Ezekieli 30 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ezekieli 30:1-26

Za Kulangidwa kwa Igupto

1Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.

“ ‘Ufuwule mawu awa akuti,

‘Kalanga, tsiku lafika!’

3Pakuti tsiku layandikira,

tsiku la Yehova lili pafupi,

tsiku la mitambo yakuda,

tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.

4Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto

ndipo mavuto adzafika pa Kusi.

Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto,

chuma chake chidzatengedwa

ndipo maziko ake adzagumuka.

5Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.

6“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:

“ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa

ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu.

Adzaphedwa ndi lupanga

kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ”

ndikutero Ine Ambuye Yehova.

7“ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja

kupambana mabwinja ena onse opasuka,

ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka

kupambana mizinda ina yonse.

8Nditatha kutentha Igupto

ndi kupha onse omuthandiza,

pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.

9“ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.

10“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni

kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.

11Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja

adzabwera kudzawononga dzikolo.

Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto

ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.

12Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo

ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa.

Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo

pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.

Ine Yehova ndayankhula.

13“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,

“ ‘Ndidzawononga mafano

ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi.

Simudzakhalanso mfumu mu Igupto,

ndipo ndidzaopseza dziko lonse.

14Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,

ndi kutentha mzinda wa Zowani.

Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.

15Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,

linga lolimba la Igupto,

ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.

16Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;

Peluziumu adzazunzika ndi ululu.

Malinga a Thebesi adzagumuka,

ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.

17Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti

adzaphedwa ndi lupanga

ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.

18Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima

pamene ndidzathyola goli la Igupto;

motero kunyada kwake kudzatha.

Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,

ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.

19Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,

ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”

Farao Watha Mphamvu

20Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: 21“Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. 22Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake. 23Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. 24Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo. 25Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto. 26Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”