但以理书 7 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

但以理书 7:1-28

但以理梦见四兽

1巴比伦伯沙撒元年,但以理在床上做了一个梦,脑中出现了异象,便把梦记录下来,讲述其中的大意。 2但以理说:“我在夜间的异象中看见天风四面吹来,搅动大海。 3接着,四只巨兽从海中上来,各有不同的形状。 4第一只兽像狮子,但有鹰的翅膀。我观看时,见它的翅膀被拔掉。它被扶起来,像人一样双脚站在地上,并被赋予人的头脑。 5第二只兽像熊,用两只后腿站立,牙齿间叼着三根肋骨,有声音对它说,‘起来,多吞吃肉吧!’

6“此后,我继续观看,见还有一只兽像豹,背上有四个如鸟翼般的翅膀。这兽有四个头,并被赋予权柄。 7此后,我在夜间的异象中看见第四只兽,恐怖可怕,极其强壮,用大铁牙吞吃、咬碎猎物,用脚践踏所剩的。这兽与前三只兽不同,它有十个角。 8我观看这些角时,见其中长出一个小角,先前的角中有三个被连根拔出,让它取而代之。这小角有人的眼睛和说狂言的口。

9“我看见宝座已设立,

上面坐着亘古长存者,

祂的衣服洁白如雪,

头发如纯净的羊毛。

祂的宝座是火焰,

宝座的轮子是烈火。

10从祂面前流出火河,

事奉祂的有千千,

侍立在祂面前的有万万。

祂坐下要审判,

案卷已经展开。

11“我继续观看,见那兽被杀,身体被毁并被扔进火中,因为它的小角口出狂言。 12至于其余的兽,它们的权柄都被夺去,但获准再存活一段时间。

13“我在夜间的异象中看见一位像人子的,驾着天云而来,到亘古长存者那里,被引到祂面前。 14他得到权柄、荣耀和国度,各族、各邦、各语种的人都要事奉他。他的统治直到永远、没有穷尽,他的国度永不灭亡。

解释异象

15“我但以理心中不安,脑中出现的异象令我恐惧, 16便走近一位侍立一旁的,问他这些事的意思。他就向我解释这些事的意思,说, 17‘这四只巨兽是指四个将要在世上兴起的国。 18但至高者的圣民必承受国度,并永永远远拥有国度。’

19“那时,我想知道关于第四兽的事,它与其余三兽不同,极其可怕,有铁牙铜爪,吞吃、咬碎猎物,用脚践踏所剩的。 20我也想知道有关它头上的十角及后来长出的小角的事。这小角取代了三角,它有眼和说狂言的口,比其他的角更强大。 21我看见这小角与圣民争战,并占了上风。 22后来亘古长存的至高者来为祂的圣民申冤。圣民拥有国度的时候到了。

23“那位侍立一旁的说,‘第四只兽是指世上将兴起的第四个国,与其他各国不同,它将吞吃、践踏、咬碎天下。 24十角是指这国中将兴起十个王,后来又兴起一王,与先前的王不同,他将制服三个王。 25他必亵渎至高者,迫害至高者的圣民,试图改变节期和律法。圣民将被交在他手中三年半。 26然而,审判者将坐下来审判,夺去并永远废除他的权柄。 27那时,国度、权柄和天下万国的尊荣必赐给至高者的圣民。祂的国度直到永远,一切掌权者都要事奉祂,顺服祂。’

28“这就是我的梦。我但以理心中十分害怕,脸色苍白,但我没有把这事告诉别人。”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 7:1-28

Maloto a Danieli a Zirombo Zinayi

1Chaka choyamba cha ufumu wa Belisazara wa ku Babuloni, Danieli akugona pa bedi lake analota maloto ndipo anaona masomphenya. Iye analemba malotowo mwachidule.

2Danieli anati, “Mʼmasomphenya anga usiku, ndinaona nyanga yayikulu ikuvunduka ndi mphepo zochokera mbali zonse zinayi za mlengalenga. 3Ndipo mʼnyangayo munatuluka zirombo zazikulu zinayi, chilichonse chosiyana ndi chinzake.

4“Choyamba chinali ngati mkango, ndipo chinali ndi mapiko ngati a chiwombankhanga. Ndinayangʼanitsitsa, kenaka mapiko ake anakhadzuka ndipo chinanyamulidwa ndi kuyimirira ndi miyendo yake iwiri ngati munthu, ndipo anachipatsa mtima wa munthu.

5“Ndipo ndinaona chirombo chachiwiri, chimene chimaoneka ngati chimbalangondo. Chinali chonyamuka mbali imodzi, ndipo chinapana nthiti zitatu mʼkamwa mwake pakati pa mano ake. Anachilamula kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri!’

6“Pambuyo pake, ndinaona chirombo china, chimene chinkaoneka ngati kambuku. Pa msana pake chinali ndi mapiko anayi onga a mbalame. Chirombo ichi chinali ndi mitu inayi, ndipo chinapatsidwa mphamvu kuti chilamulire.

7“Zitatha izi, mʼmasomphenya anga usiku, ndinaonanso chirombo chachinayi chitayima patsogolo panga. Chinali choopsa, chochititsa mantha ndi champhamvu kwambiri. Chinali ndi mano akuluakulu a chitsulo. Chimati chikatekedza ndi kumeza adani ake kenaka chinapondereza chilichonse chotsala. Ichi chinali chosiyana ndi zirombo zoyambirira zija, ndipo chinali ndi nyanga khumi.

