民数记 28 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

民数记 28:1-31

日常献祭的条例

1耶和华对摩西说: 2“你告诉以色列人,要在规定的时间献上蒙我悦纳的馨香火祭,作为我的食物。 3以下是他们要献给耶和华的火祭。

“每天两只毫无残疾、一岁的公羊羔作燔祭, 4早晨和傍晚各献一只, 5同时献上素祭——一公斤细面粉调上一升油。 6这是在西奈山上规定的日常燔祭,是献给耶和华的馨香火祭。 7与每只羊羔一同献上的还有一升酒,要将酒洒在圣所作为献给耶和华的奠祭。 8傍晚献羊羔时,也要像早上一样同时献上素祭和奠祭,作蒙耶和华悦纳的馨香火祭。

安息日献的祭

9“安息日,要献两只毫无残疾、一岁的公羊羔,同时献上奠祭以及两公斤调油的细面粉作素祭。 10这是在日常燔祭和奠祭以外安息日所献的燔祭。

初一献的祭

11“在朔日,要给耶和华献燔祭——两头公牛犊、一只公绵羊和七只一岁的公羊羔,都要毫无残疾。 12同时要献上调了油的细面粉作素祭,每头公牛需献三公斤素祭,每只公绵羊需献两公斤素祭, 13每只公羊羔需献一公斤素祭。这馨香的燔祭是献给耶和华的火祭。 14献燔祭时要同时献上奠祭,每头公牛需献二升奠酒,每只公绵羊需献一点二升奠酒,每只羊羔需献一升奠酒。这是朔日要献的燔祭,一年之中月月如此。 15除了日常的燔祭和奠祭以外,还要把一只公山羊献给耶和华作赎罪祭。

逾越节献的祭

16“一月十四日是耶和华的逾越节, 17十五日开始节庆,你们要连续七天吃无酵饼。 18第一天要举行圣会,不可做日常工作。 19你们要把毫无残疾的两头公牛犊、一只公绵羊和七只一岁的公羊羔献给耶和华作燔祭; 20同时要献上调了油的细面粉作素祭,每头公牛需献三公斤素祭,每只公绵羊需献两公斤素祭, 21每只公羊羔需献一公斤素祭; 22同时还要献一只公山羊作赎罪祭,为你们赎罪。 23除了早晨献的日常燔祭以外,要献上这些祭物。 24接连七天,除了日常的燔祭和同献的奠祭以外,还要照上面的规定给耶和华献上馨香的火祭。 25第七天,你们要举行圣会,不可做日常工作。

七七收获节献的祭

26“七七收获节庄稼初熟之日,就是你们把新素祭献给耶和华的日子,不可工作,要举行圣会。 27你们要把两头公牛犊、一只公绵羊和七只一岁的公羊羔献给耶和华作馨香的燔祭。 28同时要献上调了油的细面粉作素祭,每头公牛需献三公斤素祭,每只公绵羊需献两公斤素祭, 29每只公羊羔需献一公斤素祭。 30此外,还要献上一只公山羊作赎罪祭,为你们赎罪。 31除了日常的燔祭和同献的素祭以外,还要献上奠祭。祭牲不可有残疾。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Numeri 28:1-31

Zopereka za Tsiku ndi Tsiku

1Yehova anawuza Mose kuti, 2“Lamula Aisraeli kuti, ‘Onetsetsani kuti mukupereka kwa Ine pa nthawi yoyikika, chopereka cha chakudya chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Ine.’ 3Awuze kuti, ‘Nsembe ya chakudya imene muzipereka pa moto kwa Yehova tsiku ndi tsiku ndi iyi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri, wopanda chilema. 4Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. 5Muziperekanso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi. 6Iyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku imene analamula pa phiri la Sinai kuti ikhale fungo lokoma, nsembe yopsereza pa moto yopereka kwa Yehova. 7Chopereka chachakumwa chikhale lita imodzi yachakumwa chaukali pa nkhosa iliyonse. Muzithira pamalo opatulika, kupereka kwa Yehova. 8Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’ ”

Zopereka za pa Sabata

9“ ‘Pa tsiku la Sabata, muzipereka nsembe ana ankhosa awiri a chaka chimodzi wopanda chilema, pamodzi ndi chopereka chachakumwa ndi chopereka chachakudya chokwana makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. 10Iyi ndi nsembe yopsereza ya pa Sabata iliyonse, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake chachakumwa.’ ”

Zopereka za pa Mwezi

11“Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, onse wopanda chilema. 12Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; ndi nkhosa yayimuna, chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; 13ndipo pa mwana wankhosa aliyense, chopereka cha ufa wa kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, izi ndi za nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto ya kwa Yehova. 14Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka. 15Powonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake cha chakumwa, mbuzi yayimuna imodzi iperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopepesera machimo.

Paska

16“ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova. 17Pa tsiku la 15 la mwezi womwewo pazikhala chikondwerero. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. 18Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. 19Koma muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri aamuna a chaka chimodzi, onsewo wopanda chilema. 20Pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; makilogalamu awiri pa nkhosa yayimuna iliyonse. 21Kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa asanu ndi awiri aja. 22Muziphatikizapo mbuzi yayimuna monga nsembe yopepesera machimo anu. 23Muzikonza zimenezi nthawi zonse, powonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa. 24Motere muzikonza chakudya cha nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pa masiku asanu ndi awiri ngati fungo lokomera Yehova. Zimenezi ziziperekedwa kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse pamodzi ndi nsembe yachakumwa. 25Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse.

Madyerero a Masabata

26“ ‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. 27Muzipereka nsembe zopsereza za ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa imodzi yayimuna ndi ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi monga fungo lokomera Yehova. 28Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pazikhala chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri. 29Ndipo pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja, kilogalamu imodzi. 30Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu. 31Muzipereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za zakumwa ndi nsembe yake ya chakudya. Onetsetsani kuti nyamazo zilibe chilema.