2 Kings 4 – NIV & CCL

New International Version

2 Kings 4:1-44

The Widow’s Olive Oil

1The wife of a man from the company of the prophets cried out to Elisha, “Your servant my husband is dead, and you know that he revered the Lord. But now his creditor is coming to take my two boys as his slaves.”

2Elisha replied to her, “How can I help you? Tell me, what do you have in your house?”

“Your servant has nothing there at all,” she said, “except a small jar of olive oil.”

3Elisha said, “Go around and ask all your neighbors for empty jars. Don’t ask for just a few. 4Then go inside and shut the door behind you and your sons. Pour oil into all the jars, and as each is filled, put it to one side.”

5She left him and shut the door behind her and her sons. They brought the jars to her and she kept pouring. 6When all the jars were full, she said to her son, “Bring me another one.”

But he replied, “There is not a jar left.” Then the oil stopped flowing.

7She went and told the man of God, and he said, “Go, sell the oil and pay your debts. You and your sons can live on what is left.”

The Shunammite’s Son Restored to Life

8One day Elisha went to Shunem. And a well-to-do woman was there, who urged him to stay for a meal. So whenever he came by, he stopped there to eat. 9She said to her husband, “I know that this man who often comes our way is a holy man of God. 10Let’s make a small room on the roof and put in it a bed and a table, a chair and a lamp for him. Then he can stay there whenever he comes to us.”

11One day when Elisha came, he went up to his room and lay down there. 12He said to his servant Gehazi, “Call the Shunammite.” So he called her, and she stood before him. 13Elisha said to him, “Tell her, ‘You have gone to all this trouble for us. Now what can be done for you? Can we speak on your behalf to the king or the commander of the army?’ ”

She replied, “I have a home among my own people.”

14“What can be done for her?” Elisha asked.

Gehazi said, “She has no son, and her husband is old.”

15Then Elisha said, “Call her.” So he called her, and she stood in the doorway. 16“About this time next year,” Elisha said, “you will hold a son in your arms.”

“No, my lord!” she objected. “Please, man of God, don’t mislead your servant!”

17But the woman became pregnant, and the next year about that same time she gave birth to a son, just as Elisha had told her.

18The child grew, and one day he went out to his father, who was with the reapers. 19He said to his father, “My head! My head!”

His father told a servant, “Carry him to his mother.” 20After the servant had lifted him up and carried him to his mother, the boy sat on her lap until noon, and then he died. 21She went up and laid him on the bed of the man of God, then shut the door and went out.

22She called her husband and said, “Please send me one of the servants and a donkey so I can go to the man of God quickly and return.”

23“Why go to him today?” he asked. “It’s not the New Moon or the Sabbath.”

“That’s all right,” she said.

24She saddled the donkey and said to her servant, “Lead on; don’t slow down for me unless I tell you.” 25So she set out and came to the man of God at Mount Carmel.

When he saw her in the distance, the man of God said to his servant Gehazi, “Look! There’s the Shunammite! 26Run to meet her and ask her, ‘Are you all right? Is your husband all right? Is your child all right?’ ”

“Everything is all right,” she said.

27When she reached the man of God at the mountain, she took hold of his feet. Gehazi came over to push her away, but the man of God said, “Leave her alone! She is in bitter distress, but the Lord has hidden it from me and has not told me why.”

28“Did I ask you for a son, my lord?” she said. “Didn’t I tell you, ‘Don’t raise my hopes’?”

29Elisha said to Gehazi, “Tuck your cloak into your belt, take my staff in your hand and run. Don’t greet anyone you meet, and if anyone greets you, do not answer. Lay my staff on the boy’s face.”

30But the child’s mother said, “As surely as the Lord lives and as you live, I will not leave you.” So he got up and followed her.

31Gehazi went on ahead and laid the staff on the boy’s face, but there was no sound or response. So Gehazi went back to meet Elisha and told him, “The boy has not awakened.”

