民数记 33 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 33:1-56

从埃及到约旦河

1以下是以色列人在摩西亚伦的领导下离开埃及列队行军的路线。 2摩西遵照耶和华的吩咐记录启行的地点,以下是他们停留过的地方。

3一月十五日,即逾越节的第二天,埃及人眼睁睁地看着以色列人昂首挺胸地离开了兰塞4当时埃及人正埋葬他们的长子,耶和华击杀了他们的长子,并借此惩罚了他们的众神明。 5以色列人从兰塞启行,至疏割扎营; 6疏割启行,至旷野边界的以倘扎营; 7以倘启行,又折回巴力·洗分对面的比哈·希录,在密夺附近扎营; 8比哈·希录启行,经过红海到书珥旷野,在伊坦旷野走了三天,至玛拉扎营; 9玛拉启行,至以琳扎营,那里有十二股水泉和七十棵棕树; 10以琳启行,至红海岸边扎营; 11从红海启行,至旷野扎营; 12旷野启行,至脱加扎营; 13脱加启行,至亚录扎营; 14亚录启行,至利非订扎营,在那里民众没有水喝; 15利非订启行,至西奈旷野扎营; 16西奈旷野启行,至基博罗·哈他瓦扎营; 17基博罗·哈他瓦启行,至哈洗录扎营; 18哈洗录启行,至利提玛扎营; 19利提玛启行,至临门·帕烈扎营; 20临门·帕烈启行,至立拿扎营; 21立拿启行,至勒撒扎营; 22勒撒启行,至基希拉他扎营; 23基希拉他启行,至沙斐山扎营; 24沙斐山启行,至哈拉大扎营; 25哈拉大启行,至玛吉希录扎营; 26玛吉希录启行,至他哈扎营; 27他哈启行,至他拉扎营; 28他拉启行,至密加扎营; 29密加启行,至哈摩拿扎营; 30哈摩拿启行,至摩西录扎营; 31摩西录启行,至比尼·亚干扎营; 32比尼·亚干启行,至曷·哈吉甲扎营; 33曷·哈吉甲启行,至约巴他扎营; 34约巴他启行,至阿博拿扎营; 35阿博拿启行,至以旬·迦别扎营; 36以旬·迦别启行,至旷野的加低斯扎营; 37加低斯启行,至以东边界的何珥山扎营。

38以色列人离开埃及后的第四十年五月一日,亚伦祭司遵照耶和华的吩咐上了何珥山,并在那里离世, 39享年一百二十三岁。

40在南地的迦南亚拉得王得知了以色列人要来的消息。

41以色列人从何珥山启行,至撒摩拿扎营; 42撒摩拿启行,至普嫩扎营; 43普嫩启行,至阿伯扎营; 44阿伯启行,至摩押边境的以耶·亚巴琳扎营; 45以耶·亚巴琳启行,至底本·迦得扎营; 46底本·迦得启行,至亚门·低比拉太音扎营; 47亚门·低比拉太音启行,至尼波对面的亚巴琳山扎营; 48亚巴琳山启行,至耶利哥对面、约旦河边的摩押平原扎营。 49他们沿着约旦河在摩押平原扎营,营地从伯·耶施末一直延伸到亚伯·什亭

50耶和华在耶利哥对面、约旦河边的摩押平原对摩西说: 51“你告诉以色列人,‘你们过约旦河进了迦南以后, 52一定要赶走当地的居民,毁掉他们一切的石像和铸像,拆毁他们所有的丘坛。 53你们要占领那片土地,住在那里,因为我已经把那里赐给你们作产业了。 54你们要按宗族家系抽签分配土地,人口多的多分,人口少的少分,抽到哪块地就得哪块地。 55如果你们不赶走那里的居民,留下来的人必成为你们眼里的刺和肋旁的荆棘,在你们所居之地搅扰你们, 56我也会用预备对付他们的方法来对付你们。’”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 33:1-56

Malo omwe Aisraeli Anayima pa Ulendo Wawo

1Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni. 2Mose analemba malo amene anayambira maulendo awo molamulidwa ndi Yehova. Maulendo awo ndi malo omwe anayambira ndi awa:

3Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona, 4pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo.

5Aisraeli atachoka ku Ramesesi, anamanga misasa yawo ku Sukoti.

6Atachoka ku Sukoti anakamanga misasa yawo ku Etamu, mʼmbali mwa chipululu.

7Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli.

8Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara.

9Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko.

10Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira.

11Atachoka ku Nyanja Yofiira anakamanga misasa yawo mʼchipululu cha Sini.

12Atachoka ku chipululu cha Sini anakamanga ku Dofika.

13Atachoka ku Dofika anakamanga misasa yawo ku Alusi.

14Atachoka ku Alusi anakamanga misasa yawo ku Refidimu, kumene kunalibe madzi woti anthu ndi kumwa.

15Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai

16Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava.

17Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti.

18Atachoka ku Heziroti anakamanga ku Ritima.

19Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi.

20Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina.

21Atachoka ku Libina anakamanga ku Risa.

22Atachoka ku Risa anakamanga ku Kehelata.

23Atachoka ku Kehelata anakamanga ku phiri la Seferi.

24Atachoka ku phiri la Seferi anakamanga ku Harada.

25Atachoka ku Harada anakamanga ku Mekheloti.

26Atachoka ku Mekheloti anakamanga ku Tahati.

27Atachoka ku Tahati anakamanga ku Tera.

28Atachoka ku Tera anakamanga ku Mitika.

29Atachoka ku Mitika anakamanga ku Hasimona.

30Atachoka ku Hasimona anakamanga ku Moseroti.

31Atachoka ku Moseroti anakamanga ku Beni Yaakani.

32Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi.

33Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata.

34Atachoka ku Yotibata anakamanga ku Abirona.

35Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi.

36Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi.

37Anachoka ku Kadesi ndi kukamanga ku phiri la Hori, mʼmalire mwa dziko la Edomu. 38Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto. 39Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123.

40Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi yomwe inkakhala ku Negevi kummwera kwa Kanaani, inamva kuti Aisraeli akubwera.

41Atachoka ku phiri la Hori anakamanga ku Zalimoni.

42Atachoka ku Zalimoni anakamanga ku Punoni.

43Atachoka ku Punoni anakamanga ku Oboti.

44Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu.

45Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi.

46Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu.

47Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo.

48Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. 49Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu.

50Pa zigwa za Mowabu, mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, 51“Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani, 52mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo. 53Mukalande dzikolo ndi kukhalamo chifukwa ndakupatsani dziko limenelo kuti mukhalemo. 54Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu.

55“ ‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo. 56Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’ ”