以西結書 10 – CCBT & CCL

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

以西結書 10:1-22

耶和華的榮耀離開聖殿

1我觀看,只見基路伯天使頭頂上的穹蒼之中好像有一個藍寶石寶座。 2耶和華對那穿細麻衣的人說:「你到基路伯天使下邊旋轉的輪子中間,雙手拿滿火炭,撒在城上。」我見他進去了。

3當他進去的時候,基路伯天使站在殿的南邊,內院充滿了雲彩。 4耶和華的榮耀從基路伯天使的上面升起,停在殿的門口,殿裡充滿了雲彩,院子也充滿了耶和華榮耀的光輝。 5基路伯天使展翅的響聲好像全能上帝說話的聲音,在外院也可以聽見。

6祂對那穿細麻衣的人說:「你要從基路伯天使下面旋轉的輪子中取火。」那人便進去,站在一個輪子旁邊。 7有一個基路伯天使伸手到他們中間的火裡,取了些火放在那人手裡,那人就拿了出去。 8基路伯天使的翅膀下彷彿有人的手。

9我又看見四個基路伯天使旁各有一個閃耀如綠寶石的輪子。 10四個輪子結構一樣,好像輪套輪。 11基路伯天使移動時,不必轉身就可以向四方移動。前輪朝哪個方向移動,其他的輪子也朝哪個方向移動,不必轉向。 12這四個基路伯天使的全身,包括他們的手、背、翅膀和輪子都佈滿了眼睛。 13我聽見他們稱這些輪子為「旋轉輪」。 14每一個基路伯天使都有四張臉:第一張是基路伯天使的臉,第二張是人的臉,第三張是獅子的臉,第四張是鷹的臉。

15然後,這些基路伯天使都向上升去,他們就是我在迦巴魯河邊所見的活物。 16基路伯天使移動,輪子也隨之移動;基路伯天使展翅飛離地面,輪子也隨之離開地面; 17基路伯天使停住,輪子也隨之停住;基路伯天使上升,輪子也隨之上升。因為活物的靈在輪子中。

18那時,耶和華的榮耀離開了殿的門口,停在基路伯天使上面。 19我看見基路伯天使展翅飛離地面,輪子也隨之飛離。他們停在耶和華殿的東門,以色列上帝的榮耀在他們上面。 20這些是我在迦巴魯河邊所看見的活物,他們在以色列上帝的下面。我知道他們是基路伯天使。 21他們各有四張臉,兩對翅膀,翅膀下彷彿有人的手, 22他們的面貌和我在迦巴魯河邊所見的一樣,每一個都向前直走。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 10:1-22

Ulemerero Uchoka ku mʼNyumba ya Mulungu

1Ine nditayangʼana ku thambo limene lili pamwamba pa mitu ya akerubi ndinangoona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wa mwala wa safiro. 2Tsono Yehova anawuza munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi. Udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa akerubiwo ndipo uwawaze mu mzinda.” Iye anachita zimenezi ine ndikuona.

3Apa akerubiwo anali atayima mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu pamene munthuyo ankalowa. Tsono mtambo unadzaza bwalo lamʼkati. 4Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pamwamba pa akerubi ndipo unafika ku chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Mtambo unadzaza Nyumba ya Mulungu, ndipo kuwala kwa ulemerero wa Yehova kunadzaza bwalolo. 5Phokoso la mapiko a akerubi limamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe linamvekera liwu la Mulungu Wamphamvuzonse akamayankhula.

6Kenaka Yehova analamula munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pala moto pakati pa mikombero, pakati pa akerubi.” Munthu uja anapitadi nakayima pa mbali pa mkombero umodzi. 7Ndipo mmodzi wa akerubi anatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pawo. Iye anapalako motowo ndipo anapatsa munthu wovala chovala chabafuta uja. Tsono iye anawulandira natuluka. 8Ndiye kuti kunsi kwa mapiko akerubi kumaoneka zinthu zooneka ngati manja a munthu.

9Ine nditayangʼanitsitsa ndinaona mikombero inayi pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi; mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala yokongola ya krizoliti. 10Maonekedwe a mikombero inayi ija anali ofanana. Mkombero uliwonse umaoneka ngati mkombero wolowana ndi unzake. 11Poyenda akerubiwo, amapita mbali iliyonse ya mbali zinayizo kumene akerubiwo amayangʼana. Mikomberoyo simatembenuka pamene akerubiwo ankayenda. Kulikonse kumene mutu walunjika nʼkumene ankapita popanda kutembenuka. 12Matupi awo onse, misana yawo, manja awo ndi mapiko awo zinali ndi maso okhaokha, monganso mʼmene inalili mikombero yawo inayi ija. 13Ine ndinamva mikombero ikutchedwa kuti, “mikombero yakamvuluvulu.” 14Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi. Nkhope yoyamba inali ya Kerubi, nkhope yachiwiri inali ya munthu, nkhope yachitatu inali ya mkango ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga.

15Tsono akerubi aja anawuluka. Izi zinali zamoyo zija zimene ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. 16Pamene akerubi ankayenda, nayonso mikombero ya mʼmbali mwawo inkayenda. Akerubiwo ankati akatambasula mapiko awo kuti auluke mikombero sinkachoka mʼmbali mwawo. 17Akerubiwo ankati akayima, mikombero inkayimanso. Ngati akerubiwo auluka, mikomberoyo inkapita nawo chifukwa mzimu wa zamoyozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.

18Pamenepo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu ndi kukakhala pamwamba pa akerubi. 19Ine ndikuona akerubi, anatambasula mapiko awo ndi kuwuluka. Pamene ankapita, mikombero inapita nawo pamodzi. Akerubi anakayima pa khomo la chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Tsono ulemerero wowala wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo.

20Izi ndizo zamoyo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israeli ku mtsinje wa Kebara, ndipo ndinazindikira kuti anali akerubi. 21Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi ndi mapiko anayi, ndipo kunsi kwa mapiko awo kunali chinthu chimene chimaoneka ngati manja a munthu. 22Nkhope zawo zinali zofanana ndi zomwe ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. Kerubi aliyense amayenda molunjika.