Exodus 28 – NIV & CCL

New International Version

Exodus 28:1-43

The Priestly Garments

1“Have Aaron your brother brought to you from among the Israelites, along with his sons Nadab and Abihu, Eleazar and Ithamar, so they may serve me as priests. 2Make sacred garments for your brother Aaron to give him dignity and honor. 3Tell all the skilled workers to whom I have given wisdom in such matters that they are to make garments for Aaron, for his consecration, so he may serve me as priest. 4These are the garments they are to make: a breastpiece, an ephod, a robe, a woven tunic, a turban and a sash. They are to make these sacred garments for your brother Aaron and his sons, so they may serve me as priests. 5Have them use gold, and blue, purple and scarlet yarn, and fine linen.

The Ephod

6“Make the ephod of gold, and of blue, purple and scarlet yarn, and of finely twisted linen—the work of skilled hands. 7It is to have two shoulder pieces attached to two of its corners, so it can be fastened. 8Its skillfully woven waistband is to be like it—of one piece with the ephod and made with gold, and with blue, purple and scarlet yarn, and with finely twisted linen.

9“Take two onyx stones and engrave on them the names of the sons of Israel 10in the order of their birth—six names on one stone and the remaining six on the other. 11Engrave the names of the sons of Israel on the two stones the way a gem cutter engraves a seal. Then mount the stones in gold filigree settings 12and fasten them on the shoulder pieces of the ephod as memorial stones for the sons of Israel. Aaron is to bear the names on his shoulders as a memorial before the Lord. 13Make gold filigree settings 14and two braided chains of pure gold, like a rope, and attach the chains to the settings.

The Breastpiece

15“Fashion a breastpiece for making decisions—the work of skilled hands. Make it like the ephod: of gold, and of blue, purple and scarlet yarn, and of finely twisted linen. 16It is to be square—a span28:16 That is, about 9 inches or about 23 centimeters long and a span wide—and folded double. 17Then mount four rows of precious stones on it. The first row shall be carnelian, chrysolite and beryl; 18the second row shall be turquoise, lapis lazuli and emerald; 19the third row shall be jacinth, agate and amethyst; 20the fourth row shall be topaz, onyx and jasper.28:20 The precise identification of some of these precious stones is uncertain. Mount them in gold filigree settings. 21There are to be twelve stones, one for each of the names of the sons of Israel, each engraved like a seal with the name of one of the twelve tribes.

22“For the breastpiece make braided chains of pure gold, like a rope. 23Make two gold rings for it and fasten them to two corners of the breastpiece. 24Fasten the two gold chains to the rings at the corners of the breastpiece, 25and the other ends of the chains to the two settings, attaching them to the shoulder pieces of the ephod at the front. 26Make two gold rings and attach them to the other two corners of the breastpiece on the inside edge next to the ephod. 27Make two more gold rings and attach them to the bottom of the shoulder pieces on the front of the ephod, close to the seam just above the waistband of the ephod. 28The rings of the breastpiece are to be tied to the rings of the ephod with blue cord, connecting it to the waistband, so that the breastpiece will not swing out from the ephod.

29“Whenever Aaron enters the Holy Place, he will bear the names of the sons of Israel over his heart on the breastpiece of decision as a continuing memorial before the Lord. 30Also put the Urim and the Thummim in the breastpiece, so they may be over Aaron’s heart whenever he enters the presence of the Lord. Thus Aaron will always bear the means of making decisions for the Israelites over his heart before the Lord.

Other Priestly Garments

31“Make the robe of the ephod entirely of blue cloth, 32with an opening for the head in its center. There shall be a woven edge like a collar28:32 The meaning of the Hebrew for this word is uncertain. around this opening, so that it will not tear. 33Make pomegranates of blue, purple and scarlet yarn around the hem of the robe, with gold bells between them. 34The gold bells and the pomegranates are to alternate around the hem of the robe. 35Aaron must wear it when he ministers. The sound of the bells will be heard when he enters the Holy Place before the Lord and when he comes out, so that he will not die.

36“Make a plate of pure gold and engrave on it as on a seal: holy to the Lord. 37Fasten a blue cord to it to attach it to the turban; it is to be on the front of the turban. 38It will be on Aaron’s forehead, and he will bear the guilt involved in the sacred gifts the Israelites consecrate, whatever their gifts may be. It will be on Aaron’s forehead continually so that they will be acceptable to the Lord.

39“Weave the tunic of fine linen and make the turban of fine linen. The sash is to be the work of an embroiderer. 40Make tunics, sashes and caps for Aaron’s sons to give them dignity and honor. 41After you put these clothes on your brother Aaron and his sons, anoint and ordain them. Consecrate them so they may serve me as priests.

42“Make linen undergarments as a covering for the body, reaching from the waist to the thigh. 43Aaron and his sons must wear them whenever they enter the tent of meeting or approach the altar to minister in the Holy Place, so that they will not incur guilt and die.

