Josué 12 – OL & CCL

O Livro

Josué 12:1-24

A lista dos reis derrotados

1Esta é a lista dos reis da margem oriental do rio Jordão, cujas cidades foram destruídas pelos israelitas; uma área que ia desde o vale do rio Arnom até ao monte Hermon, incluindo as cidades do deserto oriental.

2Um deles era o rei Siom dos amorreus, que vivia em Hesbom. O seu reino cobria o território que tinha por limite, dum lado Aroer, mesmo na extremidade do vale de Arnom, e a meio da depressão cavada pelo rio Arnom, e do outro lado o rio Jaboque até metade de Gileade, que servia de fronteira com os amonitas. 3Portanto, inclui desde a planície até ao mar da Galileia, do lado oriental, até ao mar da planície, o mar Salgado, estendendo-se em direção a Bete-Jesimote, a sul, até às encostas do monte Pisga.

4Outro era o rei Ogue de Basã, o último dos refaítas, que vivia em Astarote e Edrei. 5Era ele quem governava aquele território que se estendia do monte Hermon a norte, até Salca no monte Basã, a oriente; a ocidente ia até aos limites dos reinos de Gesur e Maacá. O seu reino cobria também uma área a sul, que incluía a metade norte de Gileade, onde a fronteira tocava os limites do reino de Siom rei de Hesbom. 6Moisés e o povo de Israel tinham destruído esses povos e a terra tinha sido dada à tribo de Rúben, à tribo de Gad e à meia tribo de Manassés.

7Foram ainda os seguintes reinos que Josué, comandando o exército de Israel, destruiu a ocidente do Jordão. (Essa terra que fica entre Baal-Gad no vale do Líbano e o monte Halaque, a ocidente do monte Seir, foi dada por Josué às outras tribos de Israel. 8Essa área incluía a zona das colinas, as planuras, o Arabá, as vertentes na montanha, o deserto da Judeia e o Negueve. Os povos que lá viviam eram os hititas, os amorreus, os cananeus, os perizeus, os heveus e os jebuseus.)

9Eram os reis das seguintes cidades:

Jericó,

Ai perto de Betel,

10Jerusalém,

Hebrom,

11Jarmute,

Laquis,

12Eglom,

Gezer,

13Debir,

Geder,

14Horma,

Arade,

15Libna,

Adulão,

16Maqueda,

Betel,

17Tapua,

Hefer,

18Afeque,

Lasarom,

19Madom,

Hazor,

20Simrom-Merom,

Acsafe,

21Taanaque,

Megido,

22Quedes,

Jocneão no Carmelo,

23Dor em Nafate-Dor,

Goiim em Gilgal,

24e Tirza.

Ao todo, trinta e um reis que foram aniquilados e as suas cidades destruídas.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yoswa 12:1-24

Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa

1Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:

2Sihoni mfumu ya Aamori,

amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. 3Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.

4Ogi mfumu ya mzinda wa Basani,

amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. 5Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.

6Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.

7Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. 8Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:

9mfumu ya Yeriko imodzimfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzi10mfumu ya Yerusalemu imodzimfumu ya Hebroni imodzi11mfumu ya Yarimuti imodzimfumu ya Lakisi imodzi12mfumu ya Egiloni imodzimfumu ya Gezeri imodzi13mfumu ya Debri imodzimfumu ya Gederi imodzi14mfumu ya Horima imodzimfumu ya Aradi imodzi15mfumu ya Libina imodzimfumu ya Adulamu imodzi16mfumu ya Makeda imodzimfumu ya Beteli imodzi17mfumu ya Tapuwa imodzimfumu ya Heferi imodzi18mfumu ya Afeki imodzimfumu ya Lasaroni imodzi19mfumu ya Madoni imodzimfumu ya Hazori imodzi20mfumu ya Simuroni Meroni imodzimfumu ya Akisafu imodzi21mfumu ya Taanaki imodzimfumu ya Megido imodzi22mfumu ya Kadesi imodzimfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzi23mfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzimfumu ya Goyini ku Giligala imodzi24mfumu ya Tiriza imodzimafumu onse pamodzi analipo 31.