32When Elisha reached the house, there was the boy lying dead on his couch. 33He went in, shut the door on the two of them and prayed to the Lord. 34Then he got on the bed and lay on the boy, mouth to mouth, eyes to eyes, hands to hands. As he stretched himself out on him, the boy’s body grew warm. 35Elisha turned away and walked back and forth in the room and then got on the bed and stretched out on him once more. The boy sneezed seven times and opened his eyes.

36Elisha summoned Gehazi and said, “Call the Shunammite.” And he did. When she came, he said, “Take your son.” 37She came in, fell at his feet and bowed to the ground. Then she took her son and went out.

Death in the Pot

38Elisha returned to Gilgal and there was a famine in that region. While the company of the prophets was meeting with him, he said to his servant, “Put on the large pot and cook some stew for these prophets.”

39One of them went out into the fields to gather herbs and found a wild vine and picked as many of its gourds as his garment could hold. When he returned, he cut them up into the pot of stew, though no one knew what they were. 40The stew was poured out for the men, but as they began to eat it, they cried out, “Man of God, there is death in the pot!” And they could not eat it.

41Elisha said, “Get some flour.” He put it into the pot and said, “Serve it to the people to eat.” And there was nothing harmful in the pot.

Feeding of a Hundred

42A man came from Baal Shalishah, bringing the man of God twenty loaves of barley bread baked from the first ripe grain, along with some heads of new grain. “Give it to the people to eat,” Elisha said.

43“How can I set this before a hundred men?” his servant asked.

But Elisha answered, “Give it to the people to eat. For this is what the Lord says: ‘They will eat and have some left over.’ ” 44Then he set it before them, and they ate and had some left over, according to the word of the Lord.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 4:1-44

Mafuta a Mkazi Wamasiye

1Mkazi wa mmodzi mwa ana a aneneri anafuwula kwa Elisa kuti, “Mtumiki wanu, mwamuna wanga wamwalira ndipo inu mukudziwa kuti ankaopa Yehova. Koma tsopano munthu amene mwamuna wanga anakongolako zinthu zake, akubwera kudzatenga ana anga awiri aamuna kuti akhale akapolo ake.”

2Elisa anayankha mayiyo kuti, “Kodi ufuna ndikuchitire chiyani? Tandiwuza uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?”

Mayiyo anayankha kuti, “Mdzakazi wanu alibe kanthu kalikonse koma timafuta pangʼono chabe.”

3Elisa anati, “Pita kabwereke mitsuko yonse yopanda kanthu kwa anzako. Usakabwereke mitsuko yochepa. 4Kenaka ukalowe mʼnyumba mwako ndi kudzitsekera iwe ndi ana ako. Mukakatero mukakhuthulire mafuta mʼmitsuko yonseyo, ndipo mtsuko uliwonse ukadzaza muzikawuyika pambali.”

5Mayi uja anachoka kwa Elisa nakadzitsekera ndi ana ake. Anthu anabweretsa mitsuko kwa iye ndipo ankathiramo mafuta. 6Mitsuko yonse itadzaza, mayiyo anawuza mwana wake kuti, “Bweretsa mtsuko wina.”

Koma iye anayankha kuti, “Mitsuko yonse yatha.” Pamenepo mafuta analeka kutuluka.

7Mayiyo anapita nakamuwuza munthu wa Mulungu amene anamuyankha kuti, “Pita, kagulitse mafutawo ndipo ukabweze ngongole ija. Ndalama zotsalazo zikakhale zako ndi ana ako.”

Elisa Aukitsa Mwana wa Mayi wa ku Sunemu

8Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu. Kumeneko kunkakhala mayi wina wachuma amene anawumiriza Elisa kuti adye chakudya. Choncho nthawi iliyonse imene Elisa amadutsa kumeneko, ankayima ndi kudya. 9Mayiyo anawuza mwamuna wake kuti, “Taonani, ine ndikudziwa kuti munthu amene amadutsa pano nthawi zambiriyu ndi munthu woyera wa Mulungu. 10Tiyeni timumangire kachipinda kakangʼono pa denga la nyumbayi ndi kumuyikiramo bedi ndi tebulo, mpando ndi nyale. Akabwera kuno azikhala mʼmenemo.”

