以西結書 14 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以西結書 14:1-23

斥責拜偶像的以色列人

1那時,幾位以色列的長老到我這裡來,坐在我面前。 2耶和華對我說: 3「人子啊,這些人在心裡立起偶像,把導致犯罪的絆腳石放在自己面前,我豈能讓他們來求問? 4你告訴他們,主耶和華這樣說,『任何以色列人若在心裡立起偶像,把導致犯罪的絆腳石放在自己面前,又來求問先知,我耶和華必按他心中假神的數目親自用懲罰回答他, 5好奪回以色列人的心,他們因為拜偶像而遠離我。』

6「因此,你要告訴以色列人,主耶和華這樣說,『你們要悔改,離棄你們的偶像,離棄那些可憎之事。 7因為以色列人或是在以色列定居的外族人若背棄我,在心中樹立偶像,把導致犯罪的絆腳石放在自己面前,又來向先知求問我的旨意,我耶和華必親自用懲罰回答他。 8我必嚴懲他,使他成為眾人的鑒戒和笑柄。我必將他從我的子民中剷除。這樣,你們就知道我是耶和華。 9如果先知受迷惑說預言,那是我耶和華任他胡作非為,我必伸手懲治他,把他從我的以色列百姓中除滅。 10他們必擔當自己的罪過——假先知與求問的人要擔當同樣的罪過。 11這樣,以色列人便不再偏離我,不再犯罪玷污自己。他們要做我的子民,我要做他們的上帝。這是主耶和華說的。』」

12耶和華對我說: 13「人子啊,若有國家犯罪背叛我,我必伸手斷絕他們的糧源,使饑荒遍地,毀滅人和牲畜。 14即使挪亞但以理約伯三人在那裡,他們也只能因義行而自己得救。這是主耶和華說的。 15倘若我使猛獸在那裡橫行、肆虐,以致那裡荒涼、人蹤絕跡, 16縱然這三個義人在那裡,我憑我的永恆起誓,他們也不能救自己的兒女,只能自己得救,那裡卻要荒涼。這是主耶和華說的。 17倘若我使刀劍臨到那裡,毀滅人和牲畜, 18縱然這三個義人在那裡,我憑我的永恆起誓,他們也不能救自己的兒女,只能自己得救。這是主耶和華說的。 19倘若我叫瘟疫在那裡肆虐,發烈怒毀滅那裡的人和牲畜, 20縱然挪亞但以理約伯在那裡,我憑我的永恆起誓,他們也不能救自己的兒女,只能因義行而自己得救。這是主耶和華說的。

21「主耶和華說,『我要把戰禍、饑荒、猛獸和瘟疫這四大刑罰降在耶路撒冷,毀滅人和牲畜。 22然而,其中仍有倖免的人帶著兒女逃出來。他們會逃到你們這裡,你們看見他們的所作所為,便會對我在耶路撒冷所降的一切災難感到欣慰。 23你們看見他們的所作所為,就知道我不是無緣無故地懲罰耶路撒冷。』這是主耶和華說的。」

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 14:1-23

Yehova Adzudzula Opembedza Mafano

1Tsiku lina ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kwa ine ndipo anakhala pansi pamaso panga. 2Ndipo Yehova anandipatsa uthenga uwu nati, 3“Iwe mwana wa munthu, anthu awa ayika mtima pa mafano awo. Ayikanso maso awo pa zinthu zina zoyipa zopunthwitsa. Kodi ayembekezera kuti ndiwayankhe chimene atandifunse? 4Tsono yankhula nawo ndi kuwawuza kuti zimene akunena Ambuye Yehova: ‘Ngati Mwisraeli aliyense ayika mtima wake pa mafano ndi kuyika maso ake pa zinthu zoyipa zopunthwitsa, kenaka nʼkupita kwa mneneri, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha molingana ndi kuchuluka kwa mafano ake. 5Ine ndidzachita zimenezi kuti mwina nʼkukopa mitima ya anthu a Israeli, amene andisiya chifukwa cha mafano awo.’

6“Nʼchifukwa chake uwawuze Aisraeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Lapani! Siyani mafano anu ndi ntchito zanu zonse zonyansa!

7“ ‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha. 8Ine ndidzalimbana naye munthu ameneyo ndipo ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo. Ndidzamuchotsa pakati pa anthu anga. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

9“ ‘Ndipo ngati mneneri anyengedwa nanenera, Ine Yehova ndiye ndamunyenga mneneri ameneyo, ndipo ndidzatambasula dzanja langa kumukantha ndi kumuwononga pakati pa anthu anga Aisraeli. 10Iwo adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Chilango cha wodzafunsira nzeru kwa mneneri chidzafanana ndi chilango cha mneneriyo. 11Ndidzachita zimenezi kuti Aisraeli asasocherenso kundisiya Ine ndi kuti asadziyipitsenso ndi machimo awo. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Chilango Chosathawika

12Yehova anayankhula nane kuti, 13“Iwe mwana wa munthu, ngati dziko lindichimwira posandikhulupirira, Ine ndidzatambasula dzanja langa kulikantha pochepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala pa dzikolo ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 14Ngakhale anthu atatu awa, Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, akanangopulumutsa moyo wawo chifukwa cha chilungamo chawo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

15“Kapena ndikanatumiza zirombo mʼdziko monse ndi kulisiya lopanda anthu, ndipo dzikolo nʼkukhala chipululu chakuti munthu sangadutse chifukwa cha zirombo. 16Apanso, ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo okha akanapulumuka, koma dziko likanasanduka chipululu.’

17“Kapena ndikanatumiza lupanga mʼdzikolo ndi kunena kuti, ‘Lupanga lipite mʼdziko monse,’ ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 18Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna kapena ana aakazi. Iwo okha akanapulumuka.’

19“Kapena ndikanatumiza mliri mʼdzikomo ndi kuonetsa ukali wanga pokhetsa magazi, kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. 20Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti ngakhale Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, sakanatha ngakhale kupulumutsa mwana wamwamuna kapena wamkazi. Akanangodzipulumutsa okha chifukwa cha chilungamo chawo.

21“Pakuti Ambuye Yehova akuti: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzatumiza pa Yerusalemu zilango zanga zinayi izi: lupanga, njala, zirombo ndi mliri kuti ziwononge anthu ake ndi nyama zomwe! 22Komabe padzakhala ena opulumuka, ana aamuna ndi ana aakazi amene adzatulutsidwa mʼdzikomo. Iwo adzabwera kwa inu, ndipo mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo, mitima yanu idzakhala pansi mukadzakumbukira chilango chimene ndinachita pa Yerusalemu. 23Mitima yanu idzakhala pansi mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo. Tsono mudzadziwa kuti Yerusalemu sindinamuchite zimenezi popanda chifukwa, akutero Ambuye Yehova.”