Miyambo 14 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 14:1-35

1Mkazi wanzeru amamanga banja lake,

koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.

2Amene amayenda molungama amaopa Yehova,

koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova.

3Kuyankhula kwa chitsiru kumamuyitanira ndodo pa msana,

koma milomo ya munthu wanzeru imamuteteza.

4Pakasowa ngʼombe zolima gome limakhala lopanda chakudya,

koma pakakhala ngʼombe zamphamvu zakudya zimachulukanso.

5Mboni yokhulupirika sinama,

koma mboni yonyenga imayankhula zabodza.

6Wonyoza anzake amafunafuna nzeru koma osayipeza,

koma munthu womvetsa bwino amadziwa zinthu msanga.

7Khala kutali ndi munthu wopusa

chifukwa sudzapeza mawu a nzeru.

8Nzeru za munthu wochenjera zagona pakuzindikira njira zake.

Koma uchitsiru wa zitsiru umapusitsidwa ndi chinyengo chawo chomwe.

9Zitsiru zimanyoza za kulapa machimo, awo,

koma kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.

10Mtima uliwonse umadziwa wokha zowawa zake,

ndipo palibe wina aliyense angadziwe kukondwa kwake.

11Nyumba ya munthu woyipa idzapasuka,

koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.

12Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu,

koma kumatsiriziro kwake ndi ku imfa.

13Ngakhale poseka mtima utha kumva kuwawa,

ndipo mathero achimwemwe akhoza kukhala chisoni.

14Munthu wosakhulupirika adzalandira zogwirizana ndi ntchito yake,

koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito yake.

15Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse,

koma munthu wochenjera amaganizira bwino mayendedwe ake.

16Munthu wanzeru amaopa Mulungu ndipo amapewa zoyipa,

koma munthu wopusa ndi wokula mtima amakhala wosasamala.

17Munthu wopsa mtima msanga amachita zinthu za uchitsiru,

ndipo anthu amadana ndi munthu wachinyengo.

18Anthu opusa amalandira uchitsiru,

koma anthu ochenjera amavekedwa chipewa cha ulemerero wa kudziwa zinthu.

19Anthu oyipa adzagwada pamaso pa anthu abwino,

ndipo anthu oyipa adzapempha thandizo kwa anthu olungama.

20Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda,

koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri.

21Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa

koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa.

22Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera?

Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika.

23Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu,

koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi.

24Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe,

koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru.

25Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo,

koma mboni yabodza imaphetsa.

26Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanira

ndipo iye adzakhala pothawira pa ana ake.

27Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo,

kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa.

28Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu,

koma popanda anthu kalonga amawonongeka.

29Munthu wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri,

koma munthu wopsa mtima msanga amaonetsa uchitsiru wake.

30Mtima wodekha umapatsa thupi moyo,

koma nsanje imawoletsa mafupa.

31Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake,

koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.

32Anthu oyipa adzakanthidwa chifukwa cha ntchito zawo zomwe,

koma olungama adzatetezedwa mwa imfa yawo.

33Nzeru zimakhala mu mtima mwa anthu omvetsa zinthu,

koma nzeru sipezeka mu mtima mwa zitsiru.

34Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,

koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.

35Mfumu imasangalatsidwa ndi wantchito wanzeru,

koma imachitira ukali wantchito wochititsa manyazi.