaze magazi ake mbali zonse za guwa. 3Tsono apereke mafuta ake onse: mchira wamafuta ndi mafuta amene amakuta matumbo. 4Aperekenso impsyo ziwiri, mafuta ake pamodzi ndi mafuta onse amene ali chamʼchiwuno, ndiponso mafuta onse amene aphimba chiwindi. 5Wansembe azitenthe pa guwa kuti zikhale nsembe yotentha pa moto, yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo lopalamula. 6Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kudyako nsembeyo koma adyere ku malo opatulika. Imeneyi ndi nsembe yopatulika kwambiri.

7“ ‘Nsembe yopepesera tchimo lopalamula ndi yofanana ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo. Ndipo nsembe ziwiri zonsezi zili ndi lamulo limodzi lokha. Wansembe amene wachita mwambo wa nsembe yopepesera machimo a kupalamula atenge nyamayo ngati yake. 8Wansembe wopereka nsembe yopsereza ya munthu wina aliyense, atenge chikopa cha nsembe yopserezayo kuti chikhale chake. 9Chopereka chilichonse cha chakudya chophika mu uvuni kapena chokazinga mu mʼphika kapena mu chiwaya ndi cha wansembe amene wapereka nsembezo. 10Ndipo chopereka china chilichonse cha chakudya chosakaniza ndi mafuta kapena chowuma, chikhale cha ana onse a Aaroni ndipo anawo achigawane mofanana.

Nsembe Yachiyanjano

11“ ‘Malamulo a nsembe ya chiyanjano imene munthu angathe kupereka kwa Yehova ndi awa:

12“ ‘Ngati munthuyo apereka chifukwa cha kuthokoza, apereke nsembeyo pamodzi ndi makeke wopanda yisiti, osakaniza ndi mafuta; timitanda ta buledi wopanda yisiti, topyapyala, topaka mafuta, ndiponso makeke a ufa wosalala wophikidwa bwino, wosakaniza ndi mafuta. 13Pamodzi ndi nsembe yachiyanjano yothokozerayo abwerenso ndi makeke opangidwa ndi yisiti ngati chopereka chake. 14Munthuyo atenge mtanda umodzi pa mtanda wa buledi wa mtundu uliwonse kuti ukhale nsembe yopereka kwa Yehova. Tsono mtanda umenewo ndi wake wa wansembe amene awaze magazi a nsembe yachiyanjano. 15Nyama ya nsembe yachiyanjano yothokozera idyedwe pa tsiku lomwe nsembeyo yaperekedwa ndipo isatsaleko mpaka mmawa.

16“ ‘Koma ngati nsembe yakeyo apereka chifukwa cha lumbiro kapena mwaufulu, nsembeyo adye tsiku lomwe yaperekedwalo. Koma yotsala angathe kuyidya mmawa mwake. 17Ngati nyama ina ya nsembe yatsalabe mpaka tsiku lachitatu, imeneyo itenthedwe pa moto. 18Ngati munthu adya nyama yachiyanjano pa tsiku lachitatu, nsembeyo sidzalandiridwa. Amene wayipereka nsembeyo Mulungu sadzamulandira ndipo nsembeyo idzakhala yonyansa pamaso pa Mulungu, yosamupindulira kanthu woperekayo.

19“ ‘Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa, munthu asayidye, koma itenthedwe pa moto. Aliyense amene ali woyeretsedwa angathe kudya nyama inayo. 20Koma ngati munthu wina amene ndi wosayeretsedwa adya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake. 21Ndipo ngati munthu wina akhudza chinthu chodetsedwa, kaya chonyansa cha munthu kapena cha nyama, kapenanso chonyansa china chilichonse, ndipo kenaka nʼkudya nyama ya nsembe yachiyanjano imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo achotsedwe pakati anthu a mtundu wake.’ ”

Za Kuletsa Kudya Mafuta ndi Magazi

22Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 23“Awuze Aisraeli kuti, ‘Musadye mafuta a ngʼombe, nkhosa kapenanso mbuzi. 24Mafuta a nyama yofa yokha, kapena mafuta a nyama yophedwa ndi zirombo akhoza kuwagwiritsa ntchito iliyonse, koma inu musadye mafuta amenewo. 25Pakuti munthu wakudya mafuta a nyama yoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe yotentha pa moto, ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu a mtundu wake. 26Ndipo kulikonse kumene mukakhale musakadye magazi a mbalame iliyonse kapena magazi a nyama iliyonse. 27Ngati munthu aliyense adya magazi achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake.’ ”

Gawo la Ansembe

28Yehova anayankhula ndi Mose kuti, 29“Awuze Aisraeli kuti, Aliyense amene apereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, abwere ndi gawo la nsembeyo kwa Yehova. 30Atenge ndi manja ake zigawo za chopereka zoyenera kuzitentha pa moto ngati chopereka kwa Yehova. Abweretse mafuta, pamodzi ndi chidale chomwe, ndipo chidalecho achiweyule kuti chikhale chopereka choweyula kwa Yehova. 31Wansembe atenthe mafutawo pa guwa koma chidalecho chikhale cha Aaroni ndi ana ake. 32Mumupatse wansembe ntchafu ya kumanja ya nsembe yanu yachiyanjano kuti ikhale chopereka chanu kwa iye. 33Mwana wa Aaroni amene amapereka magazi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano, adzitenga ntchafu ya kumanja kukhala gawo lake. 34Choncho pa zopereka zachiyanjano za Aisraeli, Ine ndatengapo chidale chomwe amaweyula ndi ntchafu zimene amapereka nsembe ndipo ndazipereka kwa wansembe Aaroni ndi ana ake. Izi ndizo gawo lawo nthawi zonse pa zopereka za Aisraeli.”

35Zimenezi ndi chigawo cha Aaroni ndi ana ake chotapidwa pa zopereka kwa Yehova zoti zitenthedwe pa moto zimene zinaperekedwa pa tsiku limene anapatulidwa kuti akhale ansembe otumikira Yehova. 36Yehova ndiye analamulira kuti pa zopereka za Aisraeli azitapapo zimenezi ndi kuwapatsa ansembe ngati gawo lawo. Yehovayo analamula zimenezi pa tsiku limene ansembewo anapatulidwa ndipo anachikhazikitsa ngati lamulo la nthawi zonse.

37Awa ndi malamulo a nsembe izi: nsembe yopsereza, nsembe yachakudya, nsembe yopepesera machimo, nsembe yopepesera kupalamula, nsembe ya mwambo wodzoza ndi nsembe yachiyanjano. 38Malamulo amenewa Yehova anapereka kwa Mose pa Phiri la Sinai pa tsiku limene Yehova analamulira Aisraeli kuti abwere ndi zopereka za kwa Yehova, ku chipululu cha Sinai kuja.