Exodus 20 – NIV & CCL

New International Version

Exodus 20:1-26

The Ten Commandments

1And God spoke all these words:

2“I am the Lord your God, who brought you out of Egypt, out of the land of slavery.

3“You shall have no other gods before20:3 Or besides me.

4“You shall not make for yourself an image in the form of anything in heaven above or on the earth beneath or in the waters below. 5You shall not bow down to them or worship them; for I, the Lord your God, am a jealous God, punishing the children for the sin of the parents to the third and fourth generation of those who hate me, 6but showing love to a thousand generations of those who love me and keep my commandments.

7“You shall not misuse the name of the Lord your God, for the Lord will not hold anyone guiltless who misuses his name.

8“Remember the Sabbath day by keeping it holy. 9Six days you shall labor and do all your work, 10but the seventh day is a sabbath to the Lord your God. On it you shall not do any work, neither you, nor your son or daughter, nor your male or female servant, nor your animals, nor any foreigner residing in your towns. 11For in six days the Lord made the heavens and the earth, the sea, and all that is in them, but he rested on the seventh day. Therefore the Lord blessed the Sabbath day and made it holy.

12“Honor your father and your mother, so that you may live long in the land the Lord your God is giving you.

13“You shall not murder.

14“You shall not commit adultery.

15“You shall not steal.

16“You shall not give false testimony against your neighbor.

17“You shall not covet your neighbor’s house. You shall not covet your neighbor’s wife, or his male or female servant, his ox or donkey, or anything that belongs to your neighbor.”

18When the people saw the thunder and lightning and heard the trumpet and saw the mountain in smoke, they trembled with fear. They stayed at a distance 19and said to Moses, “Speak to us yourself and we will listen. But do not have God speak to us or we will die.”

20Moses said to the people, “Do not be afraid. God has come to test you, so that the fear of God will be with you to keep you from sinning.”

21The people remained at a distance, while Moses approached the thick darkness where God was.

Idols and Altars

22Then the Lord said to Moses, “Tell the Israelites this: ‘You have seen for yourselves that I have spoken to you from heaven: 23Do not make any gods to be alongside me; do not make for yourselves gods of silver or gods of gold.

24“ ‘Make an altar of earth for me and sacrifice on it your burnt offerings and fellowship offerings, your sheep and goats and your cattle. Wherever I cause my name to be honored, I will come to you and bless you. 25If you make an altar of stones for me, do not build it with dressed stones, for you will defile it if you use a tool on it. 26And do not go up to my altar on steps, or your private parts may be exposed.’

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Eksodo 20:1-26

Malamulo Khumi

1Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati:

2“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.

3“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.”

4“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. 5Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane. 6Koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda, ndi kusunga malamulo anga.

7“Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.

8“Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. 9Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi. 10Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu. 11Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera.

12“Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

13“Usaphe.

14“Usachite chigololo.

15“Usabe.

16“Usapereke umboni womunamizira mnzako.

17“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

18Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali. 19Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.”

20Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.”

21Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu.

Za Mafano ndi Maguwa Ansembe

22Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: ‘Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba. 23Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ”

24Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani. 25Ngati mudzandimangira guwa lansembe lamiyala, musagwiritse ntchito miyala yosema, pakuti mudzalidetsa mukadzagwiritsa ntchito zida. 26Musamakwere pa makwerero popita pa guwa langa lansembe kuti mungaonetse maliseche anu.