Ефесцима 5 – NSP & CCL

New Serbian Translation

Ефесцима 5:1-33

1Угледајте се, дакле, на Бога, пошто сте његова вољена деца. 2Живите у љубави, као што је Христос заволео нас, па је себе предао за нас на жртву и миомирисни принос Богу.

3Блуд и свака врста нечистоте, или похлепа нека се и не помиње међу вама, као што доликује светима. 4Ни просташтво, лудорије, ни безобразне шале, нити што неприлично; радије захваљујте. 5Јер, будите уверени: ниједан блудник, нечист или похлепан, који је раван идолопоклонику, неће узети учешћа у Царству Христовом и Божијем.

Живот у светлости

6Не дајте да вас ико заведе испразним речима. Јер, због оваквих ствари, доћи ће гнев Божији на непокорне синове. 7Не будите њихови саучесници! 8Некада сте, наиме, били тама, али сте сада светлост у Господу. Живите, стога, као деца светлости. 9Ово је, наиме, плод светлости: све што је добро, праведно и истинито. 10Истражујте шта је угодно Господу. 11Не будите саучесници оних који чине јалова дела таме, него их разоткривајте. 12Јер, срамота је и говорити о ономе што они тајно чине. 13Али све што се изнесе на светло, постаје видљиво, 14јер све што се излаже светлости, постаје светлост. Зато каже:

„Дигни се, ти што спаваш,

устани из мртвих,

и Христос ће те обасјати!“

15Брижљиво пазите како се опходите. Не понашајте се као неразумни, него као мудри! 16Искористите време јер су дани зли. 17Зато не будите неразумни, него схватите шта је воља Господња. 18Не опијајте се вином, које води у разузданост, него се испуњавајте Духом. 19Говорите једни другима речима псалама, химни и духовних песама. Певајте и славите Господа у свом срцу. 20Увек захваљујте за све Богу и Оцу у име нашег Господа Исуса Христа.

Односи у браку и породици

21Покоравајте се једни другима у страху пред Христом. 22Жене, покоравајте се својим мужевима као Господу. 23Јер, муж је глава жени, као што је Христос глава Цркви, исти Христос који је Спаситељ свога тела – Цркве. 24Као што се Црква покорава Христу, тако и жена нека се покорава мужу у свему.

25Мужеви, волите своје жене, као што је Христос волео Цркву, те је дао свој живот за њу, 26да је посвети, очистивши је купањем у води с речју, 27те да изведе пред себе Цркву у пуној слави, без мане и боре, или томе сличног, да буде света и непорочна. 28Тако су и мужеви дужни да воле своје жене као своје сопствено тело. Муж који воли своју жену, воли самога себе. 29Јер, нико не мрзи своје тело, него га храни и негује, као и Христос Цркву. 30Ми смо, наиме, делови Христовог тела. 31Као што Писмо каже:

„Зато ће човек оставити оца и мајку,

те се приљубити уз своју жену, па ће двоје бити једно тело.“

32Ово је велика тајна. Ја вам то говорим о Христу и Цркви. 33Тако сваки од вас нека воли своју жену као самога себе, а жена нека поштује свога мужа.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Aefeso 5:1-33

1Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. 2Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu.

3Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. 4Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. 5Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. 6Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. 7Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.

8Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika 9(pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi). 10Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. 11Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. 12Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. 13Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala. 14Nʼchifukwa chake Malemba akuti,

“Dzuka, wamtulo iwe,

uka kwa akufa,

ndipo Khristu adzakuwalira.”

15Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. 16Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa. 17Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite. 18Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. 19Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. 20Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

Malangizo kwa Akazi ndi Amuna Mʼbanja

21Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu.

22Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye. 23Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake. 24Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse.

25Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo 26kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake. 27Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro. 28Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. 29Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake 30pakuti ndife ziwalo za thupi lake. 31“Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” 32Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo. 33Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake.