但以理书 2 – CCB & CCL

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

但以理书 2:1-49

尼布甲尼撒的梦

1尼布甲尼撒在执政第二年做了梦,心里烦乱,无法入睡, 2便派人召来术士、巫师、行法术的和占星家2:2 占星家”亚兰文作“迦勒底人”,同下2:4510节;3:84:75:711,为他解梦。他们都来到王面前。 3王对他们说:“我做了一个梦,心里烦乱,想知道梦的意思。” 4占星家用亚兰话对王说:“愿王万岁!请将梦告诉仆人,仆人好解释梦的意思。” 5王对占星家说:“我的旨意已定,你们若不能将梦和梦的意思告诉我,必被碎尸万段,你们的家必沦为废墟。 6你们若能将梦和梦的意思告诉我,我必给你们礼物、赏赐和极大的尊荣。所以你们要将梦和梦的意思告诉我。” 7他们再次对王说:“请王将梦告诉仆人,仆人好解释梦的意思。” 8王说:“我敢肯定,你们是在拖延时间,因为你们知道我的旨意已定, 9你们若不将梦告诉我,我必惩治你们。你们串通起来在我面前胡言乱语,期待情况会改变。现在将梦告诉我,我就相信你们能解梦。” 10占星家说:“王所要求的,世上无人能做到,因为再伟大、再有权势的君王也没问过术士、巫师或占星家这样的事。 11王问的事太难,除了不在人间居住的神明外,无人能为王解答。” 12王大怒,下令处死巴比伦所有的智者。 13于是,处死智者的谕旨发出,但以理和他的同伴都在被杀之列。

14王的护卫长亚略奉命要处死巴比伦的智者,但以理机智、谨慎地应对。 15他问王的护卫长亚略:“王的命令为何这样紧急?”亚略就把情况告诉他。 16但以理便进宫求王宽限,以便为王解梦。 17然后,他回到居所将这事告诉同伴哈拿尼雅米沙利亚撒利雅18要同伴祈求天上的上帝施怜悯,显明这奥秘,以免他们和其他巴比伦的智者一起被杀。 19这奥秘在夜间的异象中向但以理显明,他便颂赞天上的上帝, 20说:

“上帝的名永永远远当受称颂,

因为智慧和能力都属于祂。

21祂改变时令和季节,废王立王,

赐智慧给智者,赐知识给哲士。

22祂显明深奥隐秘之事,

洞悉暗中的隐情,

有光与祂同住。

23我祖先的上帝啊,我感谢你,赞美你,

因你赐我智慧和能力,

应允我们的祈求,

使我们明白王的梦。”

但以理解梦

24于是,但以理去见王指派处死巴比伦智者的亚略,对他说:“不要处死巴比伦的智者,请带我去见王,我要为王解梦。” 25亚略急忙带但以理去见王,对王说:“我在被掳的犹大人中找到一个能为王解梦的。” 26王就问又名伯提沙撒但以理:“你能将我做的梦和梦的意思告诉我吗?” 27但以理回答说:“没有智者、术士、巫师或占星家可以解答王所问的奥秘, 28-30但天上的上帝能揭开奥秘,祂已把将来要发生的事告诉了王。王啊,你在床上梦见了将来的事,揭开奥秘的上帝已把将来的事指示给你。上帝将王做的梦启示给我,并非因为我的智慧胜过其他人,而是要让王知道梦的意思和王的心事。以下是王在床上做的梦和脑中出现的异象。

31“王啊,你梦见一个高大宏伟、极其明亮的塑像站在你面前,相貌可怕, 32有纯金的头、银的胸和臂、铜的肚腹和大腿、 33铁的小腿和半铁半泥的脚。 34在你观看的时候,有一块非人手凿出的石头打在塑像半铁半泥的脚上,砸碎了脚。 35铁、泥、铜、银、金随即粉碎,犹如夏天麦场上的糠秕,被风吹得无影无踪。但打碎这像的石头变成一座大山,充满整个大地。

