Ezekieli 30:1-26, Ezekieli 31:1-18 CCL

Ezekieli 30:1-26

Za Kulangidwa kwa Igupto

Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.

“ ‘Ufuwule mawu awa akuti,

‘Kalanga, tsiku lafika!’

Pakuti tsiku layandikira,

tsiku la Yehova lili pafupi,

tsiku la mitambo yakuda,

tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.

Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto

ndipo mavuto adzafika pa Kusi.

Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto,

chuma chake chidzatengedwa

ndipo maziko ake adzagumuka.

Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.

“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:

“ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa

ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu.

Adzaphedwa ndi lupanga

kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ”

ndikutero Ine Ambuye Yehova.

“ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja

kupambana mabwinja ena onse opasuka,

ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka

kupambana mizinda ina yonse.

Nditatha kutentha Igupto

ndi kupha onse omuthandiza,

pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

“ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.

“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni

kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.

Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja

adzabwera kudzawononga dzikolo.

Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto

ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.

Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo

ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa.

Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo

pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.

Ine Yehova ndayankhula.

“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndidzawononga mafano

ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi.

Simudzakhalanso mfumu mu Igupto,

ndipo ndidzaopseza dziko lonse.

Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,

ndi kutentha mzinda wa Zowani.

Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.

Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,

linga lolimba la Igupto,

ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.

Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;

Peluziumu adzazunzika ndi ululu.

Malinga a Thebesi adzagumuka,

ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.

Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti

adzaphedwa ndi lupanga

ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.

Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima

pamene ndidzathyola goli la Igupto;

motero kunyada kwake kudzatha.

Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,

ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.

Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,

ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Farao Watha Mphamvu

Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake. Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo. Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto. Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Read More of Ezekieli 30

Ezekieli 31:1-18

Mkungudza mu Lebanoni

Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti,

“ ‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?

Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,

wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango.

Unali wautali,

msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.

Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo,

akasupe ozama ankawutalikitsa.

Mitsinje yake inkayenda

mozungulira malo amene unaliwo

ndipo ngalande zake zinkafika

ku mitengo yonse ya mʼmunda.

Choncho unatalika kwambiri

kupambana mitengo yonse ya mʼmunda.

Nthambi zake zinachuluka

ndi kutalika kwambiri,

chifukwa inkalandira madzi ambiri.

Mbalame zonse zamlengalenga

zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo.

Nyama zakuthengo zonse

zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake.

Mitundu yotchuka ya anthu

inkakhala mu mthunzi wake.

Unali wokongola kwambiri,

wa nthambi zake zotambalala,

chifukwa mizu yake inazama pansi

kumene kunali madzi ochuluka.

Mʼmunda wa Mulungu munalibe

mkungudza wofanana nawo,

kapena mitengo ya payini

ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake.

Munalibenso mtengo wa mkuyu

nthambi zofanafana ndi zake.

Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse

wofanana ndi iwo kukongola kwake.

Ine ndinawupanga wokongola

wa nthambi zochuluka.

Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa

Mulungu inawuchitira nsanje.

“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake, ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake. Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya. Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake. Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.

“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.

“ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo.

“ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”

Read More of Ezekieli 31