11Tsiku lina pamene Elisa anafika ku Sunemu, iye anakalowa mʼchipinda chake chija nagona mʼmenemo. 12Iye anati kwa mtumiki wake Gehazi, “Muyitane Msunemuyu.” Ndipo anapita kukamuyitana mayiyo, ndipo anabwera nayima pamaso pa Elisa. 13Elisa anati kwa Gehazi, “Muwuze mayiyo kuti, ‘Wavutika potichitira zonsezi. Nanga tsopano ifeyo tikuchitire chiyani? Kodi ukufuna kuti tikadziwitse mfumu kapena mtsogoleri wa ankhondo zimene watichitirazi?’ ”

Mayiyo anayankha kuti, “Ine ndimakhala mwamtendere pakati pa abale anga.”

14Elisa anafunsanso Gehazi kuti, “Kodi tingamuchitire chiyani?”

Gehazi anati, “Ndithu, mayiyu alibe mwana ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.”

15Pamenepo Elisa anati, “Muyitane.” Choncho Gehazi anamuyitana, ndipo iye anabwera nayima pa khomo. 16Elisa anati kwa mayiyo, “Nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, udzakhala utanyamula mwana wamwamuna mʼmanja mwako.”

Mayiyo anatsutsa zimenezi nanena kuti, “Ayi mbuye wanga. Inu munthu wa Mulungu, musanamize mdzakazi wanu!”

17Koma mayi uja anakhala woyembekezera, ndipo chaka chotsatiracho, nthawi ngati yomweyo anabereka mwana wamwamuna monga momwe Elisa anamuwuzira.

18Mwana uja anakula, ndipo tsiku lina anapita kwa abambo ake amene anali ndi anthu odula tirigu. 19Mwanayo anafuwula kwa abambo ake kuti, “Mayo! Mutu wanga ine! Mayo! Mutu wanga ine!”

Abambo akewo anawuza wantchito wake kuti, “Munyamule ndi kukamupereka kwa amayi ake.” 20Wantchito uja atamunyamula ndi kumupereka kwa amayi ake. Mwanayo anakhala pa miyendo ya amayi akeyo mpaka masana, ndipo pambuyo pake anamwalira. 21Mayiyo ananyamula mwanayo nakamugoneka pa bedi la munthu wa Mulungu uja. Kenaka anatseka chitseko iye nʼkuchokapo.

22Iye anayitanitsa mwamuna wake namuwuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi kuti ndipite mofulumira kwa munthu wa Mulungu nʼkubwererako.”

23Mwamuna wakeyo anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukupita kwa iyeyo lero? Lero si tsiku la Chikondwerero cha Mwezi Watsopano kapena tsiku la Sabata.”

Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”

24Mayiyo anamangirira chishalo pa bulu ndipo anawuza wantchito wake kuti, “Yendetsa bulu mofulumira. Usachepetse liwiro pokhapokha nditakuwuza.” 25Choncho ananyamuka nakafika kwa munthu wa Mulungu uja ku Phiri la Karimeli.

Munthu wa Mulungu ataona mayiyo patali, anawuza mtumiki wake Gehazi kuti, “Taona! Msunemu uyo! 26Thamanga msanga ukakumane naye ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi muli bwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Kodi mwana wanu ali bwino?’ ”

Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”

27Atafika kwa munthu wa Mulunguyo pa phiripo, mayiyo anagwira mapazi a Elisa. Gehazi anabwera kuti amukankhe, koma munthu wa Mulungu anati, “Musiye! Iyeyu ali pa mavuto aakulu, koma Yehova wandibisira zimenezi ndipo sanandiwuze chifukwa chake.”

28Tsono mayiyo anati, “Mbuye wanga, kodi ine ndinakupemphani mwana? Kodi sindinakuwuzeni kuti musandinamize?”

