Miyambo 14:15-24 CCL

Miyambo 14:15-24

Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse,

koma munthu wochenjera amaganizira bwino mayendedwe ake.

Munthu wanzeru amaopa Mulungu ndipo amapewa zoyipa,

koma munthu wopusa ndi wokula mtima amakhala wosasamala.

Munthu wopsa mtima msanga amachita zinthu za uchitsiru,

ndipo anthu amadana ndi munthu wachinyengo.

Anthu opusa amalandira uchitsiru,

koma anthu ochenjera amavekedwa chipewa cha ulemerero wa kudziwa zinthu.

Anthu oyipa adzagwada pamaso pa anthu abwino,

ndipo anthu oyipa adzapempha thandizo kwa anthu olungama.

Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda,

koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri.

Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa

koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa.

Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera?

Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika.

Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu,

koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi.

Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe,

koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru.

Read More of Miyambo 14