“This is to be a lasting ordinance for Aaron and his descendants.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 28:1-43

Zovala za Ansembe

1“Aaroni mʼbale wako ndi ana ake aamuna, Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara uwapatule pakati pa Aisraeli. Abwere kwa iwe kuti anditumikire monga ansembe. 2Umusokere mʼbale wako, Aaroni, zovala zopatulika kuti azioneka mwaulemerero ndi molemekezeka. 3Uwawuze anthu onse aluso amene Ine ndawapatsa nzeru pa ntchito yosoka kuti apange zovala za Aaroni za pa mwambo womupatula, kuti iye anditumikire monga wansembe. 4Zovala zoti apange ndi izi: chovala chapachifuwa, efodi, mkanjo, mwinjiro wolukidwa, nduwira ndi lamba. Apangire mʼbale wako Aaroni ndi ana ake aamuna zovala zopatulikazi kuti iwo anditumikire monga ansembe. 5Iwo agwiritse ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira ndi yosalala yofewa.

Efodi

6“Apange efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yolukidwa mwaluso. 7Efodiyo ikhale ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. 8Lamba womangira efodi akhale wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Akhale wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala.

9“Utenge miyala iwiri ya onikisi ndipo uzokotepo mayina a ana a Israeli. 10Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo. 11Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide. 12Umangirire miyala iwiriyi pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli. Aaroni azinyamula mayinawo mʼmapewa ake kuti akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. 13Upange zoyikamo za maluwa agolide, 14ndiponso maunyolo awiri a golide wabwino kwambiri, wopetedwa ngati zingwe ndipo uwalumikize ku zoyikamozo.

Chovala Chapachifuwa

15“Upange chovala chapachifuwa chogwiritsa ntchito poweruza mlandu ndipo uchipange mwaluso kwambiri. Uchipange ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino. 16Kutalika kwake kukhale kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, ndipo chikhale chopinda pawiri. 17Uyikepo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rubi, topazi ndi berili. 18Mzere wachiwiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi; 19mzere wachitatu pakhale miyala ya opera, agate ndi ametisiti. 20Mzere wachinayi pakhale miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi uyiike mu zoyikamo zagolide. 21Miyalayo ikhalepo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse uzokotedwe ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli.

22“Upange timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe. 23Upangenso mphete ziwiri zagolide ndipo uzimangirire pa ngodya ziwiri za pa chovala chapachifuwa. 24Umangirire timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. 25Ndipo mbali ina ya timaunyoloto umangirire pa zoyikapo zake ziwiri zija ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. 26Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. 27Upangenso mphete zina ziwiri zagolide ndipo uzilumikize kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi. 28Tsono umangirire mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi.

29“Pamene Aaroni akulowa kumalo opatulika azivala chovala chapachifuwa cha zoweruzira chija chimene chalembedwa mayina a ana a Israeli kuti Yehova awakumbukire nthawi zonse. 30Ndiponso uyike Urimu ndi Tumimu mu chovala chapachifuwa cha zoweruziracho, kuti zikhale pamtima pa Aaroni. Choncho Aaroniyo adzakhala akutenga nthawi zonse zida zomuthandizira kuweruza ana a Israeli pamene adzafika pamaso pa Yehova.

Zovala Zina za Ansembe

31“Uyipangire efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo. 32Mkanjowo ukhala ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo pakhale chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike. 33Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, upange mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira zokhala ndi maberu agolide pakati pake. 34Choncho pazikhala mphonje imodzi kenaka belu limodzi, kuzungulira mpendero wa mkanjo wonse. 35Aaroni azivala mkanjowo pamene akutumikira ngati wansembe. Kulira kwa maberu kuzimveka pamene akulowa mʼmalo opatulika pamaso pa Yehova ndiponso pamene akutuluka, kuti asafe.

36“Upange duwa lagolide wabwino kwambiri kukhala ngati chidindo ndipo uzokotepo mawu akuti, choperekedwa kwa Yehova. 37Ulimange ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira ya Aaroni, ndipo duwalo likhale kutsogolo kwa nduwirayo. 38Lidzakhala pa mphumi ya Aaroni, motero iye adzasenza cholakwa chilichonse cha pa zopereka zilizonse zimene Aisraeli amazipatulira Yehova. Aaroni azivala chikwangwanichi pa mphumi pake nthawi zonse kuti Yehova alandire zopereka za anthu ake.

39“Uluke mwinjiro wa nsalu yofewa yosalala ndiponso upange nduwira ya nsalu yofewa yosalala. Lamba wake akhale wolukidwa bwino ndi munthu waluso. 40Upangirenso ana a Aaroni mwinjiro, malamba ndi nduwira kuti azioneka mwaulemu ndi molemekezeka. 41Zovala zimenezi umuveke Aaroni, mʼbale wako ndi ana ake. Kenaka uwadzoze, uwapatse udindo ndi kuwapatula kuti anditumikire ngati ansembe anga.

42“Uwapangire akabudula a nsalu yofewa oyambira mʼchiwuno kulekeza mʼntchafu kuti asamaonetse maliseche. 43Aaroni ndi ana ake ayenera kuvala akabudulawo pamene akulowa mu tenti ya msonkhano kapena pamene akupita ku guwa lansembe kukatumikira malo oyera kuopa kuti angachimwe ndi kufa.

“Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aaroni ndi zidzukulu zake.”