29Elisa anawuza Gehazi kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga ndodo yanga mʼdzanja lako ndipo thamanga. Ngati ukumana ndi munthu wina aliyense, usamupatse moni, ndipo ngati wina akupatsa moni, usayankhe. Ukagoneke ndodo yanga pa nkhope ya mwanayo.”

30Koma mayi wake wa mwana uja anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Choncho Elisa ananyamuka natsatira mayiyo.

31Gehazi anatsogola nakagoneka ndodoyo pa nkhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena kugwedezeka kuonetsa kuti ali moyo. Choncho Gehazi anabwerera kukakumana ndi Elisa ndipo anamuwuza kuti, “Mwanayo sanatsitsimuke.”

32Ndipo Elisa atafika ku nyumbako, taonani, mwanayo anali wakufa atamugoneka pa bedi lake. 33Elisa analowa mʼnyumbamo natseka chitseko. Anali awiri okha mʼchipindamo ndipo iye anapemphera kwa Yehova. 34Kenaka anakwera pa bedi ndi kumugonera mwanayo, pakamwa pake panakhudzana ndi pakamwa pa mwanayo, maso ake anakhudzana ndi maso a mwanayo, ndipo manja ake anakhudzana ndi manja a mwanayo. Pamene ankadzitambalitsa yekha pa mwanayo, thupi la mwanayo linayamba kufunda. 35Elisa anatembenuka nayenda uku ndi uku kamodzi mʼchipindamo ndipo kenaka anakweranso pa bedi nagoneranso mwanayo. Mwanayo anayetsemula kasanu ndi kawiri ndipo anatsekula maso ake.

36Elisa anayitana Gehazi ndipo anati, “Muyitane Msunemuyo.” Ndipo anaterodi. Mayiyo atabwera, Elisa anati, “Tenga mwana wako.” 37Mayiyo analowa, nagwada pa mapazi a Elisa, naweramitsa mutu wake pansi. Kenaka ananyamula mwana wake natuluka.

Imfa mu Mʼphika

38Elisa anabwerera ku Giligala ndipo ku dera limenelo kunali njala. Elisa akukumana ndi ana a aneneri, anati kwa mtumiki wake, “Ika mʼphika waukulu pa moto ndipo uwaphikire chakudya anthu awa.”

39Mmodzi mwa ana aneneriwo anapita kuthengo kukafuna ndiwo ndipo anakapeza mpesa wakuthengo. Iye anathyolako zipatso zake nadzaza nsalu yake. Atabwerera, anazidula zipatsozo naziyika mu mʼphika, ngakhale kuti panalibe amene ankazidziwa. 40Anawapakulira anthu chakudyacho, koma atayamba kudya, anthuwo anafuwula kuti, “Inu munthu wa Mulungu muli imfa mu mʼphikamu!” Ndipo sakanatha kudya chakudyacho.

41Elisa anati, “Bweretsani ufa.” Iye anathira ufa mu mʼphikamo ndipo anati, “Perekani chakudyachi kwa anthu kuti adye.” Ndipo mu mʼphikamo munalibenso zoopsa.

Kudyetsa Anthu 100

42Munthu wina wochokera ku Baala-Salisa anabwera atamutengera munthu wa Mulungu malofu a barele makumi awiri opangidwa kuchokera ku zokolola zoyamba kucha, pamodzinso ndi ngala zatsopano za tirigu. Elisa anati kwa munthuyo, “Apatse anthu kuti adye.”

43Mtumiki wake anafunsa kuti, “Kodi ndikachigawe motani chakudyachi kwa anthu 100?”

Koma Elisa anamuwuzanso kuti, “Apatse anthu adye. Pakuti izi ndi zimene Yehova akunena kuti, ‘Iwo adzadya chakudyachi ndipo china chidzatsalako.’ ” 44Tsono iye anachipereka kwa anthuwo ndipo anadya china nʼkutsalako, molingana ndi mawu a Yehova.