列王纪上 6 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

列王纪上 6:1-38

建造圣殿

1所罗门在做以色列王的第四年二月,即西弗月,开始为耶和华建殿。那时正是以色列人离开埃及后第四百八十年。 2所罗门王为耶和华建造的殿长二十七米,宽九米,高十三米半。 3殿前的门廊和殿一样宽九米,深四米半。 4殿有精致的窗户。 5靠殿墙、围着外殿和内殿又造了三层厢房, 6底层宽二点二五米,中层宽二点七米,上层宽三点一米。厢房的横梁都搭在殿墙突出的地方,免得插入殿墙。 7建殿的石头都在采石场凿好了,建殿的时候听不到锤子、斧头或其他铁器的响声。

8底层厢房的进口在殿的南面,沿着一道螺旋楼梯可以通到第二层和第三层。 9殿建成后,殿顶装上香柏木的梁木和木板。 10靠着殿墙所造的厢房每一层高二点二五米,用香柏木的梁木与殿墙接连起来。

耶和华的约

11耶和华对所罗门说: 12“关于你所建的这殿,若你遵行我的律例,顺从我的典章,谨守我的一切诫命,我必实现我对你父亲大卫的应许。 13我必住在以色列人当中,不抛弃我的以色列子民。”

14所罗门建造的殿落成了。 15殿里的墙壁和天花板都铺上了香柏木,地面都铺上了松木板。 16在殿的后部,从地面至天花板用香柏木板隔出长九米的内殿,就是至圣所。 17在至圣所外面是外殿,长十八米。 18殿内全部铺上香柏木,不露一点石头,香柏木上刻着野瓜和花朵的图案。 19殿的至圣所用来安放耶和华的约柜。 20至圣所长、宽和高都是九米,里面全贴上纯金,香柏木造的祭坛也包上纯金。 21殿内全部贴上纯金,至圣所前面有金链拦着。 22殿内都贴上纯金,至圣所内的祭坛也都包上纯金。

23至圣所里面放着两个橄榄木造的基路伯天使,各高四米半, 24各有两个二点二五米长的翅膀,双翅展开,两翅尖相距四点五米。 25两个基路伯的大小和形状一模一样, 26高度都是四点五米。 27他将两个基路伯安在至圣所内,两个基路伯展开翅膀,各有一个翅膀在至圣所的中央相接,另一个翅膀的尖端触到墙壁。 28这两个基路伯天使也包上金。

29内殿和外殿的墙壁都刻上基路伯天使、棕树和花朵的图案, 30地板是铺金的。 31至圣所的门、门楣和门柱都是橄榄木造的,门柱呈五角形。 32两扇用橄榄木造的门上都刻着基路伯天使、棕树和花朵的图案,并包上金。 33外殿的四角形门柱也是用橄榄木造的, 34两扇门是松木造的,每一扇门都分为可折叠的两片, 35上面刻着基路伯天使、棕树和花朵的图案,并包上金。 36内院的墙是由三层凿好的石头和一层香柏木建的。

37耶和华的殿在所罗门执政第四年的西弗月奠基, 38在他执政的第十一年的布勒月,即八月全部按规格建成,历经七年。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mafumu 6:1-38

Solomoni Amanga Nyumba ya Mulungu

1Patapita zaka 480 Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto, chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomoni mu Israeli, mwezi wa Zivi, umene ndi mwezi wachiwiri, Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova.

2Nyumba imene Solomoni anamangira Yehova mulitali mwake inali mamita 27, mulifupi mwake inali mamita asanu ndi anayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka. 3Chipinda chakubwalo mʼmbali mwake chinali mamita asanu ndi anayi kulingana ndi mulifupi mwa Nyumbayo ndipo kutalika kwake kunali kwa mamita anayi ndi theka. 4Anapanga mazenera amene maferemu ake anali olowa mʼkati mwa makoma a Nyumbayo. 5Mʼmbali mwa makoma a Nyumba yayikulu ndi chipinda chopatulika chamʼkati, anamanga zipinda zosanjikizana, mozungulira. 6Chipinda chapansi, mulifupi mwake chinali mamita awiri, chipinda chapakati mulifupi mwake chinali mamita awiri ndi theka ndipo chipinda chapamwamba penipeni mulifupi mwake chinali mamita atatu. Iye anapanga zinthu zosongoka kunja kwa khoma la kunja kuzungulira Nyumbayo kuti asamapise kanthu pa makoma a Nyumba ya Mulungu.

7Poyimanga Nyumbayo, anagwiritsa ntchito miyala yosemeratu, ndipo pogwira ntchitoyo sipanamveke nyundo, nkhwangwa kapena chida china chilichonse.

