Hebrews 10 – NIV & CCL

New International Version

Hebrews 10:1-39

Christ’s Sacrifice Once for All

1The law is only a shadow of the good things that are coming—not the realities themselves. For this reason it can never, by the same sacrifices repeated endlessly year after year, make perfect those who draw near to worship. 2Otherwise, would they not have stopped being offered? For the worshipers would have been cleansed once for all, and would no longer have felt guilty for their sins. 3But those sacrifices are an annual reminder of sins. 4It is impossible for the blood of bulls and goats to take away sins.

5Therefore, when Christ came into the world, he said:

“Sacrifice and offering you did not desire,

but a body you prepared for me;

6with burnt offerings and sin offerings

you were not pleased.

7Then I said, ‘Here I am—it is written about me in the scroll—

I have come to do your will, my God.’ ”10:7 Psalm 40:6-8 (see Septuagint)

8First he said, “Sacrifices and offerings, burnt offerings and sin offerings you did not desire, nor were you pleased with them”—though they were offered in accordance with the law. 9Then he said, “Here I am, I have come to do your will.” He sets aside the first to establish the second. 10And by that will, we have been made holy through the sacrifice of the body of Jesus Christ once for all.

11Day after day every priest stands and performs his religious duties; again and again he offers the same sacrifices, which can never take away sins. 12But when this priest had offered for all time one sacrifice for sins, he sat down at the right hand of God, 13and since that time he waits for his enemies to be made his footstool. 14For by one sacrifice he has made perfect forever those who are being made holy.

15The Holy Spirit also testifies to us about this. First he says:

16“This is the covenant I will make with them

after that time, says the Lord.

I will put my laws in their hearts,

and I will write them on their minds.”10:16 Jer. 31:33

17Then he adds:

“Their sins and lawless acts

I will remember no more.”10:17 Jer. 31:34

18And where these have been forgiven, sacrifice for sin is no longer necessary.

A Call to Persevere in Faith

19Therefore, brothers and sisters, since we have confidence to enter the Most Holy Place by the blood of Jesus, 20by a new and living way opened for us through the curtain, that is, his body, 21and since we have a great priest over the house of God, 22let us draw near to God with a sincere heart and with the full assurance that faith brings, having our hearts sprinkled to cleanse us from a guilty conscience and having our bodies washed with pure water. 23Let us hold unswervingly to the hope we profess, for he who promised is faithful. 24And let us consider how we may spur one another on toward love and good deeds, 25not giving up meeting together, as some are in the habit of doing, but encouraging one another—and all the more as you see the Day approaching.

26If we deliberately keep on sinning after we have received the knowledge of the truth, no sacrifice for sins is left, 27but only a fearful expectation of judgment and of raging fire that will consume the enemies of God. 28Anyone who rejected the law of Moses died without mercy on the testimony of two or three witnesses. 29How much more severely do you think someone deserves to be punished who has trampled the Son of God underfoot, who has treated as an unholy thing the blood of the covenant that sanctified them, and who has insulted the Spirit of grace? 30For we know him who said, “It is mine to avenge; I will repay,”10:30 Deut. 32:35 and again, “The Lord will judge his people.”10:30 Deut. 32:36; Psalm 135:14 31It is a dreadful thing to fall into the hands of the living God.

32Remember those earlier days after you had received the light, when you endured in a great conflict full of suffering. 33Sometimes you were publicly exposed to insult and persecution; at other times you stood side by side with those who were so treated. 34You suffered along with those in prison and joyfully accepted the confiscation of your property, because you knew that you yourselves had better and lasting possessions. 35So do not throw away your confidence; it will be richly rewarded.

36You need to persevere so that when you have done the will of God, you will receive what he has promised. 37For,

“In just a little while,

he who is coming will come

and will not delay.”10:37 Isaiah 26:20; Hab. 2:3

38And,

“But my righteous10:38 Some manuscripts But the righteous one will live by faith.

And I take no pleasure

in the one who shrinks back.”10:38 Hab. 2:4 (see Septuagint)

39But we do not belong to those who shrink back and are destroyed, but to those who have faith and are saved.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ahebri 10:1-39

Yesu Nsembe ya Anthu Onse

1Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza. 2Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo. 3Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka. 4Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.

5Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati,

“Simunafune nsembe kapena zopereka,

koma thupi munandikonzera.

6Simunakondwere nazo nsembe zopsereza

ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo.

7Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine,

Inu Mulungu, ndabwera kudzachita zimene mukufuna monga zinalembedwa mʼMalemba.’ ”

8Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe. 9Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri. 10Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.

11Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo. 12Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu. 13Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. 14Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.

15Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,

16“Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo

atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.

“Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo,

ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”

17Ndipo akutinso:

“Sindidzakumbukiranso konse

machimo awo ndi zolakwa zawo.”

18Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.

Kulimbika Mtima ndi Kupirira pa Chikhulupiriro

19Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.

26Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. 27Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu 28Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu. 29Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo? 30Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.” 31Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.

32Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri. 33Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere. 34Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.

35Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu. 36Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza. 37Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe,

Iye amene akubwera adzabwera ndipo sadzachedwa ayi.

38Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.

Ndipo ngati iye abwerera mʼmbuyo chifukwa cha mantha,

Ine sindidzakondwera naye.

39Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.