36“这就是梦的内容。现在我们要为王解梦。 37王啊,你是万王之王,天上的上帝已将国度、权柄、能力和尊荣赐给你, 38也将居住在各地的世人、走兽和飞禽都交在你手中,让你管理。你就是那金头。 39在你之后,必有另一国兴起,不及你的国强大。之后是将要统治天下的第三个国,是铜的。 40接着是坚如铁的第四国,能击垮、打碎列国,正如铁能击垮、打碎一切。 41你看见半铁半陶泥的脚和脚趾,表示那将是一个分裂的国。正如你看见铁和泥混杂在一起,它必有铁一般的力量。 42半铁半泥的脚趾表示那国必半强半弱。 43你看见铁和泥混杂在一起,这表示那国的民族彼此混杂通婚,却不能团结,正如铁和泥无法混合。 44在以上列王统治的时候,天上的上帝必设立一国——永不灭亡、外族无法夺其政权。这国将击垮、消灭列国,并且永远长存。 45你看见那块非人手从山中凿出的石头打碎铁、铜、泥、银和金。伟大的上帝已把将来的事告诉了王。这梦是真实的,解释是可靠的。”

46尼布甲尼撒王俯伏在地,向但以理下拜,并下令给他献供物和香。 47王对但以理说:“你们的上帝真是万神之神、万王之主、奥秘的启示者,因为你能揭开这个奥秘。” 48王赐但以理高官及许多贵重的礼物,派他治理巴比伦全省,管理巴比伦所有的智者。 49王又应允但以理的请求,派沙得拉米煞亚伯尼歌负责巴比伦省的事务。但以理仍在朝中供职。

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Danieli 2:1-49

Maloto a Nebukadinezara

1Chaka chachiwiri cha ulamuliro wake, Nebukadinezara analota maloto; anavutika mu mtima mwake ndipo analephera kugona. 2Tsono mfumu inayitana amatsenga, owombeza, amawula ndi oyangʼana nyenyezi kuti amufotokozere zomwe analota. Pamene iwo analowa ndi kuyima pamaso pa mfumu, 3mfumuyo inawawuza kuti, “Ndalota loto lomwe likundisautsa ndipo ndikufuna kudziwa tanthauzo lake.”

4Pamenepa alawuli anati kwa mfumu mʼChiaramu, “Mukhale ndi moyo wautali mfumu! Tiwuzeni ife atumiki anu zimene mwalota, ndipo tidzakuwuzani tanthauzo lake.”

5Mfumu inayankha alawuliwo kuti, “Zimene ndatsimikiza kuchita ndi izi: Ngati inu simundifotokozera zimene ndalota ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa bwinja. 6Koma ngati mundiwuza zimene ndalota ndi tanthauzo lake, ndidzakupatsani mphatso ndi mphotho ndi ulemu waukulu. Choncho mundiwuze zimene ndalota ndi tanthauzo lake.”

7Iwo anayankhanso kachiwiri kuti, “Mfumu iwuze atumiki ake chimene yalota, ndipo ife tidzatanthauzira.”

8Ndipo mfumu inayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti mukungozengereza kufuna kutaya nthawi chabe chifukwa mukuzindikira kuti izi ndi zimene ndatsimikiza kuchita. 9Ngati simundiwuza zimene ndalota, chilango chake ndi chimodzi. Inu mwagwirizana kuti mundiwuze ine bodza ndi chinyengo ndi kuyembekeza kuti ine ndisintha. Tsono mundiwuze zimene ndalota, ndipo ine ndidzadziwa kuti mukhoza kunditanthauzira.”

10Alawuli anayankha mfumu kuti, “Palibe munthu pa dziko lapansi amene akhoza kuchita chimene mfumu ikufunsa! Palibe mfumu, kaya yayikulu kapena yamphamvu bwanji imene inafunsapo amatsenga, owombeza kapena alawuli aliwonse zimenezi. 11Zimene mfumu yafunsa ndi zapatali. Palibe wina amene angathe kuwulula izi kwa mfumu kupatula milungu, ndipo sikhala pakati pa anthu.”

12Zimenezi zinapsetsa mtima mfumu ndipo inakwiya kwambiri kotero inalamula kuti anzeru onse a ku Babuloni aphedwe. 13Choncho lamulo linaperekedwa kuti anthu anzeru aphedwe, ndipo anatuma anthu kukafunafuna Danieli ndi anzake kuti iwonso aphedwe.

14Danieli anayankhula mwanzeru ndi mwaulemu kwa Ariyoki, mkulu wa asilikali olondera mfumu amene anatumidwa kukapha anthu anzeru a ku Babuloni. 15Danieli anafunsa Ariyoki kapitawo wa mfumu kuti, “Chifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lankhanza lotere?” Kenaka Ariyoki anafotokoza nkhaniyi kwa Danieli. 16Danieli anapita mofulumira kwa mfumu ndipo anamupempha kuti amupatse nthawi kuti amuwuze zimene walota ndi tanthauzo lake.

17Kenaka Danieli anabwerera ku nyumba kwake ndi kukafotokozera anzake aja zimenezi: Hananiya, Misaeli ndi Azariya. 18Danieli anadandaulira anzake kuti apemphe kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo ndi kumuwululira chinsinsi, kuti iye ndi anzakewo asanyongedwe pamodzi ndi anzeru ena onse a ku Babuloni. 19Usiku Yehova anamuwululira Danieli chinsinsi chija mʼmasomphenya. Pamenepo Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba, 20ndipo anati:

“Litamandike dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi;

nzeru ndi mphamvu zonse ndi zake.

21Amasintha nthawi ndi nyengo;

amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso.

Amapatsa nzeru kwa anzeru

ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu.

22Amavumbulutsa zinthu zozama ndi zobisika;

amadziwa zimene zili mu mdima,

ndipo kuwunika kumakhala ndi Iye.

23Ndikuyamika ndi kutamanda Inu Mulungu wa makolo anga:

mwandipatsa nzeru ndi mphamvu,

mwandiwululira zomwe tinakupemphani,

mwatiwululira maloto a mfumu.”

Danieli Atanthauzira Maloto

24Motero Danieli anapita kwa Ariyoki, amene mfumu inamusankha kuti akaphe anthu anzeru a ku Babuloni, ndipo anati kwa iye, “Musaphe anthu anzeru a ku Babuloni. Ndiperekezeni kwa mfumu, ndipo ndidzayimasulira maloto ake.”

25Ariyoki anapita naye Danieli kwa mfumu nthawi yomweyo ndipo anati, “Ndapeza munthu pakati pa akapolo ochokera ku Yuda amene akhoza kuwuza mfumu zimene maloto ake akutanthauza.”

26Mfumu inafunsa Danieli (wotchedwanso Belitesezara) kuti, “Kodi ukhoza kundiwuza zomwe ine ndinaona mʼmaloto anga ndi tanthauzo lake?”

27Danieli anayankha kuti, “Palibe munthu wanzeru, wowombeza, wamatsenga kapena wamawula amene akhoza kufotokozera mfumu chinsinsi chimene mwafuna kudziwa, 28koma kuli Mulungu kumwamba amene amawulula zinsinsi. Iye waonetsera mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitika mʼmasiku akutsogolo. Maloto ndi masomphenya anu amene munawaona mukugona pa bedi lanu ndi awa:

29“Mukugona pa bedi, inu Mfumu, maganizo anakufikirani a zinthu zakutsogolo, ndipo Yehova wowulula zinsinsi anakuonetserani zimene zidzachitika. 30Koma chinsinsi ichi chavumbulutsidwa kwa ine, si chifukwa chakuti ndili ndi nzeru zochuluka kuposa anthu ena onse, koma kuti mfumu mudziwe tanthauzo la maloto anu ndi kuti muzindikire maganizo amene anali mu mtima mwanu.