8“Ndikulingalira za nyangazo, ndinaona nyanga ina, yocheperapo, imene inkatuluka pakati pa zinzake. Zitatu mwa nyanga zoyamba zija zinazulidwa mwa icho. Nyanga iyi inali ndi maso a munthu ndi pakamwa pamene pankayankhula zodzitama.

9“Ine ndikuyangʼanabe ndinaona

“mipando yaufumu ikukhazikitsidwa,

ndipo Mkulu Wachikhalire anakhala pa mpando wake.

Zovala zake zinali zoyera ngati chisanu chowundana;

tsitsi la kumutu kwake linali loyera ngati thonje.

Mpando wake waufumu unali wonga malawi a moto,

ndipo mikombero yake yonse inkayaka moto.

10Mtsinje wa moto unkayenda,

kuchokera patsogolo pake.

Anthu miyandamiyanda ankamutumikira;

ndipo anthu osawerengeka anayima pamaso pake.

Abwalo anakhala malo awo,

ndipo mabuku anatsekulidwa.

11“Ndinapitiriza kuyangʼanitsitsa chifukwa cha mawu odzitamandira amene nyanga ija inkayankhula. Ndili chiyangʼanire choncho chirombo chachinayi chija chinaphedwa ndipo thupi lake linawonongedwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 12Zirombo zina zija zinalandidwa ulamuliro wawo, koma zinaloledwa kukhala ndi moyo kwa kanthawi.

13“Ndikuyangʼanabe zinthu mʼmasomphenya usiku, ndinaona wina ngati mwana wa munthu, akubwera ndi mitambo ya kumwamba. Anayandikira Mkulu Wachikhalire uja. Ena anamuperekeza kwa Iye. 14Anapatsidwa ulamuliro, ulemerero ndi mphamvu za ufumu kuti anthu a mitundu ina yonse, mayiko ndi anthu aziyankhulo zosiyanasiyana apembedze iye. Mphamvu zake ndi mphamvu zamuyaya zimene sizidzatha, ndipo ufumu wake sudzawonongeka konse.

Tanthauzo la Maloto

15“Ine Danieli ndinavutika mu mzimu, ndipo zimene ndinaziona mʼmasomphenya zinandisautsa mʼmaganizo. 16Ndinayandikira mmodzi mwa amene anayima pamenepo ndi kumufunsa tanthauzo lenileni la zonsezi.

“Kotero anandiwuza ndi kundipatsa tanthauzo la zinthu zonse izi: 17‘Zirombo zikuluzikulu zinayi zija ndi maufumu anayi amene adzaoneka pa dziko lapansi. 18Koma oyera mtima a Wammwambamwamba adzalandira ufumu ndipo udzakhala nawo mpaka muyaya, inde ku nthawi zonse.’

19“Kenaka ndinafuna kudziwa tanthauzo lenileni la chirombo chachinayi chija, chimene chinali chosiyana ndi zinzake zonse ndi choopsa kwambiri, cha mano ake achitsulo ndi zikhadabo zamkuwa; chirombo chimene chinapweteka ndi kumeza zinazo ndi kupondaponda chilichonse chimene chinatsala. 20Ndinafunanso kudziwa za nyanga khumi za pa mutu pake ndiponso ina ija, nyanga imene inaphuka pambuyo pake ndi kugwetsa zitatu zija. Imeneyi ndi nyanga ija yokhala ndi maso ndi pakamwa poyankhula modzitamandira, ndipo inkaoneka yayikulu kupambana zina zonse. 21Ndikuyangʼanitsitsa, nyanga imeneyi inathira nkhondo anthu oyera mtima ndi kuwagonjetsa, 22mpaka pamene Mkulu Wachikhalire uja anafika ndi kuweruza mokomera oyera mtima a Wammwambamwamba. Tsono nthawi inafika imene anthu oyera mtimawo analandira ufumu.

23“Tsono anandifotokozera kuti, ‘Chirombo chachinayi chija ndi ufumu wachinayi umene udzaoneka pa dziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu anzake onse ndipo udzawononga dziko lonse lapansi. Udzalipondaponda ndi kuliphwasula. 24Nyanga khumi zija ndiwo mafumu khumi amene adzatuluka mu ufumu umenewu. Pambuyo pake mfumu ina idzadzuka, yosiyana ndi mafumu a mʼmbuyomu; iyo idzagonjetsa mafumu atatu. 25Idzayankhula motsutsana ndi Wammwambamwamba ndipo adzazunza oyera mtima ndi kusintha masiku azikondwerero ndi malamulo. Oyera mtimawo adzalamulidwa ndi mfumuyi kwa zaka zitatu ndi theka.

26“ ‘Koma bwalo lidzapereka chiweruzo, ndipo mphamvu zake zidzalandidwa ndi kuwonongedwa kotheratu mpaka muyaya. 27Kenaka ulamuliro, mphamvu ndi ukulu wa maufumu pa dziko lonse lapansi zidzaperekedwa kwa oyera mtima, a Wammwambamwamba. Ufumu wawo udzakhala ufumu wosatha, ndipo olamulira onse adzawalamulira ndi kuwamvera.’ ”

28“Apa ndiye pa mapeto pa nkhaniyi. Ine Danieli, ndinasautsidwa kwambiri mʼmaganizo anga, ndipo nkhope yanga inasandulika, koma ndinasunga nkhaniyi mu mtima mwanga.”