何西阿书 13 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

何西阿书 13:1-16

对以色列的最后审判

1以法莲支派在以色列地位崇高,

他们一开口,人都恐惧颤抖。

但他们却祭拜巴力,自招灭亡。

2如今他们作恶日甚,

凭借自己的聪明用银子铸造神像,

但这不过是匠人之作。

人们议论他们说:

“那些献祭的人竟亲吻牛犊偶像!”

3他们像晨雾,如转瞬即逝的朝露,

像麦场上飞旋而去的糠秕,

又像窗口冒出的轻烟。

4耶和华说:

“自从你们离开埃及以来,

我就是你们的上帝耶和华。

除我以外,你们不可有别的神明;

在我以外,你们也没有别的救主。

5我曾在干旱的旷野照顾你们,

6但你们吃得饱足以后,

就心高气傲,忘记了我。

7因此,我要像狮子攻击你们,

如豹子潜伏在路旁;

8我要像一头失了幼崽的母熊冲向你们,

撕裂你们的胸膛;

我要像母狮吞噬你们,

像凶猛的野兽撕碎你们。

9以色列啊,你要灭亡了,

因为你抵挡我,抵挡你的帮助者。

10你曾求我为你设立君王和首领,

现在拯救你的君王在哪里呢?

在各城管理你的首领在哪里呢?

11我在愤怒中赐给你君王,

也在愤怒中废黜他们。

12以法莲的过犯已被记录在册,

他的罪恶已被储存入库。

13临产的阵痛要临到他,

但他是毫无智慧的孩子,

分娩之时却不离开母腹。

14我要把他们从阴间的权势下赎回吗?

我要救他们脱离死亡吗?

死亡啊,你去降灾给他们吧!

阴间啊,你去毁灭他们吧!

我不会再怜悯他们。

15尽管以法莲在众弟兄中最强盛,

但炙热的东风——耶和华的风要从沙漠刮来,

使清泉枯竭,水井干涸。

他储藏的一切珍宝都要被掳去。

16撒玛利亚人背叛了他们的上帝,

要担当自己的罪过。

他们将丧身刀下,

他们的孩子要被摔死,

孕妇要被剖腹。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Hoseya 13:1-16

Mkwiyo wa Yehova pa Israeli

1Kale Efereimu ankati akayankhula, anthu ankanjenjemera;

anali wolemekezeka mu Israeli.

Koma analakwa popembedza Baala, motero anafa.

2Tsopano akunka nachimwirachimwirabe;

akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo,

zifanizo zopangidwa mwaluso,

zonsezo zopangidwa ndi amisiri.

Amanena za anthu awa kuti,

“Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe

ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”

3Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa,

ngati mame amene amakamuka msanga,

ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu,

ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.

4Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu,

amene ndinakutulutsani mu Igupto.

Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha,

palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.

5Ndinakusamalira mʼchipululu,

mʼdziko lotentha kwambiri.

6Pamene ndinawadyetsa, iwo anakhuta;

iwo atakhuta anayamba kunyada;

ndipo anandiyiwala Ine.

7Motero ndidzawalumphira ngati mkango,

ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.

8Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake,

ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola.

Ndidzawapwepweta ngati mkango;

chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.

9“Iwe Israeli, wawonongedwa,

chifukwa ukutsutsana ndi Ine, ukutsutsana ndi mthandizi wako.

10Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse?

Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti,

amene iwe unanena za iwo kuti,

‘Patseni mfumu ndi akalonga?’

11Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima,

ndipo ndinayichotsa mwaukali.

12Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa,

machimo ake alembedwa mʼbuku.

13Zowawa zonga za mayi pa nthawi yobala mwana zamugwera,

koma iye ndi mwana wopanda nzeru,

pamene nthawi yake yobadwa yafika

iyeyo safuna kutuluka mʼmimba mwa amayi ake.

14“Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda;

ndidzawawombola ku imfa.

Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti?

Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti?

“Sindidzachitanso chifundo,

15ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake,

mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera,

ikuwomba kuchokera ku chipululu.

Kasupe wake adzaphwa

ndipo chitsime chake chidzawuma.

Chuma chake chonse chamtengowapatali

chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.

16Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo,

chifukwa anawukira Mulungu wawo.

Adzaphedwa ndi lupanga;

ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi,

akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”