31“Inu mfumu, munaona chinthu chowumba chachikulu chimene chinayima pamaso panu. Chowumbachi chinali chonyezimira mʼmaonekedwe. 32Mutu wa chowumbacho unali wagolide wabwino kwambiri. Chifuwa ndi manja ake zinali zasiliva. Mimba ndi ntchafu zake zinali zamkuwa. 33Miyendo yake inali yachitsulo, mapazi ake anali achitsulo chosakaniza ndi dongo. 34Inu mukuona, mwala unagamuka, koma osati ndi manja a munthu. Unagwera fanolo pa mapazi ake achitsulo chosakaniza ndi dongo aja ndi kuwaphwanya. 35Tsono chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide zonse zinaphwanyika pamodzi ndikukhala tizidutswa towuluka ndi mphepo ngati mungu wa mowombera tirigu nthawi ya chilimwe. Zonse zinawuluka ndi mphepo osasiyako chilichonse. Koma mwala umene unagwera pa chowumba chija unasanduka phiri lalikulu ndi kudzaza dziko lonse lapansi.

36“Maloto aja ndi amenewa; tidzafotokoza tanthauzo lake kwa mfumu. 37Inu mfumu, ndinu mfumu ya mafumu. Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu, ulamuliro ndi mphamvu ndi ulemerero; 38Iye anayika mʼmanja mwanu anthu ndi nyama zakuthengo ndi mbalame zamlengalenga. Kulikonse kumene zikhala, iye anakuyikani wolamulira wa zonse. Inu ndinu mutu wagolidewo.

39“Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi. 40Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse. 41Ndipo monga munaonera kuti mapazi ndi zala zake zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho uwu udzakhala ufumu wogawikana; komabe udzakhala ndi mphamvu zina zachitsulo zotikita. 42Monga zala zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho ufumu uwu udzakhala pangʼono wolimba ndi pangʼono wofowoka. 43Ndipo monga munaona chitsulo chosakanizidwa ndi dongo, choncho anthu adzakhala wosakanizana ndipo sadzagwirizana, monga muja chitsulo sichingasakanizike ndi dongo.

44“Pa nthawi ya mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa, kapenanso kuperekedwa kwa anthu ena. Udzawononga maufumu onse aja ndi kuwatheratu, koma iwo wokha udzakhalapobe mpaka muyaya. 45Limeneli ndilo tanthauzo la masomphenya a mwala umene unagamuka pa phiri, koma osati ndi manja a anthu; mwala umene unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide mʼtizidutswa.

“Mulungu wamkulu wakuonetsani mfumu chimene chidzachitika kutsogolo. Malotowo ndi woona ndipo tanthauzo lake ndi lodalirika.”

46Pamenepo mfumu Nebukadinezara inadzigwetsa chafufumimba pamaso pa Danieli ndi kumupatsa ulemu. Ndipo inalamula kuti anthu onse amuthirire Danieli nsembe ndi kumufukizira lubani. 47Mfumu inati kwa Danieli, “Zoonadi, Mulungu wako ndi Mulungu wa milungu ndi Ambuye wa mafumu ndi wowulula zinsinsi, pakuti iwe wathadi kuwulula chinsinsi ichi.”

48Ndipo mfumu inamukweza Danieli ndi kumupatsa mphatso zambiri. Anamuyika kuti akhale wolamulira chigawo chonse cha Babuloni ndi kutinso akhale woyangʼanira anthu ake onse anzeru. 49Komanso, monga mwa pempho la Danieli, mfumu inayika Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti akhale oyangʼanira chigawo cha Babuloni, pamene Danieliyo ankakhazikika mʼbwalo la mfumu.