8Chipata cholowera ku chipinda chapansi chinali mbali ya kummwera kwa Nyumbayo. Panali makwerero okwerera ku chipinda chapakati ndiponso chipinda cha pamwamba. 9Choncho anamanga Nyumbayo mpaka kuyimaliza ndipo denga lake linali la mitanda ndi matabwa a mkungudza. 10Msinkhu wa chipinda chilichonse unali mamita awiri, ndipo anazilumukiza ku Nyumbayo ndi mitanda yamkungudza.

11Yehova anayankhula ndi Solomoni kuti, 12“Kunena za Nyumba imene ukumangayi, ngati iwe udzamvera malangizo anga ndi kutsatira mawu anga, ngati udzasunga malamulo anga ndi kuwachita, Ine ndidzakwaniritsa zonse zomwe ndinalonjeza Davide abambo ako. 13Ndipo Ine ndidzakhazikika pakati pa ana a Israeli ndipo sindidzawasiya anthu anga Aisraeli.”

14Kotero Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu nayimaliza. 15Anakuta khoma la mʼkati mwake ndi matabwa a mkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku denga ndipo pansi pa Nyumbayo anayalapo matabwa a payini. 16Kumbuyo kwa Nyumbayo anadula chipinda chachitali mamita asanu ndi anayi. Chipindachi anachimanga ndi matabwa a mkungudza kuyambira pansi mpaka ku denga kuti chikhale chipinda chopatulika chamʼkati mwa Nyumba ya Mulungu ngati Malo Wopatulika Kwambiri. 17Chipinda chachikulu chimene chinali kutsogolo kwa Malo Wopatulika Kwambiriwa, chinali mamita 18 mulitali mwake. 18Mʼkati mwa Nyumbayi munali matabwa a mkungudza, pamene anajambulapo zithunzi za zikho ndi maluwa. Paliponse panali mkungudza wokhawokha. Panalibe mwala uliwonse umene unkaonekera.

19Anakonza malo wopatulika mʼkati mwa Nyumbayi kuti ayikemo Bokosi la Chipangano cha Yehova. 20Malo wopatulika a mʼkatiwo anali a mamita asanu ndi anayi mulitali mwake, mulifupi mwake, ndi msinkhu wake. Anakuta mʼkati mwake ndi golide weniweni ndiponso anapanga guwa lansembe la matabwa a mkungudza. 21Solomoni anakutira golide weniweni mʼkati mwake mwa Nyumbayi, ndipo anayalika maunyolo a golide mopingasa kutsogolo kwa malo wopatulika amene anakutidwa ndi golide. 22Motero anakuta mʼkati monse ndi golide. Anakutanso ndi golide guwa lansembe la mʼkati mwa chipinda chopatulika.

23Mʼchipinda chopatulika cha mʼkati anapangamo akerubi awiri a mtengo wa olivi. Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka. 24Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita awiri ndi theka, phiko linanso linali mamita awiri ndi theka, kutambasula mapiko awiriwo, kuchokera msonga ina mpaka msonga ina kutalika kwake kunali mamita anayi ndi theka. 25Kerubi wachiwiriyo msinkhu wake unalinso mamita anayi ndi theka, pakuti akerubi awiriwo anali a misinkhu yofanana ndi a mapangidwe ofanana. 26Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka. 27Solomoni anayika akerubiwo mʼchipinda cha mʼkati mwenimweni mwa Nyumba ya Mulungu, atatambasula mapiko awo. Phiko la kerubi wina limakhudza khoma lina, pamene phiko la winayo limakhudza khoma linanso ndipo mapiko awo amakhudzana pakati pa chipindacho. 28Akerubiwo anawakuta ndi golide.

29Pa makoma onse kuzungulira Nyumbayo, mʼzipinda za mʼkati ndi za kunja zomwe, anajambulapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa. 30Anayala golide pansi mu Nyumbamo mʼzipinda zamʼkati ndi zakunja zomwe.

31Ndipo pa khomo lolowera ku malo wopatulika amʼkati anapanga zitseko za mtengo wa olivi ndipo khonde lake linali ndi mbali zisanu. 32Ndipo pa zitseko ziwiri zija za mtengo wa olivi anajambulapo kerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa ndipo anapaka golide akerubiwo ndi mitengo ya mgwalangwayo. 33Anapanganso chimodzimodzi mphuthu za mbali zinayi za mtengo wa olivi za pa khomo la Nyumbayo. 34Solomoni anapanganso zitseko ziwiri za payini. Chitseko chilichonse chinali ndi mbali ziwiri zotha kuzipinda. 35Pa zitsekozo anagobapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa wotambasuka ndipo zojambulazo anazikuta ndi golide wopyapyala.

36Ndipo anamanga bwalo la mʼkati lokhala ndi khoma lokhala ndi mizere itatu ya miyala yosema ndiponso mzere umodzi wa matabwa osemedwa a mkungudza.

37Maziko a Nyumba ya Yehova anamangidwa pa chaka chachinayi, mwezi wa Zivi. 38Pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumba anatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Anamanga Nyumbayo kwa zaka zisanu ndi ziwiri.